Luka 24
24
Kuhyuka kwa Yesu
Matayo 28:1-10; Maluko 16:1-8; Yohana 20:1-10
1Siku loyamba la jhuma umawamawa, achamayi wajha adatenga mafuta yajha yonunghila adakonjekela ni kupitanavo pa chiliza. 2Yapo adafika kumanda, adakomana mwala ujha waukulu lagunghulichidwa kutali ni pakhomo chiliza. 3Nambho yapo adalowa mkati mwa chiliza, sadalipheze chitanda la Ambuye Yesu. 4Yapo amadabwa nghani zijha, wandhu awili yawo adavala njhalu zong'azikila ngati umeme wa mbhambe, adaima mwachizulumukila pakati pao. 5Achazimayi wajha adaopa kupunda ni adakwatama maso yao mbaka panjhi. Wandhu awili wajha adakamba, “Chifuko chiyani mumfunafuna mundhu wamoyo pakati pa wandhu akufa? 6Iye palibepo pano, wahyuka. Mkumbukile umo wadakambila yapo wadali pamojhi ni anyiimwe kujha ku Galilaya, 7yapo wadakamba, ‘Ine mwana wa Mundhu nifunika kuikidwa mmanja mwa wandhu amachimo, sinipachikidwe ni siku lakatatu sinihyuke.’ ”
8Ndiipo wachikazi wajha adayakumbukila mawu yayo Yesu wadakambila, 9yapo adabwelela kuchokela kuchiliza ni kwaakambila atumwi wake khumi ni mmojhi wajha, pamojhi ni wina wonjhe, nghani zonjhe zidachokela. 10Wandhu yawo amafotokoza nghani kwa atumwi wajha, adali Maliya waku Magidalena, Yoana ni Maliya amake a Yakobo, pamojhi ni wachikazi wina yawo adali pamojhi naanyiiwo. 11Nambho atumwi wajha sadaakhulupililo wajha waachikazi ni nghani izo amazikamba, ndande adaziona zilibe mate yaliyonjhe. 12Ata chimwecho, Petulo wadanyamuka ni kuthamangila kujha ku chiliza, yapo wadafika wadakwatama ni kuzuzumila mchiliza mujha, wadangoona sandape zakhalila pajha. Wadabwelela kukhomo uku niwadabwa kuusu nghani izi zidachokela.
Yesu watulukila awili mnjila ya Emau
Maluko 16:12-13
13Siku limwelo aochatila wake awili adali paulendo wopita ku muchijhijhi chimojhi icho chimatanidwa Emau. Utali wake ni wokwana kilometa kumi ni imojhi kuchokela ku Yelusalemu. 14Anyiiwo amakambilila vindhu ivo vachokela. 15Yapo adali akali niakamba ni kukambilana kuusu ngani zimenezo, Yesu mwenewake wadatulukila ni kuyenda pamojhi na anyiiwo. 16Adamuona ni maso yawo, nambho adachekelezedwa kuti siadakhoza kumjhiwa.
17Yesu wadaafunjha, “Bwanji, nghani zanji izo mkambilana uku ni muyenda?” Wandhu wajha adaima uku ali chete, nghope zao nizilangiza chisoni. 18Mmojhi wao uyo wamatanidwa Kileopa wadamfunjha, “Bwanji, iwe ni mlendo kuno ku Yelusalemu mbaka usadajhiwa vindhu ivo vachokela pamasiku yochepaya?” 19Yesu wadafunjha, “Vindhu vanji ivo vachokela?” Adamuyangha, “Nghani za Yesu waku Nazaleti. Iye wadali mlosi, wa mbhavu pa ivo wamavichita ni pakukamba kwake, pachogolo pa Mnungu ni pachogolo pa wandhu wonjhe. 20Ajhukulu wa akuluakulu ni achogoleli awandhu adamchocha kuti walamulidwe nyifa, ni anyiiwo adampachika pamtanda. 21Nambho ife timakhulupilila kuti iye nde uyo wadatumidwa kwaombola wandhu a Izilaeli. Kupitilila yameneyo, lelo ni siku la katatu kuyambila vachitika vimenevi. 22Ni wachikazi wina pagulu lathu atizizwicha. Adapita pachiliza lelo umawamawa, 23nambho sadachikomane chitanda cha Yesu. Adabwelela ni kukamba kuti atulukilidwa ni atumiki akumwamba Amnungu, yawo adakambila kuti Yesu wakali wamoyo. 24Wandhu wina yawo adali pamojhi ni ife, adapita pachiliza kukaona yayo adakambilidwa ni wachikazi wajha, nambho sadamkomane Yesu.”
