Luka 16
16
Chifani cha woimilila wanjelu
1Yesu wadakambila oyaluzidwa wake, “Padali mundhu mmojhi wopata uyo wadali ni woimilila chuma chake. Wopatayo wadavela kuti woimilila yujha wawananga chuma icho wadapachidwa kuimilila. 2Siku limojhi wopata yujha wadamtana woimilia wadamfunjha, ‘Bwanji, nghani zanji izi nizivela kuusu iwe? Nichulile vindhu ivo nakupacha uviimilile, ndande siukhalanjho woimilila wa chuma changa.’ 3Woimilila yujha wadaganizila wadakamba, ‘Wopata wanga anitopola njhito yoimilila chuma chao, chipano sinichite chiyani? Nilibe mbhavu zolimila, ni kupembhapembha niona njhoni. 4Chipano! Najhiwa icho sinichite, kuti yapo wopata wanga sanitopole njhito yoimilila chuma chao, wandhu akhoze kunilandila mmakomo mwao.’ 5Ndiipo wadaatana mmojhimmojhi wa angongole wa wopata wake. Wadamfunjha woyamba, ‘Nichulile, uli ni ngongole kiasi chanji cha mafuta kwa wopata wanga?’ 6Ndiipo wadamuyangha, ‘Nidaidwa madumu 185 ya mafuta ya zeituni.’ Woimilila yujha wadamkambila, ‘Tenga hati ya ngongole yako ni ulembele madumu tisini ni yawili.’ 7Ndiipo wadamfunjha wakawili, ‘Ni iwe uli ni ngongole yokwana bwanji?’ Iye wadayangha, ‘Nidaidwa maguniya miya ziwili za ufa wa ngano.’ Woyimilila yujha wadamkambila, ‘Lemba udaidwa maguniya miya mbili sitini.’ 8Nambho wopata wake yujha wadamuelekela woyimilila wosakhulupilika ndande wadali ni njelu kupunda, ndande wandhu ajhiko lino lapanjhi ni wochenjela kupunda, nambho wandhu yawo amchata Mnungu osati anjelu ngati anyiiwo.”
9Yesu wadaendekela kwakambila, “Nanenjho nikukambilani, chitumileni chuma cha jhiko lino mujhipatile mabwenji kuti chuma chimenecho yapo sichithe mkhoze kulandilidwa ni Mnungu ku umoyo wa muyaya.”
10Waliyonjhe uyo wakhoza kukhulupika pavindhu vochepa kupunda, siwakhoze kukhulupilika kwa vindhu vavikulu. Waliyonjhe uyo siwakhulupika pa vindhu vochepa siwakhulipilika pa vindhu vavikulu. 11Chimwecho, ngati siudakhale okhulupilika pakutumila chuma chapajhiko lapanjhi, yani uyo siwakukhulupilileni kukupachani chuma cha uzimu? 12Ni ngati simukhulupilka pachuma cha mundhu wina, yani uyo siwakupacheni chuma icho chili chanu mwachiwene wake?
13Palibe kapolo uyo wakhoza kutumikila wakulu awili kwa ndhawi imojhi. Pakuti siwamuipile mmojhi wao ni kumkonda mnjake, kapina siwagwilizane ni mmojhi ni kumdelela mnjake. Chemwecho, simngakhoze kumtumikila Mnungu ni ndalama vonjhe pamojhi.
Mayaluzo ina ya Yesu
Matayo 11:12-13; 5:31-32; Maluko 10:11-12
14Nambho Afalisayo yawo amakonda ndalama yapo adayavela yameneyo, adamseka Yesu kwa kumdelela. 15Yesu wadayangha, “Anyiimwe mujhichita kuti woongoka pamaso pa wandhu, nambho Mnungu waijhiwa mitima yanu. Pakuti chindhu icho wandhu achiona kuti chaphindu, kwa Mnungu ni chokwiicha.”
16“Thauko la Musa ni mayaluzo ya alosi, yamalalikidwa mbaka yapo wadafika Yohana mbatizi. Kuyambila ndhawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mnungu ulalikidwa, ni kila mmojhi walowamo kwa mbhavu mu ufumu umeneo. 17Nilahisi jhiko lapanjhi ni kumwamba kupita, kusiyana ata lembo limojhi kuchokapo muthauko la Musa.”
18Waliyonjhe uyo wamsiya mkazake ni kukwata wamkazi mwina, wachita chogololo. Ni wammuna uyo wamkwata wamkazi uyo wasiyidwa ni mmunake, wachitanayo chigololo.
Mundhu wopata ni Lazalo
19“Padali mundhu mmojhi wopata uyo wamavala njhalu zokhadwa zamtengo wapamwamba, uyo wamakhala kwa anasa masiku yonjhe. 20Pachicheko chake padali wosauka mmojhi, jina lake Lazalo, uyo wadajhala vilonda thupi lambhumbhu. 21Lazalo wamakhumbila kudya vakudya vokhalila ivo vimagwa panjhi pa meza ya mundhu wopatayo. Ata agalu amajha kumnyambita vilonda vake. 22Pambuyo wosauka Lazalo wadamwalila, atamuki akumwamba Amnungu adamtenga ni kumuika wakhale pamojhi ni Ibulahimu. Mundhu wopata yujha nayonjho wadamwalila ni wadaikidwa mmanda. 23Mundhu wopata yapo wadali mmavuto yayakulu kugahena, wadapenya, wadamuona Ibulahimu kwapatali, ni pafupi pake wadalipo Lazalo. 24Chimwecho, mundhu wopatayo wadamtana Ibulahimu, ‘Atate Ibulahimu, nilengeleni lisungu, mumtume Lazalo wabize chala chake mmajhi kuti wajhe kuzizilicha lilime langa, chifuko nipata mavuto kupunda kuno ku Gahena.’ 25Nambho Ibulahimu wadamuyangha, ‘Mwana wanga, kumbukila yapo udali wamoyo pajhiko udathopata vindhu vabwino ivo udavikhumbila, ni Lazalo wadapata mavuto. Nambho chipano, Lazalo wathilidwa mtima, ni iwe uvutika. 26Ata chimwecho, pakati panu ni ife pali jhenje lalikulu, kuti yawo afuna kuchoka kuno kujha kumeneko sadakhoza, kapina yawo afuna kuchoka kumeneko kujha kuno kwathu alepele.’ 27Ndiipo wopatayo wadampembha kupunda, ‘Basi nikupembhani atate wanga a Ibulahimu, mumtume Lazalo wapite kukhomo kwa achabale wanga. 28Nili ni achabale asano kumeneko, wapite wakaonye kuti naonjho sadafika kumalo yano ya mavuto.’ 29Nambho Ibulahimu wadamuyangha, ‘Achabale wako ali ni mathauko ya Musa ni malembo ya alosi, asiye ayavechele yameneyo.’ 30Nambho wopatayo wadakambanjho, ‘Atate wanga a Ibulahimu, ngati mundhu wakachoka kuno nikwapitila, salape machimo yawo.’ 31Ndiipo Ibulahimu wadamuyangha, ‘Ngati sayavela mathauko ya Musa pamojhi ni malembo ya alosi, sangakhoze kuvela ata ngati wakapitila mmojhi uyo wahyuka kuchokela kwa akufa.’”
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Luka 16: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: