Luka 17
17
Mayaluzo ya machimo ni kulekeleledwa
Matayo 18:6-7,21-22; Maluko 9:42
1Yesu wadakambila woyaluzidwa wake, “Vindhu ivo vimchiticha mundhu kuchita machimo sivichelezedwa. Nambho siwavutike mundhu yujha siwamchitiche mundhu wachite machimo. 2Idakali bwino mundhu mmeneyo wadakamangidwa mbhelo yopelela mkhosi mwake ni kuponyedwa pakati panyanja, kusiyana ni kumchiticha mundhu mmojhi wakhulupilila wachite chimo. 3Chimwecho jhipenyeleleni! Ngati mbale wako wakhulupilila wakachita machimo, mnyindile ni ngati walapa, mlekelele. 4Ata ngati wakachimwa mala saba pa siku limohji nikujha kwako mala saba, wakakamba, ‘Nalapa,’ umlekelele.”
Chikhulupi
5Oyaluzidwa wake adamkambila Yesu, “Mtionjezele chikhulupi.” 6Yesu wadayangha, “Mdakakhala ni chikhulupi chaching'ono ngati mbeu ya haladali, mdakakhoza kuukambila mtengo wa mkuuyuwu, ‘Zuka upite ukamele mnyanja,’ ni iwo udakakuvelani.”
Njhito ya mtumiki
7Yesu wadakamba, “Ngati mmojhi wanu wali ni mbowa uyo walima kapina kudyecha mbelele. Bwanji, mbowayo yapo wabwela kuchoka kumunda, wopata yujha wamkambila mbowa wake wajhe chisanga kudya chakudya? 8Bwanji, mmalo mwake siwamkambila, ‘Nikonjele chakudya nidye, ukonjeke kuti unitumikile yapo nikudya ni kumwa. Ndiipo pambuyo pake ukhoza kudya ni kumwa.’ 9Bwanji, mundhu mmeneyo siwamuyamika mbowa mmeneyo ndande wachita chijha wadalamulidwa wachite? 10Chimwecho, namwenjho mkathochita yonjhe yayo mulamulidwa, kambani, ‘Ife ni mbowa yawo tilibe phindu, tayachitape yayo talamulidwa kuchita.’ ”
Yesu walamicha amakate khumi
11Yesu ni oyaluzidwa wake yapo wadali paulendo wopita ku Yelusalemu, wapitila malile ya Samaliya ni Galilaya. 12Yapo wamapita mu chijhijhi chimojhi, wadakomana ni wandhu khumi adamjhela Yesu ni adaima patali. 13Adakweza mvekelo, “Ambuye Yesu, tilengeleni lisungu!” 14Yesu yapo wadaaona amakate wajha, wadaakambila, “Pitani mkajhilangize kwa ajhukulu.” Yapo adali akali mnjila, adalama utenda ni kuvomelezeka kwa chikhalidwe cha kumlambila Mnungu. 15Mmojhi wao yapo wadaona kuti walama, wadabwelela kwa Yesu uku niwamtamanda Mnungu kwa mvekelo waukulu. 16Wadagwa chifufumimba mmiyendo ya Yesu ni kumuyamika. Mundhu mmeneyo wadali Msamaliya. 17Yesu wadamfunjha, “Bwanji, osati wandhu khumi yao adalamichidwa ni kuvomelezeka kwa chikhalidwe cha kumlimbila Mnungu? Bwanji, anyiwajha tisa alikuti? 18Bwanji, padalibe ata mmojhi uyo wadabwela kumpacha ulemu Mnungu, nambho uyu mlendope?” 19Ndiipo Yesu wadamkambila mundhu yujha, “Ima ujhipita, chikhulupililo chako chakulamicha.”
Kujha kwa ufumu wa Mnungu
Matayo 24:23-28,37-41
20Siku limojhi Afalisayo adamfunjha Yesu kuti Ufumu wa Mnungu ukujha chakanji, iye wadayangha, “Ufumu wakumwamba siukujha kwa kuuona kwa maso. 21Chimwecho, palibe mundhu uyo siwakhoze kukamba, ‘Uliyapa,’ kapina, ‘Uwo uliyapo.’ Pakuti Ufumu wa Mnungu uli mkati mwanu.”
22Ndiipo wadaakambila oyaluzidwa wake, “Masiku yatokujha yapo simukhumbile kuliona siku limojhi la masiku ya ine Mwana wa Mundhu, nambho simuliona. 23Wandhu saakukambileni, ‘Uyo uko,’ kapina, ‘Uyu yapa!’ Nambho, msadaakhulupilila. 24Pakuti siku limenelo, ine Mwana wa Mundhu sinionekele ngati dangalila umo liwalila kumwamba, kuyambila mathelo imojhi mbaka injake. 25Poyamba ine Mwana wa Mundhu, nifunika niyambe kuvutika kupunda ni kukanidwa ni wandhu ambadwa uno.”
26“Ngati umo idali pa masiku ya Nuhu, nde umo siikhalile pa masiku ya kujha kwa ine Mwana wa Mundhu. 27Pa masiku ya Nuhu, wandhu amadya ni kumwa, amakwata ni kukwatiwa mbaka siku lijha yapo Nuhu wadalowa mu chombo, kufulikila yapo mafuliko ya vula yayikulu yadachokela ni kuwapha wandhu ni vindhu vonjhe. 28Idali chimwecho pa masiku ya Lutu. Wandhu amadya ni kumwa, amagula ni kugulicha, amalima ni kumanga nyumba. 29Nambho siku limenelo Lutu yapo wadachoka ku Sodoma, udagwa moto wa chibeliti kuchokela kumwamba udamwazika ngati vula, ni kwaapha wonjhe. 30Umu ndeumo siikhalile kwa ine Mwana wa Mundhu yapo sinichokele.”
31Wadaendekela kukamba, “Siku limenelo, mundhu uyo siwakhale pa chindu la nyumba siwadachika kutenga vindhu vake ivo wadavisiya mkati mwa nyumba. Chimwechonjho mundhu uyo wali kumunda siwadabwelela kukhomo kutenga chilichonjhe. 32Kumbukilani vindhu vidampata mkazake wa Lutu! 33Mundhu waliyonjhe uyo wafuna kuupulumucha umoyo wake siwautaye, ni mundhu waliyonjhe uyo siwautaye umoyo wake, siwauombole. 34Nikukambilani chemwechi, usiku umeneo wandhu awili saagone pamojhi pachithanda, nambho mmojhi siwatengedwe ni mnjake siwalekedwe. 35Wachikazi awili saakhale pamojhi kupela chakudya pa mbhelo, nambho mmojhi siwatengedwe ni mnjake siwalekedwe. 36Wandhu awili saakhale pamojhi kulima munda, mmojhi siwatengedwe, ni mnjake siwalekedwe.”
37Pamenpo woyaluzidwa adamfunjha, “Ambuye, kuti uko siyachitike yaya?”
Wadayangha, “Yapo pali chitanda, ndeyapo sizisonghane nghwazi.”
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Luka 17: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: