Luka 20

20
Mafunjho kuusu ulamuli wa Yesu
Matayo 21:23-27; Maluko 11:27-33
1Siku limojhi Yesu yapo wamayaluza wandhu Mnyumba ya Mnungu ni kwalalikila wandhu nghani za uthenga wabwino, achogoleli, oyaluza amathauko la Musa ni azee adajha kwaiye, 2adamfunjha, “Utikambile, uchita chimwechi kwa ulamuli wa yani? Yani uyo wakupacha ulamuli uwu?”
3Yesu wadaayangha, “Nanenjho nikufunjheni funjho, mnikambile, 4ulamuli wo batiza wa Yohana udachokela kwa Mnungu kapina kwa mundhu?”
5Adakambilana chimwechi, “Ngati tikakamba kuti udachokela kumwamba kwa Mnungu, iye siwatifunjhe, ‘Ndande yanji simudamkhulupilile iye?’ 6Ni tikanena, ‘Udachokela kwa wandhu,’ wandhu wonjhe satiphe potiponya miyala, chifuko wandhu wonjhewa akhulupilila kuti Yohana wadali mlosi.” 7Basi, adamuyangha, “Sitijhiwa ulamuli umeneo udachokela kuti.”
8Yesu wadakambila, “Nanenjho sinikukambilani nichita chimwechi kwa ulamuli wanji.”
Chifani cha obwelekecha munda kwa malipilo
Matayo 21:33-46; Maluko 12:1-12
9Yesu wadayendekela kwakambila wandhu kwa chifani ichi, “Padali mundhu mmojhi wadavyala munda wa zabibu, wadabwelekecha alimi kwa malipilo, nayo wadapita kukhala kutali kwa masiku yambili. 10Ndhawi yokolola yapo idafika, mundhu yujha wadamtuma mbowa wake kupita kwa mundhu yujha wadambweleka munda, kuti wakatenge gawo la vokolola. Nambho alimi wajha adambula mbowa yujha ni kumbweza manja yachaje. 11Mwene munda yujha wadamtuma mbowa mwina, nambho nayonjho adambula, nikumchitila vanjhoni ni kumbweza manja yachajhe. 12Wadamtumanjho mbowa wakatatu, nayonjho adampweteka ni kumtaya kubwalo kwa munda. 13Mwene munda yujha wadaganizila niwakamba, ‘Ifunika nichite bwanji? Sinimtume mwana wanga wayokha uyo nimkonda, kapina iyeyu samlemekeze.’ 14Nambho anyiwajha adabwelekechedwa yapo adamuona adakambilana, ‘Uyu nde olanja wake, tiyeni timphe kuti ulisiwo ukhale wathu.’ 15Chimwecho, adamuchocha kubwalo kwa munda wa zabibu ujha, ni kumupha.
“Bwanji, mwene munda yujha siwachite chiyani anyiwajha adabwelekechedwa munda? 16Iye siwajhe ni kwaapha anyiwajha adabwelekechedwa munda, ni kwapacha wina munda wa zabibu ujha.”
Wandhu ameneo yapo adavela chimwecho, adakamba, “Notho! Mnungu wavikanghile kutali kuti vindhu vimenevo visadachokela ata pang'ono!”
17Nambho Yesu wadapenyechecha ni kwafunjha, “Bwanji, malembo ya Mnungu yali ni mate yanji yayo yakamba,
‘Mwala uwo wakanidwa ni wandhu womanga,
chipano wakhala mwala wokhulupilika pomangila nyumba.’
18Mundhu waliyonjhe uyo wakugwa pa mwala umenewo, siwatyoke vipinjilivipinjili, ni waliyonjhe uyo silimgwele, silimpele ni kukhala ufa.”
Funjho kuusu kupeleka malipilo
Matayo 22:15-22; Maluko 12:13-17
19Oyaluza athauko ni ajhukulu wakulu, adafunafuna njila yomgwila Yesu siku limenelo, ndande adajhiwa kuti chifani chijha chimausu anyiiwo, nambho amaopa wandhu. 20Chimwecho, waadatuma wandhu kuti amchatilile Yesu, yao adajhichita kuti okhulupilika. Adachita chimwecho kuti amkodweleche Yesu kwa mawu yake, ni ampeleke kwa achogoleli ajhiko la ku Loma. 21Chimwecho apelelezi wajha adamfunjha Yesu, “Oyaluza, ife tijhiwa kuti munena ni kuyaluza bwino, ni simkondela mundhu, nambho muyaluza ngati umo watitumila Mnungu. 22Tikambileni, bwanji, thauko la Musa litilola kulipila malipilo kwa mfumu wa mkulu wa Aloma?”
23Nambho Yesu wadajhiwa msambha wawo, wadaakambila, 24“Nilangizeni gelenjha. Bwanji, chitunjhi ichi ni malembo yali pamwamba ni yayani?”
25Anyiiwo adamuyangha, “Ni ya Kaisali, mfumu wamkulu wa Aloma.” Ndiipo Yesu wadaakambila, “Mpacheni Kaisali mfumu wamkulu wa Aloma icho chili cha mfumu wa Aloma, ni mpacheni Mnungu icho chili cha Mnungu.” 26Adalepela kumkodwecha pamayangho yayo wadayangha pamaso pa wandhu. Nambho adazizwa kupunda pa mayangho yayo Yesu wadayangha, adakhala chete.
Mafunjho kuusu kuhyuka
Matayo 22:23-33; Maluko 12:18-27
27Masadukayo wina yao akamba kuti palibe kuhyuka, adafika kwa Yesu ni kumfunjha, 28“Oyaluza, Musa wadatilembela kuti, ngati mbale mmojhi wamwalila ni kusiya mkazake popande wana, basi mbalewakeyo wamkwate wamkaziyo, kuti wambalile mbale wake wana. 29Ndiipo, kudali achabale saba mnyumba imojhi. Woyamba yujha wadakwata ni kufa popande kusiya mwana. 30Ni wakawili wadamkwata wamkazi yujha, nayonjho wadafa popande kusiya wana, 31ni wakatatu nayonjho chimwecho, wadamkwata wamkazi mmeneyo. Chimwecho, wonjhe saba adamkwata wamkazi mmojhi ni adafa popande kusiya mwana. 32Pothela, wamkazi yujha wadafa. 33Chipano, siku la chihyukicho, wamkazi mmeneyo siwakhale wayani? Pakuti achabale wonjhe saba adamkwata wamkaziyo.”
34Yesu wadaayangha, “Wandhu amasiku yano pajhiko lapanjhi akwata ni kukwatiwa, 35nambho wandhu yawo Mnungu siwaone kuti afunika kuhyukichidwa ni kukhala moyo panyengo izo zikujha, saakwata kapina kukwatiwa. 36Anyiiwo siafanjho pakuti siakhale ngati atumiki wa kumwamba Amnungu. Anyiiwo ni wana Amnungu, pakuti waapacha kukhalanjho amoyo. 37Nambho ata malembo ya Musa yachimikiza kuti wandhu yawo amwalila sahyuke. Ni mmalembo yake yayo yadalembedwa kuusu fukutu ilo limawaka moto, iye wadaatana Ambuye, ‘Mnungu wa Ibulahimu, Mnungu wa Isaka ni Mnungu wa Yakobo.’ 38Iye osati Mnungu wa wandhu akufa, nambho iye ni Mnungu wa wandhu amoyo, pakuti wonjhe yawo akhala kwaiye ali ni umoyo.”
39Oyaluza akumojhi athauko, adakamba, “Oyaluza, mwayangha bwino!” 40Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, anyiiwo saadayese kumfunjha mafunjho yanjakenjho.
Kilisito ni mwana wa yani
Matayo 22:41-46; Maluko 12:35-37
41Yesu wadaafunjha, “Ikhala bwanji wandhu ajhikamba Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu ni mwana wa Daudi? 42Ndande, Daudi mwenewake mchikalakala cha Zabuli wadakamba,
‘Ambuye adamkambila Mbuye wanga,
Khala bendeka langa la ukulu ni ulamulilo
43mbaka yapo sinaike adani wako yapo saakhale mpando wopondela miyendo yako.’
44Chipano, ngati Daudi wadamtana Iye, ‘Ambuye,’ ikhala bwanji Kilisito wakhalenjho mwana wa Daudi?”
Kukhala maso ni oyaluza athauko
Matayo 23:1-36; Maluko 12:38-40
45Wandhu wonjhe yapo amamvechela, Yesu wadakambila oyaluzidwa wake, 46“Mkhale maso ni woyaluza amathauko. Anyiiwo akonda kuyendayenda uku avalila makhanzu yayatali. Yawo akonda kulonjeledwa mmalo yayo akomana wandhu ambili, ni anyiyawo akonda kukhala mmipando ya pachogolo mnyumba za mapembhelo, ni kukonda kukhala mipando ya ulemu mmaphwando. 47Yawo atenga chuma cha wachikazi yawo afedwa ni achamunawo ni kupembhela mapembhelo yayatali, kuti awonekane kuti ni abwino pamaso pa wandhu. Wandu ngati achamenecho, salamulidwe kupunda.”

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Luka 20: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល