Vichito 16

16
Timoseo walunjana ni Poolo ni Sila
1Ndiipo Poolo wadafika ku Delibe ni Lisitila, uko wamakhala ochatila mmojhi wa chi Yahudi uyo wadamkhulupila Yesu wamatanidwa Timoseo, uyo amake adali ochatila wa Chiyahudi, nambho atate wake adali Agiliki. 2Timoseo wadali ni wamaelekeledwa bwino ni wajha wandhu adamkhulupila Yesu ku Lisitila ni Ikonio. 3Ndiipo Poolo wamafuna kumtenga Timeseo kuti wachatane ni iye, chimwecho wadamchita mdulidwe. Iye wadachita chimwecho ndande Ayahudi wonjhe yawo amakhala malo yameneyo amajhiwa kuti atate a Timoseo ni Agiliki. 4Yapo amapita mmijhi ijha, adaapacha wandhu ujha uthenga udachochedwa ni Atumwi ni achogoleli kujha ku Yelusalemu, ni adaakambila ayachate. 5Chimwecho wandhu adamkhulupilila Kilisito adaendekela kukhala nganganga mu chikhulupililo ni anyiwajha amakhulupila amaendekela kuchuluka siku hadi siku.
Poolo waona maloso
6Poolo ni achanjake adapita mmijhi ya Filigia ni Galatiya, ndande Mzimu Woyela udaakaniza kulalikila uthenga wa Bwino ku jhiko la Asia. 7Adafika mmalile mwa mujhi wa Musiya. Adayesa kulowa ku mujhi wa Bisiniya, nambho mzimu wa Yesu udaakaniza kulowa mmenemo. 8Chimwecho adapita kumujhi wa Musia, ni kufika ku Tuloa. 9Usiku ujha, Poolo wadaona maloso yayo wadamuona mundhu mmojhi kuchoka ku Makedoniya. Mundhu mmeneyo wadaima pachogolo pake ni kumpembha uku niwakamba, “Uyomboke ujhe ku Makedoniya dala ukatithangatile.” 10Poolo yapo wadaona maloso yameneyo, tidakonjeka msanga ni kumanga ulendo wopita kumujhi wa Makedoniya. Tidazindikila kuti Mnungu watitana kuti tikalalikile Uthenga Wabwino kujha ku Makedoniya.
Lidiya wamkhulupila Kilisito
11Tidamanga ulendo kwa sitima kuchokela ku Tuloa mbaka ku chilumba cha Samosilake. Siku ilo lidachatila tidayendekela ni ulendo mbaka ku mujhi wa Neapoli. 12Tidachoka kumeneko ni kupita mbaka ku Filipi, mujhi waukulu wa Makedoniya, uwo udali panjhi pa ulamulilo wa Aloma. Tidakhala mmujhi umenewo kwa masiku yochepa. 13Siku Lopumulila tidapita kubwalo kwa mujhi, mmbhepete mwa mchinje uko timaganiza kuti malo yochitila mapembhelo. Tidakhala ni kuyamba kukamba ni wachikazi yao adasonghana kumeneko. 14Mmojhi wa anyiwajha adativechela wadali Lidiya uyo wadachokela ku Tiyatila, uyo wamagulicha njhalu za mtengo wa ukulu. Iye wadali mundhu wa bwino. Ambuye Mnungu adamchita Lidiya wakhulupilile chijha wamakamba Poolo. 15Iye pamojhi ni wandhu wonjhe yawo amakhala mnyumba mwake adabatizidwa. Ndiipo wadatitana kunyumba kwake, niwakamba, “Ngati muuona kuti ine nakhulupilila Ambuye Yesu, majhani kukhomo kwanga mkhale.” Wadatipembha kupunda tipite kukhomo lake.
Poolo ni Sila aikidwa mndende
16Siku limojhi yapo timapita pamalo pampajha pochitila mapembhelo, tidakomana ni mbowa mmojhi wa mkazi uyo wadali ni chiwanda. Mwali mmeneyo wadali ni mzimu woombeza mkati mwake, uwo umampacha nghongono za kuombeza yayo siyachokele mchogolo. Mnamwali mmeneyo wamapacha opata ndalama zambili kwa njhito yake ya kuombeza. 17Mwali mmeneyo wadamchata Poolo ni ife malo yonjhe yayo timapita, uku niwakweza mvekelo, pokamba, “Wandhu anyiyawa ni atumwi wa Mnungu wa mkulu! Akukambilani umo mukhoza kuomboledwa!” 18Wadayendekela kukamba chimwecho kwa masiku yambili mbaka mawu yake yadamkwiicha Poolo. Poolo wadang'anamuka ni kuchinyindila chijha chiwanda niwakamba, “Kwa mbhavu za Yesu Kilisito, nikulamula uchoke mkati mwake!” Pampajha chijha chiwanda chidamchoka.
