Yohana 6
6
Yesu waapacha wandhu elufu zisano chakudya
Matayo 14:13-21; Maluko 6:30-44; Luka 9:10-17
1Pambuyo pa yameneyo, Yesu wadayomboka nyanja ya Galilaya, iyo imatanidwanjho Tibelia. 2Ndiipo Gulu lalikulu la wandhu lidaendekela kumchota ndande adaviona vizindikilo ivo wadachita pa kwalamicha odwala. 3Ndiipo Yesu wadakwela kuphili, wadakhala pamojhi ni oyaluzidwa wake. 4Ndhawi imeneyo phwando la Pasaka la Ayahudi lidawandikila. 5Yesu yapo wadapenya ni kuona gulu lalikulu nilimjhela, wadamkambila Filipo, “Sitigule kuti mabumunda yakudya wandhu adye?” 6Yesu wadakamba chimwecho kwa kumuyesa Filipo, pakuti wadajhiwa icho siwachichite.
7Ndiipo Filipo wadamuyangha, “Ata ngati tidakhala ni ndalama zochuluka sizikwana kughula chakudya cha kwakwana wandhu anyiyawa, hata ngati kila mmojhi wasiwapachidwe chibandu chaching'onope”
8Oyaluzidwa wake mwina uyo wamatanidwa Andulea, mbale wake wa Simoni Petulo, wadamkambila, 9“Walipo mnyamata mmojhi uyo wali ni mabumunda yasano iyo yakonjedwa kwa ufa wa shayili ni njhomba ziwili, nambho vindhu ivi sivikwana kwa wandhu onjhewa?”
10Ndiipo Yesu wadakamba, “Akambileni wandhu akhale panjhi.” Pamalopo padali ni matengo yayafupiyafupi yambili. Ndiipo adakhala, adalipo wachimuna elufu zisano. 11Chimwecho Yesu wadatenga mabumunda, wadaayamika Amnungu, wadagaawila wandhu anyiyao adakhala panjhi, kila mmojhi wadapata ngati umo wadafunila, wadachita chimwecho ni zijha njhomba. 12Wandhu yapo adakhuta, Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, “Kusani vipande ivo va khala visadataika.” 13Chimwecho adakusa vipande vijha va mabumunda ni kuvitila mvitundu. Adavijhaza mvitundu kumi ni viwili.
14Ndiipo wandhu anyiwajha yapo adaona vizindikilo ivo wadachita Yesu, adakamba, “Zenedi uyu nde mlosi uyo wakujha pa jhiko.” 15Yesu yapo wadajhiwa kuti wandhu amafuna amgwile dala amchite mfumu kwa mbhavu, wadajhipatula, ni kupita yokha ku phili.
Yesu wayenda pamwamba pa majhi
Matayo 14:22-33; Maluko 6:45-52
16Jhuwa yapo limabila, oyaluzidwa wake adachika kunyanja, 17adakwela sitima kupita ku Kapelinaumu. Mdima udalowa nambho Yesu wadali wakali osafike. 18Nyanja idayamba kuvunduka ndande ya vuma wa mkulu. 19Oyaluzidwa yapo adapita patali ngati meta zitatu kapina zinai, adamuona Yesu ni waenda pamwamba pa majhi, wadawandikila sitima, adaopa kupunda. 20Ndiipo Yesu wadakambila, “Simudaopa, ni ine!” 21Yapo adamkalibisha Yesu mu mbwato, ndhawi imweyo adafika kujhiko ilo amapita.
Wandhu amfunafuna Yesu
22Mawa lake, gulu la wandhu yao adakhaalila kuchija la kawili la nyanja nipo adajhiwa kuti kudalipo ni bwato umojhipe, ni Yesu siwadakwele pamojhi ni oyaluzidwa wake, nambho oyaluzidwa adali apita okha. 23Chimwecho zidafika mabwato yina kuchoka ku Tibelia kumalo uko adadya wandhu mabumunda, Ambuye Yesu yapo adayamika Amnungu. 24Wandhu yapo adajhiwa kuti Yesu ni oyaluzidwa wake achokapo pamenepo, adakwela mbwato kupita ku Kapelinaumu kumfunafuna.
