Yohana 5
5
Yesu wamlamicha mundhu wovuwala Siku lo Pumulila
1Pambuyo pa yameneyo kudalipo ni phwando la Ayahudi, nayo Yesu wadapita Ku Yelusalemu. 2Kumeneko ku Yelusalemu, pafupi ni chicheko icho chitanidwa chicheko cha mbelele, kudaliko ni thiwi ilo kwa mkambo wa Chihebulaniya, Betizata, ilo lidazungulilidwa ni khumbi zisano. 3Mkati mwake mudali odwala ambili, osapenya, andendele, ni ovuwala. Amalindilila majhi yavundulidwe, 4pakuti ndhawi za mbili mtumiki wa kumwamba wa Amnungu wamachika ndhawi zina ni kuyavundula majhi. Mundhu waliyonjhe uyo wachogolela kubila mmajhi yayo yamavundulidwa, wamalama ndhenda yaliyonjhe iyo wamadwala. 5Ndiipo, pamwepo wadalipo mundhu mmojhi uyo wadali odwala kwa ndhawi ya vyaka selasini ni nane. 6Yesu yapo wadamuona mundhu mmeneyo wagona pamenepo ni kujhiwa kuti wadakhala kwa ndhawi ya itali, wadamfunjha, “Bwanji, ufuna kulama?”
7Nayo wadayangha, “Wakulu, ine nilibe mundhu onibiza mthiwi majhi yapo yavundulidwa. Yapo niyesa kulowa, mundhu mwina wanichogolela.”
8Yesu wadamkambila, “Ima tenga chika lako ujhiyenda.” 9Pampajha mundhu mmeneyo wadalama, wadatenga chika lake ni kuyamba kuyenda.
Chindhu ichi chidachitika Siku lo Pumulila. 10Chimwecho Ayahudi wina adamkambila mundhu mmeneyo walamichidwa, “Lelo ni Siku lo Pumulila, thauko likaniza iwe kutenga chika lako.”
11Nambho iye wadaayangha, “Mundhu uyo wanilamicha nde uyo wanikambila, ‘Tenga chika lako, uyende.’ ”
12Ndiipo adamfunjha, “Mundhunji, wakukambila utenge chika lako ujhipita?”
13Nambho iye siwamamjhiwe mundhu uyo wadamlamicha, ndande Yesu wadato choka pamalo pamenepo ni kusingizikana ni ghulu lalikulu la wandhu.
14Pambuyo pake, Yesu wadampheza mmeneyo walamichidwa Panyumba ya Amnungu, wadamkambila, “Walama chipano, usadachitanjho machimo, dala sichidakuphezanjho chindhu choipa kupunda.”
15Chimwecho mundhu yujha, wadapita kwakambila achogholeli wa Ayahudi kuti Yesu nde uyo wadamlamicha.
16Ayahudi adayamba kumchaucha Yesu, ndande wadachita chindhu chimenecho Siku lo Pumulila. 17Ndiipo Yesu wadayangha, “Atate wanga achita njhito mbaka chipano, nane nifunika nichite njhito.”
18Kuchokana ni mawu yaya, achogholeli wa Ayahudi amafuna njila ya kumpha Yesu, osati kowanangape thauko la Siku lo Pumulila, nambho ndande yokamba kuti Amnungu nde Atate wake, chimwecho iye wadajhichita sawa ni Amnungu.
Ulamuli wa Mwana wa Amnungu
19Yesu wadakambila, “Uzene nikukambilani, Mwana siwakhoza kuchita chindhu yokha, icho wachiona Atate wake achita, nde icho Mwana wakhoza kuchichita. 20Atate amkonda Mwana ni kumlangiza yajha Atate wene achita, ndiipo siwamlangize vindhu vavikulu kupitilila ivi, namwe simudabwe. 21Ngati umo Atate wahyukicha omwalila ni kwapacha umoyo, chimwecho Mwana wapacha umoyo yao wakonda. 22Atate siamulamula mundhu waliyonjhe, njhito yonjhe yo lamula wamsiila Mwana, 23kuti wandhu wonjhe amlemekeze Mwana ngati umo walemekezela Atate. Waliyonjhe uyo siwamlemekeza Mwana siwalemekeza yao amtuma.”
24“Zene nikukambilani, mundhu waliyonjhe uyo wavela mawu yanga ni kwaakhulupilila Amnungu yawo anituma, ali ni umoyo wa muyaya. Sialamulidwa muyaya, nambho wachoka kunyifa ni kulowa kuumoyo. 25Zene nikukambilani, ndhawi ikujha ni chipano ilipo, yapo omwalila savele mvekelo wa Mwana wa Amnungu, ni anyiyao savele mvekelo saakhale ni umoyo. 26Ngati umo Atate ali chiyambo cha umoyo, chimwecho ampacha Mwana wao kukhala chiyambo cha umoyo. 27Chimwecho ampacha ulamuli olanga ndande iye ni mundhu Amnungu watuma. 28Simudadabwa chindhu ichi, mate yake ndhawi ikujha yapo onjhe anyiyawo ali mviliza savele mvekelo wake, 29onjhe sahyuke, anyiyawo achita vabwino sahyuke ni kupata umoyo wa muyaya, ni anyiwajha achita voipa sahyuke ni kulangidwa.”
Anyiwajha akamba nghani za Yesu
30“Ine sinikhoza kuchita chindhu kwa mbhavu zanga namwene. Ine ni lamula ngati umo nivelela kuchoka kwa Atate, ni lamulo langa ni lo vomelezeka. Pakuti sinifuna kuchita chikondi changa namwene, nambho umo wakondela uyo wanituma.”
31“Ngati nikajhichochela umboni namwene, umboni wanga siukhoza kuvomeleka kuti wa uzene. 32Nambho walipo mwina uyo wanichochela umboni, chimwecho nijhiwa kuti umboni wake ni wazene. 33Anyiimwe mdamtuma mundhu kwa Yohana, nayo wadauchocha umboni wa uzene. 34Ine sinifuna wandhu anichochele umboni, nikamba vindhu ivi kuti muomboledwe. 35Yohana wadali ngati nyali iyo imawala, namwe mdali tayali kukondwela dangalila la ndhawi yo chepa. 36Nambho ine nili ni umboni waukulu kupunda kupitilila wa Yohana. Pakuti njhito izo nipota, izo anipacha Atate nizichite, ni vizindikilo ivi nivichita nde ivo vinichochela umboni kuti Atate nde yao anituma. 37Atate yao anituma nde yao anichochela umboni. Anyiimwe simuda velepo mvekelo wake, kapina kumuona umo ali, 38ni anyiimwe simuyakhulupilila yayo niyakamba pakuti simwaakhulupilila yawo anituma. 39Anyiimwe muyapenyechecha Malembo Yoyela kwa kuganizila kuti simpate umoyo wa muyaya kwa kuyapenyechecha, nambho malembo yaya yanichochela umboni ine! 40Chimwecho simufuna kujha kwanga kuti mpate umoyo.”
41“Ine sinifuna ulemelelo kuchoka kwa wandhu. 42Nambho ine nikujhiwani kuti mulibe chikondi cha Amnungu mmitima mwanu. 43Ine najha kwa ulamuli wa Atate wanga, anyiimwe simunilandila, nambho mundhu mwina wakajha ni ulamuli wake mwene, mmeneyo simumlandile. 44Simukhoze bwanji ku khulupilila ni kwina mkonda kupachana ulemelelo mwachinawene kwa mwachinawene, simfunafuna ulemelelo uwo uchokela kwa Mnungu yokha? 45Simudaganizila kuti ine sinikupacheni mlandu kwa Atate. Musa uyo mwa mumkhulupilila anyiimwe nde uyo siwakupacheni mlandu. 46Ngati mdakamkhulupilila Musa, mdakanikhulupilila ni ine, ndande Musa wadalemba nghani zanga. 47Nambho simuyakukhulupilila yajha wayalemba, sumukhoze bwanji kukhulupilila mawu yanga?”
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Yohana 5: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.