19Mambuye ayujha mwali yapo adaona chimwecho, adajhiwa kuti chikhulupi chao chopata ndalama chatha. Adaagwila Poolo ni Sila ni kwaakwekweta mbaka ku malo yayo wandhu amakomanilani kwa njhito za kila mtundu. 20Wadaapeleka Poolo ni Sila pachogolo pa alamuli aku Loma ni kukamba, “Wandhu anyiyawa ni Ayahudi, ayambicha mkangano mmujhi mwathu. 21Ayaluza kalidwe ilo ife wandhu a ku Loma sitiloledwa kuuvomela kapina kulichita.” 22Gulu lonjhe la wandhu lidalunjana kwaahundukila Poolo ni Sila.
Ndiipo wajha alamuli amilandu adalamula avulidwe njhalu zao ni kukwapulidwa vikwapu. 23Yapo adamaliza kwabula kupunda, adaikidwa mndende. Achogoleli adaakambila alonda, “Mwaalonde wandhu anyiyawa zenezene.” 24Wamkulu wa ndende yapo wadavela yameneyo, wadaaika Poolo ni Sila mchumba cha mkhati kupunda mwa ndende ni kwaamanga mmiyendo yao pingu ya mbao.
25Usiku pakati Poolo ni Sila amapembhela ni kumuimbila Mnungu nyimbo za matamando uku omangwidwa wina niwavechela. 26Kudaveka mvekelo wa chimtingiza mndhaka, icho chidatingiza msingi wa ndende. Pampajha vicheko vidachakuka kwamkamojhi, ni maunyolo yajha adamangidwa omangidwa ameneo yadamasuka ni kugwa panjhi. 27Yujha mlonda wa ndende yapo wadauka ni kuona vicheko vandende vachekuka, wamaganiza andende athawa, chimwecho wadasolomola upanga wake kuti wajhiphe. 28Nambho Poolo wadamtana kwa mvekelo waukulu niwakamba, “Usadajhipa pakuti ife taonjhe tili muno!”
29Yujha mlonda wa ndende wadatanicha nyali, ndiipo wadalowa msanga mkati mwa ndende mujha, wadajhitaya pachogolo pa Poolo ni Sila uku nawatendhemela kwa mandha. 30Ndiipo wadaatulucha kubwalo ni kukamba, “Olemekezeka nichite chiyani kuti niomboledwe?”
31Anyiiwo adamuyangha, “Akhulupilile Ambuye Yesu Kilisito, iwe pamojhi ni wandhu amnyumba mwako nde yapo siuomboledwe.” 32Chimwecho Poolo ni Sila adamlalikila uthenga wa Ambuye, yujha mlonda pamojhi ni wandhu wonjhe yao amakhala mnyumba mwake. 33Ndhawi imweiijha yujha mlonda wa ndende wadaatenga Poolo ni Sila ni kwaachuka mabala yao. Ndiipo yujha mlonda pamojhi ni wandhu wonjhe amnyumba mwake adabatizidwa. 34Wadaatenga Poolo ni Sila mbaka kukhomo kwake, wadaapacha chakudya. Iye Pamojhi ni wandhu amnyumba mwake adachita pwandho ndande chipano amkhulupilila Mnungu.
35Umawa wake alamuli aku Loma wadaatuma asikali waakulu kwa wamkulu wa ndende akakambe, “Amasule ni uwasiye wandhu achameneo ajhipita.”
36Yujha wamkulu wa ndende wadamkambila Poolo, “Alamuli atuma uthenga kuti nikusiyeni, chimwecho chokani, mapitani kwa mtendele.”
37Nambho Poolo wadamkambila asikali, “Ukamba chiyani! Anyiwajha alamuli siadaone cholakwa chilichonjhe icho tachita, nambho atibula mikwapulo pandhandala popande kutilamula. Ata chimwecho ife ni wandhu aku Loma. Nao afuna kuti tichoke kwa chisisi. Siikhozeka, asiyeni ajhepano atituluche kubwalo!”
38Wakulu wa sikali wajha adabwela ni kwaakambila anyiwajha alamuli mawu yajha wadakamba Poolo. Yapo adavela kuti Poolo ni Sila ni wandhu aku Loma, adaopa kupunda. 39Chimwecho adapita kwaapepecha, ndiipo wadaachocha mndende ni kwaapembha kuti achoke kubwalo kwa ujha mujhi. 40Poolo ni Sila adachoka mndende, adapita ku khomo kwa Lidiya, uko adakomana ni wajha wandhu adamkhulupalila Kilisito, adaathila mtima, ndiipo adachoka.

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Vichito 16: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល