Yohana 9
9
Yesu wamlamicha mundhu uyo wabadwa osapenya
1Siku limojhi Yesu yapo wamapita wadamuona mundhu mmojhi, uyo siwapenya kuyambila kubadwa kwake. 2Basi oyaluzidwa wake adamfunjha, “Oyaluza! Yani wachita machimo, mundhu uyu kapina obala wake, mbaka wabadwe osapenye?”
3Yesu wadaayangha, “Wabadwa osapenye osati ndande ya machimo yake, kapina ya obala wake, wadabadwa chimwecho kuti mbhavu ya Amnungu iwoneke muumoyo wake. 4Ifunika tiendekele kuzichita njhito za yawo atituma kukali usana, ndande usiku ukujha uwo mundhu waliyonjhe siwakhoza kuchita njhito. 5Ndhawi nili pano pajhiko, ine nde dangalila la wandhu a pajhiko.”
6Yapo wadakamba chimwecho, wadalavula malovu panjhi, wadakonja thokope, wadamnyeka yujha osapenyeyo mmaso, 7wadamkambila, “Pita ukasambe kuthiwi la Siloamu.” Mawu Siloamu mate yake Uyo watumidwa. Chimwecho wadapita kusamba, wadabwela uku ni wapenya.
8Ndiipo, apafupi wake ni wina yao amajhiwa kuti poyamba wadali osauka pembhapembha, adakamba, “Uyu osati osauka yujha wamakhala ni kupembha?”
9Wina adakamba, “Ndemwene.” Wina adakambanjho, “Notho! Wangolingana nayo.”
Nambho yujha wadali osapenyayo wadakamba, “Nde ine!”
10Basi amamfunjha, “Chipano, maso yako yakhoza bwanji kupenya?”
11Wadayangha, “Yujha mundu watanidwa Yesu wadakonja thokope, wadaninyeka mmaso ni kunikambila nipite nikasambe ku thiwi la Siloamu. Pamenepo ine nidapita kusamba kumaso, pampajha nidakhoza kupenya.”
12Adamfunjha, “Iye walikuti?” Nayo wadaayangha,
“Ine sinijhiwa!”
Afalisayo afuana kujhiwa umo wadalamichidwa osapenya
13Ndiipo adampeleka yujha mundhu wadali sapenya kwa Afalisayo. 14Siku ilo Yesu wadamlamicha yujha sapenya lidali Siku lo Pumulila. 15Ndiipo Afalisayo adayamba kumfunjha mundhu mmeneyo, “Wakhoza bwanji kupenya?”
Niiye wadaakambila, “Wadaninyeka thokope mmaso, ni ine nidasamba ni saino nipenya”
16Afalisayo wina adakamba, “Mundhu uyu siwachoka kwa Amnungu ndande siwagwila Thauko la Siku Lopumulila.”
Nambho wina adakamba, “Mundhu wamachimo wakhoza bwanji kuchita vizindikilo ngati ivi?” Kudali ni mkangano pakati pao.
17Adamfunjhanjho yujha wadali osapenya, “Iwe nde walamichidwa maso, ukamba bwanji kuusu iye?”
Nayo wadamkambila, “Iye mlosi”
18Achogholeli wa Ayahudi sadakhulupilile kuti mundhu mmeneyo mmayambo wadali osapenya, ni chipano wapenya, mbaka yapo wadaatana obala wake. 19Chimwecho, adaafunjha obala wake, “Bwanji, uyu nde mwana wanu uyo wadabadwa osapenya? Chipano wakhoza bwanji kupenya?”
20Obala wake adayangha, “Tijhiwa kuti nde mwana wathu, ni kuti wadabadwa sapenya. 21Nambho sitijhiwa wakhoza bwanji kupenya, kapina uyo wamphenula maso. Mfunjheni mwene, iye mundhu wa mkulu, siwajhikambilile mwene.”
22Obala wake adakamba chimwecho ndande amaaopa achogholeli wa Ayahudi pakuti adavomelezana kuti waliyonjhe uyo wavomela Yesu kuti nde kilisito siwachekelezedwe kulambila mnyumba yo komanilana Ayahudi. 23Nde ndande obala wake adakamba kuti, “Amfunjhe mwene, iye ni mundhu wa mkulu.”
24Ndiipo, adamtananjho uyo wadali osapenya, adamkambila, “Apache Amnungu ulemelelo! Ife tijhiwa uyu ni mundhu wa machimo.”
25Iye wadaayangha, “Ngati wali ni machimo ine sinijhiwa. Icho nijhiwa ine nidali sapenya, chipano ni penya.”
26Ndiipo adamfunjha, “Wadakuchitila chiyani? Wadakuphenula bwanji masao yako?”
27Mundhu mmeneyo wadayangha, “Nakukambilani, simufuna kunivela, bwanji mufuna kuvelanjho? Namwe mufuna kukhala ochatila wake?”
28Nambho adamtukwana kokamba, “Iwe nde oyaluzidwa wake, ife oyaluzidwa Amusa. 29Ife tijhiwa kuti Amnungu adakamba ni Musa, nambho sitijhiwa mundhu uyu wachokela kuti!”
30Nayo wadaayangha, “Chindhu ichi ni chozwizwicha! Anyiimwe simujhiwa uko wachoka, nambho waniphenula maso yanga! 31Tijhiwa kuti Amnungu saavechela wandhu a machimo, nambho amvechela waliyonjhe uyo waalambila ni kuchita yayo ayafuna iwo. 32Kuyambila mmayambo mwa jhiko sikudavekelepo paliponjhe kuti kuli mundhu wamlamicha mundhu uyo wabadwa sapenya kupenya. 33Ngati mundhu uyu siwadachoke kwa Amnungu, sawadakakhoza kuchita chilichonjhe.”
34Adamuyangha, “Iwe wabadwa uli ni machimo, ukhoza bwanji kutiyaluza ife?” Ndiipo adamtopola mnyumba ya komanilana Ayahudi.
Afalisayo alepela kuujhiwa uzene
35Yesu yapo wadavela kuti adathomtopola mnyumba yo pezanilana Ayahudi, wadamfunjha, “Iwe umkhulupilila Mwana wa Mundhu?”
36Mundhu yujha wadayangha, “Waakulu mnikambile iye niyani, nifuna kumkhulupila.”
37Yesu wadamkambila, “Wathomuona, nayo ndeuyo wakamba niiwe chipano.”
38Ndiipo mundhu yujha wadakamba, “Nikhulupilila Ambuye!” Chimwecho wadamgwadila ni kimlambila.
39Yesu wadakamba, “Najha pajhiko kuchocha lamulo, kuti anyiyao sapenya apenye, ni anyiyao apenya akhale osapenya.”
40Afalisayo wina anyiyao adali pafupi nao adavela mawu yameneyo, adamfunjha, “Bwanji ife nafe achisapenya?”
41Yesu wadayangha, “Ngati mudakalidi achisapenya, simdakali ni machimo, nambho chipano pakuti mkamba kuti, ‘Ife tipenya,’ imeneyo ilangiza kuti muli ni volakwa.”
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Yohana 9: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.