Alom 5
5
Mate ya kuvomelezeka ni Mnungu
1Pakuti Mnungu watichita kukhala oyela kwa kumkhulupilila iye, chipano tili ni mtendele nawo, kwa njila ya Yesu Kilisito. 2Kwa kumkhulupilila Yesu, iye watipacha ubwino wake. Mbaka chipano tiendekela kukhala mu ubwino umeneo. Chipano tikondwela kupunda ndande ya chikhulupi chathu sitikhale pamojhi muulemelelo wa Mnungu. 3Osati yameneyope nambho tikondwela mavuto uku ni tijhiwa kuti mavuto yapeleka kulimba mtima pa kumkhulupilila Yesu, 4ni kulimba mtima pa kumkhulupilila Yesu kupeleka kuchimikiza kwa mtima ni kuchimikiza kwa mtima kupeleka kukhulupilila. 5Chikhulupi chimenecho sichitiphecha mtima, ndande Mnungu wathothila chikondi chake mmitima mwathu kwa njila ya mzimu woyela iyo wadatipacha.
6Pakuti Kilisito wadajha ni wadatifela ife tidali ni machimo, yapo tidali tikali sitijhikoza kujhiombola tachinawefe kwandhawi yokwana. 7Pakuti sikhozekana mundhu kumwalila ndande ya mundhu wa ubwino, nambho mundhu wakhoza kujhichocha kumwalila ndande ya mundhu wabwino. 8Nambho Mnungu wachimikiza kuti watikonda, pakuti yapo tidali tikali amachimo, kilisito wadafa ndande yathu. 9Pakuti saino tavomelezeka ni Mnungu kwa mwazi wa kilisito, chimwecho sitiomboledwe kuchokela mmbwayi yaikulu ya Mnungu! 10Yapo tidali tikali adani a Mnungu, Mnungu wadachita ubwenji ni ife kwa njila ya nyifa ya mwana wake. Ndande chipano takhala abwenji wa Amnungu, ndiipo tikhoza kupheza uzene kuti Atate siatiombole kuchokela ku mbhwayi yake, pakuti Yesu ni umoyo masiku yonjhe. 11Osati yameneyope, nambho tikondwela mkati mwa Amnungu kwa njila ya Ambuye wathu Yesu Kilisito, uyo wativanichana ni Mnungu.
Adamu ni Kilisito
12Chipano ngati mujha chimo lidalowa pajhiko kwa kupitila mundhu mmojhi, nalo lidapeleka nyifa. Chimwecho nyifa yaenela kwa wandhu wonjhe, pakuti wonjhe achita machimo. 13Mnungu yapo wadali wakali osampacha Musa Thauko lake, machimo yadalipo pajhiko, nambho Mnungu siwadawelengele wandhu kuti ali ni machimo, ndande padalibe Thauko ilo limafunika kulichata. 14Nambho kuyambila ndhawi ya Adamu mbaka ndhawi ya Musa, nyifa yalamulila wandhu wonjhe, ata wajha sadachite machimo ngati umo wadachitila Adamu,
Adamu wadali chifani cha Kiliisto uyo wadajha pambuyo.
15Nambho kulakwa kwa Adamu sikukhoza kulinganichidwa ni ubwino wa Mnungu. Mate ingakale machimo ya Mundhu Mmojhi yadapeleka nyifa kwa wonjhe. Kwa mundhu mmojhi, yaani Adamu, idakhala ndande ya nyifa kwa wandhu ambili kuchokana ni machimo yake. Nambho kwa ubwino wa mundhu mmojhi, mate yake Yesu, iye waapacha wandhu ubwino wa kuomboledwa machimo yawo. 16Tuli ni ofauti yaikulu pakati pa mbhaso ya Mnungu ni machimo ya mundhu yujha mmojhi. Pakuti pambuyo pa kulakwa kwa mundhu mmojhi, Mnungu wadaalamula kwa kwaapacha chilango, nambho pambuyo pa kulakwa kwa wandhu ambili, Mnungu wadapacha mbhaso kwa kwaalekelela. 17Zenedi kwa machimo ya mundhu mmojhi, nyifa ya muyaya idayamba kulamulila wandhu wonjhe, nambho ijhiwika kuti chijha wadachichita mundhu mmojhi, Yani Yesu kilisito, ni chabwino kupunda. Nambho yawo alandila ubwino ni mbhaso yaikulu kuchokela kwa Mnungu, ni kuvomelezedwa ni Mnungu, siakhoze pakuti sikhale ni umoyo wa muyaya kwa njila ya mundhu mmojhi, mate yake, Yesu kilisito.
18Chipano, ngati kulakwa kwa mundhu mmojhi kudatipelekela lamulo kwa wandhu wonjhe, chimwecho chichito chabwino cha mundhu mmojhi chaapacha wonjhe kuvomelezeka pachogolo pa Amnungu ni umoyo. 19Ni ngati kusiya kusavela kwa mundhu mmojhi, wandhu ambili adachitidwa amachimo, chinchijha kuvela kwa mundhu mmojhi sikwaachitee wandhu ambili kuvomelezeka ni Mnungu.
20Thauko yapo lidachokela, lidapelekela kuchuluka kwa voipa, nambho machimo yapo yadachuluka, ubwino udapunda kuchuluka. 21Ngati umo machimo umo yadali ni mbhavu ya kwapelekela wandhu, chimchijha ubwino wachita wandhu avomelezeke ni Mnungu kwa kwapeleka umoyo wa muyaya kwa njila ya Yesu kilisito, Mbuye wathu.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Alom 5: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.