Vichito 2
2
Kujha kwa Mzimu Woyela
1Yapo lidafika siku la pwando la Pentekosite, wandhu wonjhe yawo adamkhulupilila Yesu adasonghana malo yamojhi. 2Mwachizulumukila mvekelo waukulu ngati mkokomo wa mbhepo udachoka kumwamba ni kuijhaza nyumba yonjhe mujha adakhala wajha atumwi. 3Kudatulukila malilime ya moto yayo yadagawika ni kukhala pamwamba pa kila mmojhi wawo. 4Wandhu wonjhe adajhazidwa ni Mzimu Woyela, adayamba kukamba mikambo ya chilendo, ngati umo wadafunila Mzimu Woyela.
5Ndiipo kudali Ayahudi yawo amakhala mu Yelusalemu, yawo adachokela ku maiko yonjhe ya pajhiko lapanjhi. 6Yapo adavela mapokoso ya mvekelo, gulu la wandhu lidasonghana pamojhi niadabwa, pakuti kila mmojhi wao wamaavela wokhulupilila wajha niakamba kila mmojhi kwa mkambo wake mwenewake. 7Wandhu wonjhe amazizwa ni kudabwa, niakamba, “Anyiyawa wonjhe taavelawa osati wandhu Agalilaya! 8Ikhala bwanji kuti kila mmojhi wathu waavela niakamba kwa mkambo wa kukhomo? 9Wina wathu achokela ku Palisi ni wina ku Medi ni wina ku Elamu. Wina wathu ni wandhu a ku Mesopitaniya ni ku Yudeya ni Kapadokiya ni Ponto ni Asiya. 10Wina achokela ku Filigiya ni Pamfiliya ni ku Misili ni madela ya Libiya pafupi ni Kilene ni wina ni alendo kuchokela ku Loma, 11Ayahudi ni wandhu yawo adalowa mchikhulupililo cha Ayahudi, wina adachokela ku Kilete jhiko ilo lazungulilidwa ni majhi ni ku Alabu, ife taonjhe taavela wandhu anyiyawa niakamba kwa mikambo yathu tachinawene nghani za vindhu vavikulu ivo avichita Amnungu.” 12Akali kudabwa ni kuopa adafunjhana, “Mate ya vindhu ivi ni chiyani?” 13Nambho wina adadelela niakamba, “Wandhu anyiyawa alojhela!”
Petulo wayaluza wandhu
14Petulo wadaima pamojhi ni wajha atumwi khumi ni mmojhi, wadakweza mvekelo wake ni kwauzila gulu la wandhu lijha, niwakamba, “Ayahudi anjanga ni wandhu wonjhe yawo mkhala mu Yelusalemu, mlindile nikukambileni ni anyiimwe mnivechele bwino mawu yanga. 15Zenedi wandhu anyiyawa siadalojhele ngati umo muganizila, pakuti saa zino kukali saa tatu umawa! 16Nambho uzene nikuti chindhu ichi nde chijha chidakambidwa ni mlosi Yoeli, niwakamba,
17Ambuye Amnungu akamba, ‘Pa masiku yothela,
sinapache wandhu wonjhe Mzimu wanga.
Wana wanu ni anamwali wanu sialosele,
anyamata wanu saone maloso,
azee wanu saalote maloto.
18Yetu ata mbowa zanga waachimuna ni waachikazi,
sinapache Mzimu wanga pa masiku yameneyo,
anyiiwo siachoche ulosi.
19Sinichite vodabwicha kumwamba
ni vodabwicha pajhiko la panjihi.
Sikukhale mwazi, moto ni uchi waukulu.
20Jhuwa silikhale mdima,
mwezi siukhale wofiwila ngati mwazi,
likali osafika siku lijha lalikulu ni laulemelelo la Ambuye.
21Nambho, waliyonjhe uyo siwapembhele kwa jhina la Ambuye siwaomboledwe.’”
22“Anyiiwme wandhu a ku Izilaeli vechelani mawu yaya niyakamba. Yesu wa ku Nazaleti wadali mundhu uyo wadachimikizidwa kwanu ni Mnungu kupitila vodabwicha, vozizicha ni vizindikilo, ivo Mnungu wadavichita pakati panu kupitila iye, ngati umo mwachinawene wake mujhiwila. 23Kuyambila mmayambo Mundhu wadafuna anyiimwe mumphe Yesu, ni anyiimwe mdampha kwa kwasiila wandhu woipa ampachike pamtanda. 24Nambho Mnungu wadamhyukicha ni kumchocha kupweteka kwa nyifa. Pakuti siidakhozeke kuti mbhavu za nyifa zimmange iye ngati mundhu womangidwa mndende. 25Pakuti Daudi wadamkambilila Yesu chimwechi,
‘Nidaaona Atate pachogolo panga masiku yonjhe,
Ndande yake Iye wali kujhanja langa la kwene, sinitingizika.
26Chimwecho, mtima wanga wajhazidwa ni chikondwelelo,
lilime langa likondwela kupunda,
thupi langa nalo silikhale kwa chiyembekezo.
27Chifuko imwe Ambuye Amnungu simunisiya mu jhiko la wandhu akufa,
simumusiya mbowa wanu wopatulika kuwolela mchiliza.
28Mwanilangiza njila iyo inichogoza kuumoyo, simunijhaze chimwemwe kwa kukalapo kwanu.’”
29Abale wanga a Izilaeli, nifuna nikukambileni kwa kulimba mtima pamaso panu kuti mbuye wathu Daudi wadafa nikuikidwa mmanda, ni manda yake yakalipo mbaka lelo. 30Iye wadali mlosi ni wadajhiwa icho Mnungu wadamuahidi iye. Mnungu wadamuahidi kwa kulumbila kuti mundhu mmojhi wa mbadwa wa Daudi siwakhale mfumu ngati umo wadali Daudi. 31Daudi wadaona yayo siwachite Mnungu mchogolo, ndiipo wadakamba nghani za nyifa ya Yesu,
Siwadasiidwe mujhiko la wandhu akufa,
thupi lake silidaolele mu manda.
32Mnungu ndeuyo wadamuhyukicha Yesu mmeneyo, ni ife taonjhe ni amboni anghani imeneyo. 33Ngati Yesu walemekezedwa kwa kuikidwa ku jhanja la kwene la Mnungu, walandila Mzimu Woyela ngati umo adaahidi Atate. Chipano Yesu watipacha ife Mzimu Woyela, pa kumpacha kila mmojhi ngati umo muonela ni kuvela.
34“Daudi mwene wake siwadakwele kumwamba, nambho iye mwene wake wadakamba,
Ambuye wadaakambila Ambuye wanga,
‘Khala pano pa jhanja langa la kwene
35mbaka yapo sinaike adani wako kukhala paulamulilo wako.’”
36“Chipano, wandhu wonjhe a mu Izilaeli ajhiwe zene kuti, Yesu uyo anyiimwe mudampachika pamtanda, Amnungu amchita kukhala Mbuye ni Kilisito muomboli.”
37Wandhu yapo adaevela chimwecho adavela kupwetekeka mmitima yawo ni adamfunjha Petulo ni anyiwajha atumwi anjake, “Achabale wathu, tichite chiyani?”
38Petulo wadaayangha, “Lapani, kila mmojhi wanu mmbatizidwe kwa jhila la Yesu Kilisito, kuti mlekeleledwe machimo yanu ni kulandila ahadi ijha ya Mzimu Woyela. 39Pakuti ahadi iyi ni ya anyiimwe pamojhi ni achanawanu ni kwa anyiwajha wonjhe ali kutali ni wandhu wonjhe yawo atanidwa ni Ambuye Mnungu wathu.”
40Petulo wadaaonya pakukamba mawu yambili ni kwaapembha niwakamba, “Mjhipenyelele ni mbadwa uwu woipa.” 41Wandhu ambili adakhulupilila mawu ya Petulo ni adabatizidwa, wandhu ngati elufu zitatu adawonjezekela pa gulu lawo siku limenelo. 42Wonjhe adali kuvechela mayaluzo ya atumwi kila siku, amakomana pamojhi niadya chakudya cha Ambuye ni kupembhela.
Ukhalo wa wandhu wajha amkhulupilila Kilisito
43Wandhu wonjhe adali pajha adali ni mandha ndande ya vodabwicha vambili ni vizindikilo ivo vidachitidwa ni atumwi. 44Wokhulupilila wonjhe adali ni maganizo yamojhi, ni amachita kila kandhu kwa mgwilizano. 45Adagulicha vyuma vawo ni vindhu ivo adalinavo, adamgawila kila mudhu kulingana ni umo wadafunila. 46Masiku yonjhe amakomana mmakhumbi la Nyumba ya Mnungu kwa mtima umojhi. Amadya chakudya pamojhi mmanyumba zao kwa kukondwela ni kwa mtima woyela, 47niamtamanda Mnungu ni wandhu wonjhe adaakonda atumwi ameneo, siku zonjhe Ambuye amachulucha wandhu yao amaomboledwa.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Vichito 2: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.