Vichito 15

15
Atumwi ni achogoleli aphezana ku Yelusalemu
1Wandhu wina adachika ku Antiokiya ni achokela ku Yudea, nawo adayamba kwaayaluza wandhu osati Ayahudi yawo adamkhulupilila Yesu niakamba, “Simungakhoze kuomboka mbaka mchitidwe mdulidwe ngati umo lifunila thauko la Musa.” 2Nghani zimenezo zidaachita Poolo ni Banaba achuchane ni wandhu achemenewo. Chimwecho Poolo ni Banaba adasanghidwa pamojhi ni wandhu wina a ku Antiyokia yawo adamkhulupila Kilisito kupita ku Yelusalemu kukambilana ni atumwi ni azee ndande ya nghani izi.
3Wandhu ameneo adatumidwa ni gulu la wandhu adamkhulupilila Yesu, ni yapo adali mnjila kupitila kwa njila ya Fonoike ni Samaliya, adaakambila wandhu adamkhulupila Yesu, umo wandhu osati Ayahudi adamkhulupilila Mnungu, Uthenga umenewo adakondwela kupunda. 4Yapo adafika ku Yelusalemu adalandilidwa ni gulu la wandhu amkhulupila Yesu atumwi ni azee, nawo adaakambila kila kandhu icho wadachita Mnungu kupitila anyiiwo. 5Nambho wandhu wina adamkhulupila Yesu, yawo ali agulu la Mafalisayo adaima ni kukamba, “Wandhu achamenewo osati Ayahudi, afunika achitidwe mbulidwe ndiipo takambile achate thauko la Musa.”
6Atumwi ni achogoleli adasonghana pamojhi kuti akambilale nghani zimenezo. 7Yapo amafunjhana kwa ndhawi yaitali, Petulo uyo wadatanidwanjho Simoni wadaima ni kukamba, “Achakuluwanga ni achalongowanga, mujhiwa kuti mmayambo Mnungu wadanisangha ine pakati panu kuti nilalikile Uthenga Wabwino kwa wandhu osati Ayahudi, kuti nao avele ni kuukhulupilila. 8Mnungu uyo wajhiwa maganizo ya kila mmojhi, walangiza kuti waavomela pakwaapacha Mzimu Woyela ngati umo watipachila ife. 9Siwadasiyaniche pakati pathu ni anyiiwo, walekelela machimo yao ndande adamkhulupilila Yesu. 10Chipano, ndande yanji mfuna kumchucha Mnungu pa kwasenjha katundu woyaluzidwa, katundu uwo achatate wathu kapina ife sitingakhoze kunyakula? 11Siidakhala chimwecho, tikhulupilila kuti tiomboledwa kupitila ubwino wa Ambuye Yesu, naonjho aomboledwa kupitila ubwino umweo.”
12Msonghano wonjhe udakhala chete, uku niavechela Banaba ni Poolo niafotokoza umo Mnungu wadaatumila kuchita vizindikilo ni zodabwicha kwa wandhu osati Ayahudi. 13Yapo adamaliza kukamba chimwecho, Yakobo wadaakambila, “Achabale wanga nivecheleni. 14Simoni watifotokozela, umo Mnungu poyamba wadaasanghila wandhu yawo osati Ayahudi akhale wandhu wake. 15Mawu yaya ayakamba anyiyawa yali ngati mawu ya alosi, ngati umo Malembo Yoyela yakambila,
16‘Pambuyo pa kumaliza vindhu ivi, sinibwele,
siniumangenjho ufumu wa Daudi.
Sinimangenjho nyumba yake iyo yagomoka
ni kuizimikanjho kuti ilimbe,
17kuti wandhu wina wonjhe,
wandhu wonjhe osati Ayahudi yawo naatana kuti akhale wanga
sanifunefune ine.
18Nde umo nikambila ine Ambuye, nidachita chindhu ichi chijhiwike kuyambila mmayambo.’”
19Yakobo wadayendekela kukamba, “Yaya ni maganizo yanga kuti, kwaalagicha wandhu osati Ayahudi yawo amng'anamukila Mnungu. 20Mmalo mwake, tifunika tilembe kalata kwaakambila kuti sadadya vakudya ivo vachochedwa mahoka kwa viboliboli, ni asadachita chigololo, ni saadadya nyama iliyonjhe iyo yanyongopoledwa ni sadamwa mwazi. 21Kuyambila kale thauko la Musa lasomedwa, mnyumba zokomanilana Ayahudi Mmasiku Yopumulila, ni kulalikidwa mumijhi yonjhe.”