25Ndiipo Yesu wadakambila, “Wandhu anyiimwe ni asabobwa kupunda. Niwolimba kukhulupilila icho chidalamebdwa ni alosi? 26Bwanji, siidafunike Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu wavutike ni walowe mu ulemelelo wake?” 27Yesu wadafotokozela umo malembo yonjhe umo yakambila kuusu iye, kuyambila malembo ya Musa mbaka malembo ya alosi wina wonjhe.
28Yapo adawandikila pa mujhi uwo amapita, Yesu wadajhichita ngati wayendekela ni ulendo. 29Nambho anyiiwo adampembelela Yesu, niakamba, “Ukhale ni ife pakuti chipano ni ujhulo ni usiku wathowandikila.” Ndiipo wadolowa mnyumba ni kukhala nawo. 30Yapo wadakhala kudya chakudya pamojhi ni anyiiwo, iye wadatenga bumunda ni kwayamika Amnungu, wadaubandhula nikwaapacha. 31Ndhawi imweyo maso yawo yadamasuka, adamjhiwa kuti ni Yesu, ni iye wadasowa pakati pawo. 32Ndiipo adafunjhana, “Bwanji, mitima yathu siimakwelele kwa kukondwela yapo wamakamba niife ni kutifotokozela malembo mnjila mujha?” 33Ndhawi imweyo adachoka ni kubwela ku Yelusalemu. Kumeneko adakomana anyiwajha atumwi khumi ni mmojhi ni wandhu anyiyawo adali pamojhi ni anyiiwo, 34adakamba, “Zenedi, Ambuye ahyuka ni wamtulukila Simoni.” 35Ndiipo, wajha awili wadafotokozela achanjawo yayo yadachokela kunjila ni umo adamjhiwila Yesu, yapo wadabandhula bumunda.
Yesu waatulukila woyaluzidwa wake
Matayo 28:16-20; Maluko 16:14-18; Yohana 20:19-23; Vichito 1:6-8
36Yapo amakamba yameneyo, Yesu mwenewake wadaimilila pakati pao ni kukamba, “Mtendele ukhale kwanu!” 37Adajhujhumuka ni kuopa poganiza kuti chidali chimzilimu. 38Nambho iye wadaafunjha, “Ndande yanji muopa ni kukhaikila mmitima yanu? 39Yapenyeni manja yanga ni miyendo yanga, nii nde mwenewake. Pambasani manja yanga, chifuko chimzilimu chilibe thupi ni vifupa ivo nilinavo ine.”
40Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, wadaalangiza manja ni miyendo yake. 41Yapo adali akali sadakhulupilila kuti nde iye ndande ya chikondwelo ni kuzizwa, iye wadaafunjha, “Muli ni chindhu chalichonjhe cha chakudya?” 42Adampacha chibandhu cha njhomba yowamba. 43Iye wadalandila ni kudya pamaso pawo. 44Ndiipo wadakambila, “Izi nde nghani izo nidakukambilani nyengo iyo nidali pamojhi na anyiimwe kuti, yonjhe yayo yadalembedwa mu muthauko wa Musa, vikalakala va alosi ni chikalakala cha Zabuli kuusu ine, yadafunika yakwanilichidwe.”
45Ndiipo wadaachakula njelu zao kuti akhoze kuyajhiwa Malembo Yoela. 46Wadakambila, “Yadalembedwa yaya mu malembo Yoyela kuti, Kilisito Muomboli siwavutike ni kumwalila, siku la katatu siwahyuke, 47nikuti wandhu amayiko yonjhe kuyambila Yelusalemu, alalikidwe kwa jhina la Yesu kuti alape, ni kulekeleledwa machimo. 48Anyiimwe simukhale amboni avindhu ivi. 49Ine sinikutumileni uyo ahidi Atate wanga, nambho muyendekele kulindilila muno mu Yelusalemu mbaka yapo simulandile mbhavu kuchokela kumwamba.”
Yesu watengedwa kupita kumwamba
Maluko 16:19-20; Vichito 1:9-11
50Ndiipo, Yesu wadaachogoza woyaluzidwa wake kupita mbaka mbhepete mwa mujhi wa Besaniya, pamenepo wadakweza manja yake ni kwapacha mwawi. 51Yesu yapo wamapacha mwawi, wadatengedwa kumwamba ni kwasiya ni kupita kumwamba. 52Ndiipo adamulambila iye, adabwelela ku Yelusalemu, uku ajhala ni chikondwelo chachikulu, 53ni adayendekela kukhala mu mnyumba ya Mnungu masiku yonjhe namtamanda Mnungu.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Luka 24: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.