Yesu ni Bumunda ilo lipeleka Umoyo
25Yapo adampheza kuchija lakawili la nyanja adamfunjha, “Oyaluza mwafika siku lanji pano?”
26Yesu wadayangha, “Zene nikukambilani, munifunafuna osati ndande mudaviona vizindikilo, nambho ndande mudadya mabumunda ni mudakhuta. 27Msadajhichaucha ndande ya chakudya icho chilula, nambho jhichaucheni ndande ya chakudya icho sichilula ndande ya umoyo wa muyaya. Mwana wa Adamu uyo Atate amchimikiza siwakupacheni chakudya chimenecho.”
28Ndiipo adamfunjha Yesu, “Tichite chiyani kuti tikhoze kuichita njhito ya Amnungu?”
29Yesu wadayangha “Ino nde njhito iyo Amnungu afuna muichite, kumkhulupilila uyo amtuma.”
30Ndiipo adamfunjha, “Siutichitile chizindikilo chanji tione kuti tikhoze kukukhulupilila? Bwanji, siuchite chindhu chanji? 31Azee wathu adadya icho chidatanidwa mana yapo adali kuphululu, ngati umo yalembedwa, ‘Wadaapacha chakudya icho chidachoka kumwamba.’ ”
32Ndiipo Yesu wadakambila, “Zene nikukambilani, osati Musa uyo wadakupachani chakudya kuchoka kumwamba, nambho Atate wanga nde yao akupachani chakudya cha uzene kuchoka kumwamba. 33Pakuti bumunda la Amnungu nde uyo wachika kuchoka kumwamba ni kwapacha umoyo wandhu a jhiko la panjhi.”
34Ndiipo adamkambila, “Tipache chakudya chimenelo siku zonjhe.”
35Chimwecho wadaakambila, “Ine nde chakudya cha umoyo. Uyo wakujha kwanga siwaona njala ni uyo wanikhulupilila siwaona lujho muyaya. 36Nambho ngati umo nidakukambilani ata ngati mwaniona simunikhulupilila. 37Wandhu onjhe yao Atate sianipache sianichate, ni mundhu waliyonjhe uyo wakujha kwanga sinimkana, 38pakuti nachika kuchoka kumwamba osati ndande yo chita ivo nivifuna, nambho kuchita ngati umo wafunila uyo wanituma. 39Ni umu nde umo afunila yawo anituma, sinida mtaiza ata mmojhi pakati pa anyiyao anipacha, nambho nahyuche onjhe siku lo thela. 40Chindhu cha chikulu icho achifuna Atate wanga kuti, waliyonjhe uyo wamuona mwana ni kumkhulupilila wakhale ni umoyo wa muyaya, nane sinimuhyuche siku lo thela.”
41Ndiipo, Ayahudi adayamba kumng'olong'otela yapo wadakamba kuti, “Ine nde chakudya icho chachika kuchoka kumwamba.” 42Niamakamba, “Uyu osati Yesu mwana wa Yusufu? Tajhiwa atate wake ni amake! Bwanji wakamba kuti iye wadachika kuchoka kumwamba?”
43Ndiipo Yesu wadaakambila, “Siyani kung'olong'otelana mwachina wene kwa mwachinawene. 44Palibe mundhu uyo wakhoza kujha kwanga, ngati siwadaghuzidwe ni Atate yao anituma, nane sinimuhyuche mundhu mneyo siku lo thela. 45Yalembedwa mvikalakala va alosi, ‘Wandhu wonjhe sayaluzidwe ni Amnungu.’ Waliyonjhe uyo waavela Atate ni kujhiyaluza kwa iwo, wakujha kwanga. 46Palibe uyo waonapo Atate, nambho uyo wachoka kwa Amnungu, mmeyo nde uyo waona Atate. 47Nikukambilani zene, uyo wakhulupilila wali ni umoyo wa muyaya. 48Ine nde chakudya cha umoyo. 49Azee wanu adadya chakudya icho chitanidwa mana ku phululu, nambho adamwalila. 50Nambho chino nde chakudya icho chichoka kumwamba, kuti waliyonjhe uyo wakudya siwadamwalila. 51Ine nde chakudya chili cha moyo icho chachika kuchoka kumwamba. Mundhu waliyonjhe uyo siwadye chakudya ichi siwakhale moyo muyaya. Ni chakudya icho sinimpache, nde thupi langa ilo nichocha ndande ya wandhu ajhiko la panjhi.”
52Ndiipo Ayahudi adayamba kulimbana pakati pao, “Siwakhoze bwanji kutipacha thupi lake, tidye?”
53Ndiipo Yesu wadaakambila, “Zene nikukambilani, mkasiya kudyaa thupi la mwana wa Mundhu ni kumwa mwazi wake, simukhala ni umoyo mkati mwanu. 54Kila mmojhi uyo siwadye thupi langa ni kumwa mwazi wanga wali ni umoyo wa muyaya, nane sinimuhyuche siku lo thela. 55Ndande thupi langa nde chakudya cha uzene, ni mwazi wanga nde chakumwa cha uzene. 56Uyo wakudya thupi langa ni kumwa mwazi wanga, siwakhale mkati mwanga, nane sinikhale mkati mwake. 57Ngati umo Atate yawo ali amoyo adanitumila, nane nili wamoyo kupitila iwo, chimwecho uyo waniidya ine siwakhale moyo kupitila ine. 58Chino nde chakudya icho chachika kuchoka kumwamba, osati ngati mana iyo adadya azee wanu, ndiipo adamwalila. Uyo wakudya bumunda lino siwakhale moyo muyaya.” 59Yesu wadakamba mawu yameneyo yapo wamayaluza ku Kapelunaumu.
Mawu yayo yapeleka umoyo wa muyaya
60Chimwecho, ochatila wake ambili yapo adavela mawu yameneyo, adakamba, “Mayaluzo yaya yolimba! Yani wakhoza kuyavomela?”
61Yesu wadajhiwa mumtima mwake kuti oyaluzidwa wake amato dandaulila mawu limenelo, wadaafunjha, “Ndande yanji mayaluzo yaya yakujhujhumuchani? 62Siikhale bwanji yapo simumuone Mwana wa Mundhu niwabwela kupita kumwamba uko wadachoka? 63Mzimu wa Amnungu nde uwo uchocha umoyo, thupi silikhoza kandhu. Mawu yayo nakukambilani ni mzimu ni umoyo. 64Nambho, akumojhi wanu saakhulupilila.” Yesu wadaajhiwa kuyambila mmayambo anyiyawo saamkhulupilila, ni uyo siwamng'anamuke. 65Chimwecho, wadakamba, “Nde ndande nidakukambilani kuti palibe uyo wakhoza kujha kwaine popande kukhozechedwa ni Atate wanga.”
66Ndhawi imweyo, ochatila ambili pakati pao adamsiya, siadachogozane nayenjho. 67Ndiipo, Yesu wadaafunjha ochatila khumi ni awili, “Anyiimwe namwe mfuna kuchoka?”
68Simoni Petulo wadamyangha, “Ambuye tipite kwa yani? Akati imwe muli ni mawu ya umoyo wa muyaya. 69Ife tikhulupilila, ni tijhiwa kuti imwe nde yujha Oyela Amnungu”
70Yesu wadaakambila, “Bwanji, sinida kusangheni anyiimwe khumi ni awili? Ata chimwecho mmojhi wanu Satana!” 71Yesu wamamkamba nghani za Yuda mwana wa Isikaliyote, mmojhi wao oyaluzidwa anyiwajha khumi ni awili, uyo pambuyo wadamgulicha.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Yohana 6: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.