Kalata kwa wandhu adamkhulupila Yesu yawo osati Ayahudi
22Ndiipo atumwi ni achogoleli pamojhi ni gulu la wandhu adamkhulupilila Kilisito ku Yelusalamu, adalamula kusangha wachimuna wina kuchokela pagulu ni kuwatuma ku Antiyoki pamojhi ni Poolo ni Banaba. Anyiiwo adaasangha wachimuna awili yawo amalemekezedwa kupunda ni wokhulupilika, Yuda uyo watanidwa Balisaba, ni Sila, 23ndiipo wadaapacha kalata idalembedwa chimwechi,
“Ife atumwi ni achogoleli yawo tamkhulupila Yesu anjanu, tikulonjelani okhulupilila achatu yawo osati Ayahudi muli ku mujhi wa Antiokia ni jhiko la Siliya ni Kilikiya. 24Tavela kuti wandhu wina yawo adachoka mgulu lathu ni kujha kumeneko, adakulagichani, nambho anyiiwo adachita chimwecho popande ife kwaatuma kwanu. 25Chimwecho takhala pamojhi ni kuvomelezana kwaasangha wandhu wina ni kwaatuma kwanu. Anyiiwo siajhe kwanu pamojhi ni wokondedwa wathu Banaba ni Poolo, 26Banaba ni Poolo ali tayali kuchocha umoyo wao ndande ya kwatumikila Ambuye wathu Yesu Kilisito. 27Chimwecho taatuma Yuda ni Sila, anyiiwo siakufotokozeleni yajha tayalemba. 28Chimwecho Mzimu Woyela pamojhi ni ife tavomelezana tisadakupachani vindhu volimba kupita yaya ya phindu, 29msadadya chakudya chilichonjhe icho chachochedwa mahoka kwa viboliboli ni msadamwa mwazi, msadya nyama zonyongopoledwa, ni msadachita chigololo. Mkayavela yaya, simuchite bwino kupunda. Zikomu.”
30Yapo atokwalaila athenga ameneo, adapita ku Antiokia, uko adasonghana ni gulu lonjhe la wandhu yawo adamkhulupilila Yesu, ndiipo adaapacha ijha kalata. 31Wandhu yapo adamaliza kusoma kalata ijha, adakondwa kupunda ndande uthenga ujha udathila mtima. 32Yuda ni Sila, pakuti achinawenewake adali alosi, adakamba mau yambili ya kwachita akhale nganganga ni kwaathila mtima wajha adakhulupilila. 33Yapo adakhala masiku fulani kumeneko ku Antiokia, wokhulupilila wadalaila Yuda ni Sila kuti achoke kwa mtendele ni kubwela kwa wajha adatuma. 34Nambho Sila wadayendekela kukhala kumwekujha.
35Poolo ni Banaba adakhala ku Antiyoki kwa ndhawi yaitali, uko anyiiwo pamojhi ni wandhu wina adayaluza ni kulalikila Uthenga Wabwino wa Ambuye.
Poolo ni Banaba apatulana
36Pambuyo pa masiku yochepa, Poolo wadamkambila Banaba, “Tibwelele tikaapenye achabale wathu mmijhi yonjhe umo tidalalikila mawu la Ambuye kuti tikaone umo ayendekela.” 37Banaba wamafuna kumtenganjho Yohana uyo watanidwa Maluko kuti apite pamojhi ni iye. 38Nambho Poolo wadaona kuti osati bwino kumtenga Maluko ndande wadaasiyapo yapo adali ku Pamfiliya, siwadafune kuyendekela kuchita njhito na anyiiwo. 39Kudachokela mkangano waukulu pakatipao, chimwecho adagawanika. Banaba wadamtenga Maluko, adakwela sitima ni kupita ku Kipulo, 40Poolo wadamsangha Sila. Wajha adamkhulupilila Yesu pamalo pajha adampembhela kuti wapachidwe ubwino ni Ambuye, ndiipo adachoka. 41Iye wadapita pakati pa Siliya ni Kilikiya, uku ni waathila mtima gulu la wandhu amkhulupilila kilisito amalo ya meneyo.

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Vichito 15: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល