Pakuti Mnungu watichita kukhala oyela kwa kumkhulupilila iye, chipano tili ni mtendele nawo, kwa njila ya Yesu Kilisito. Kwa kumkhulupilila Yesu, iye watipacha ubwino wake. Mbaka chipano tiendekela kukhala mu ubwino umeneo. Chipano tikondwela kupunda ndande ya chikhulupi chathu sitikhale pamojhi muulemelelo wa Mnungu.