Luka 19
19
Yesu ni Zakayo
1Yesu wadapita kumujhi wa ku Yeliko, nayo wamapitapita mmikwakwa ya mmujhi umeneo. 2Padali ni mundhu mmojhi mmujhi mmenemo wamatanidwa Zakayo. Mmeneyo wadali wamkulu wa wandhu wolandila malipilo ni wadali ni chuma chambili. 3Iye wamafuna wamuone Yesu kuti ni mundhu wamtundu wanji, nambho wadalepela kumuona ndande iye wadali wamfupi, ni wandhu adachuluka. 4Chimwecho, wadathamangila mchogolo, wadakwela mumtengo wa mkuyu kuti wakhoze kumuona Yesu, pakuti wamajhiwa Yesu wamapita mnjila imeneyo. 5Yesu yapo wadafika pamalo yameneyo, wadapenya mmwamba mwa mtengo ni kumkambila, “Zakayo, chika chisanga, pakuti lelo sinikhale mlendo kukhomo lako.” 6Zakayo wadachika chisanga ni kumlandila Yesu kwa kukondwela. 7Wandhu wonjhe yapo adaona yameneyo adayamba kudandaula ni kukamba, “Wapita kukhala mlendo wa mundhu wa machimo.”
8Nambho Zakayo wadaima ni kwaakambila Ambuye, “Vechelani Ambuye! Ine sinaninghe wosauka chuma changa chakumojhi, ningati namlanda mundhu chindhu chalichonjhe, sinimbwezele kanayi.”
9Yesu wadamkambila, “Lelo uomboli wajha mnyumba ino, pakuti uyu nayo ni wa mwana wa mmuna wa Ibulahimu. 10Pakuti ine mwana wa Mundhu najha kufunafuna ni kulamicha chijha chidataika.”
Chifani cha mbowa khumi
Matayo 25:14-30
11Wandhu yapo amavechela Yesu, amaganiza kuti Ufumu wa kumwamba ulipafupi kuchokela. Ndande adali pafupi kufika mmujhi wa ku Yelusalemu. Ndiipo Yesu wadakambila chifani, 12Yesu wadakamba, “Padali ni mundhu mmojhi wa khamu la chifumu, wadapita kujhiko lakutali kuti wakalandile ulamulilo wokhala mfumu, ni pambuyo pake wabwele ni ulamulilo. 13Nambho, wakali osachoke, wadatana mbowa zake khumi ni kumpacha kila mmojhi gawo la ndalama ni kwakambila, ‘Mchitile malonda ndalamazi mbaka yapo sinibwele.’ 14Nambho wandhu ammujhi umenewo adamuipila ni adaatuma athenga kuti apite akamkambile, ‘Sitifuna mundhu mmeneyo wakhale mfumu wathu.’ ”
15“Ata chimecho mundhu mmeneyo wadapachidwa ulamulilo ni kubwela kukhomo kukhala mfumu. Ndiipo wadaatana wajha mbowa wake wadaapacha ndalama, kuti wajhiwe phindu ilo apata kila mmojhi. 16Mbowa woyamba wadafika ni kukamba, ‘Ambuye, kwa fungu lijha mudanipacha napata mafungu khumi kuchokana ni ndalama zijha mdanipacha.’ 17Mbuye yujha wadamkambila, ‘Wachitabwino, pakuti wakhala mbowa wokhulupilika pa vindhu vochepa, nikuningha ulamulilo wa mijhi khumi.’ 18Mbowa wakawili wadafika ni wadakamba, ‘Mbuye, napata mafungo ya sano kuchoka mu fungo limojhi ilo mudanipacha.’ 19Nayo wadamkambila, ‘Niiwe nikuningha ulamulile mijhi isano.’ 20Mbowa mwina wadafika ni kukamba, ‘Bwana, ndalama yanu iyo mudanipacha iyi yapa. Nidaisunga bwino kupunda mu chitambaya. 21Ndande yake nimaopa pakuti imwe ni mundhu uyo siufuna kuchefyedwa, utenga ivo osati vako, ni kucha yapo siudavyale.’ 22Bwana wake wadamuyangha, ‘Iwe ni mbowa woipa, nikulamula kuchokana ni umo wakambila! Ngati udajhiwa kuti ine ni mundhu woipa, uyo nitenga ndalama za wandhu wina izo osati zanga, ni kuvuna vakudya ivo sinidavyale, 23chipano ndande yanji siudawapache ndalama wandhu wochocha liba kuti nikabwela nitenge ndalama zanga pamojhi ni phindu?’ 24Chimwecho wadakambila anyiwajha adaima pafupi, ‘Mlandeni ndalamazo mkampache uyo wali ni mafungo khumi.’ 25Na anyiiwo adamkambila, ‘Nambho bwana, mmeneyo wali nayo mafungo khumi!’ 26Iye wadayangha, ‘Nikukambilani kuti kila uyo wali ni kandhu, siwaongezeledwe. Nambho kwa uyo walibe kandhu, ata chochepa icho walinacho, siwalandidwe. 27Nambho, anyiwajha adani wangawa, yawo siadafune nikhale mfumu, mjhenao pano kuti niwaphe pamaso panga.’ ”
Yesu walowa mu Yelusalemu kwa chikondwelo
Matayo 21:1-11; Maluko 11:1-11; Yohana 12:12-19
28Yesu yapo wadamaliza kukamba chimwechio, wadachogolela kupita ku Yelusalemu. 29Yapo wadawandikila ku mijhi ya Besifage ni Besania, pafupi ni phili ilo litanidwa phili la Mizetuni, wadatuma woyaluzidwa wake awili pakati pa oyaluzidwa wake, wadakambila, 30“Mpite mmujhi uwo uli mchogolo mwanu. Yapo simulowe mmenemo, simumpheze phunda uyo siwadatumike ni mundhu waliyonjhe, wamangidwa mmasuleni mjhe nayo pano. 31Mundhu uyo siwakufunjheni ndande yanji mummasula phunda, mkambileni, amfuna Ambuye.”
32Ndiipo adapita ni adakomana ngati umo adakambilidwa ni Yesu. 33Yapo amammasula phunda yujha, mwene phunda wadaafunjha, “Ndande yanji mummasula phunda?” 34Anyiiwo adayangha, “Ambuye amfuna.” 35Ndiipo, adampeleka kwa Yesu phunda yujha. Adayala njhalu pamwamba phunda ni kumkweza Yesu pamwamba pake. 36Yapo wamaendekela ni ulendo, wandhu adayala njhalu zao panjila.
37Yapo wadawandikila ku Yelusalemu, pa njila iyo ichikila pa phili la mizeituni, gulu lonjhe la wochatila wake adayamba kukondwela ni kumtamanda Mnungu pokweza mvekelo ndande ya vodabwicha vonjhe ivo adavionapo. 38Adakamba, “Wali ni mwawi Mfumu uyo wakujha mu jhina la Ambuye. Mtendele ukhale kumwamba kwa Mnungu, ni ulemelelo kumeneko kumwamba kupunda!” 39Afalisayo wina yawo adali mkati mwa gulu lijha, yapo adaona chimwecho, adamkambila Yesu, “Oyaluza, anyindileni oyaluzidwa wanu akhale chete!” 40Yesu wadayangha, “Nikukambilani kuti, ngati anyiyawa saakhale chete, miyala siibule phokoso.”
Yesu waulilila mujhi wa Yelusalemu
41Yesu yapo wadawandikila ni kuuona mujhi wa Yelusalemu, wadaulilila, 42wadakamba, “Idakakhala bwino ngati udakajhiwa lelo vindhu ivo vipeleka mtendele kwako! Nambho chipano yabisika pamaso pako. 43Masiku yatokujha, yapo adani wako sakuzungulile ni kukuhundukila madela yonjhe. 44Ndiipo Sakugweche panjhi iwe pamojhi ni wandhu wako onjhe. Siakusiila ata mwala uwo siukhalile pamwamba pa wina ndande siumafune kujhiwa ndhawi iyo Mnungu wakupelekela uwomboli.”
Yesu mu nyumba ya Mnungu
Matayo 21:12-17; Maluko 11:15-19; Yohana 2:13-22
45Ndiipo, Yesu wadalowa mkati mwa malo ya nyumba ya Mnungu ni kuyamba kwaatopola wandhu wajha amachita malonda mmenemo, 46wadakamba, “Yalembedwa, ‘Nyumba yanga siikhalae nyumba ya mapembhelo, nambho anyiimwe mwaichita kukhala mbhanga ya anghungu.’ ”
47Yesu wamatoyaluza mu nyumba ya mapembhelo siku ni siku. Nambho achogoleli, wakulu akulu wa ajhukulu ni oyaluza a mathauko, amafunafuna njila yakumupha Yesu, 48Nambho sadapate njila ya kumgwila, ndande wandhu wonjhe amamvechecha.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Luka 19: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.