Yohana 3

3
Yesu ni Nikodemo
1Wadalipo mchogholeli mmojhi wa Chiyahudi, wa ghulu la Afalisayo, jhina lake Nikodemo. 2Siku limojhi usiku Nikodemo wadamchata Yesu, wadamkambila, “Oyaluza, tijhiwa kuti imwe oyaluza yao mwatumidwa ni Amnungu, pakuti palibe mundhu uyo wakhoza kuchita vizindikilo ngati ivo muchita popande Amnungu kukhala pamojhi naye.”
3Yesu wadamuyangha, “Uzene nikukambila, mundhu ngati siwabadwa kakawili siwakhoza kuuona Ufumu wa Amnungu.”
4Ndiipo Nikodemo wadamfunjha, “Mzee wakhoza bwanji kubadwanjho? Siwakhoze bwanji kulowa mmimba mwa amaye wake nikubaadwanjho?”
5Yesu wadayangha, “Uzene nikukambila, mundhu ngati siwabadwa kwa majhi ni Mzimu, siwakhoza kulowa mu Ufumu wa Amnungu 6Mundhu wabadwa chithupi kwa atate wake ni amake, nambho wabadwa Chizimu kwa Mzimu woyela. 7Siudadabwa pakuti nakukambila kuti lazima kubadwanjho. 8Mbhepo iputa ni kupita uko ifuna, uvela mvekelo wake, nambho siujhiwa uko ichoka kapina uko ipita. Nde umo ili kwa mundhu uyo wabadwa kwa Mzimu woyela.”
9Nikodemo wadafunjha, “Siikhozeke bwanji vindhu ivi?”
10Yesu wadayangha, “Bwanji, iwe ni oyaluza olemekezedwa Izilaeli, ata chimwecho siuvijhiwa vindhu ivi? 11Uzene nikukambila, ife tikamba yayo tiyajhiwa, ni tifotokozelela vindhu ivo taviona, nambho mau yathu simuyavomela. 12Ngati nakukambilani vindhu va pajhiko la panjhi, namwe simudakhulupilile, simukhulupilile bwanji nikakukambilani vindhu va kumwamba? 13Palibe mundhu uyo wadapitapo kumwamba, nambho Mwana wa Mundhu uyo wadachika kuchokela ku mwamba.”
14Ngati Musa umo wadaipachikila njoka pamtengo kujha ku phululu, nde umo Mwana wa Mundhu nayo wafunika kupachikidwa, 15kuti kila uyo wamkhulupilila wakhale ni umoyo wa muyaya. 16Mateyake Amnungu adaakonda wandhu a jhiko la panjhi ni kumchocha Mwana wao wa yokha, kuti kila uyo wamkhulupilila siwadatayika, nambho wakhale ni umoyo muyaya. 17Mate yake Amnungu siwadamtume Mwana wake kuti walamule wandhu a pajhiko la panjhi, nambho waombole kupitila mwana wao.
18“Uyo wamkhulupilila iye siwa lamulidwa, uyo siwamkhulupilila watho lamulidwa, ndande yosamkhulupilila Mwana wa yokha wa Amnungu. 19Lamulo lene nde ili, dangalila wajha pajhiko la panjhi, nambho wandhu akonda mdima kusiyana dangalila, ndande vochitika vao ni voipa. 20Waliyonjhe uyo wachita voipa waliipila dangalila, siwakhoza kujha kudangalila, pakuti siwafuna vindhu vake vijhiwike. 21Nambho yawo achita uzene akujha kudangalila, kuti vichito vao vionekele padanga kuti yachitika kwa kwaavela Amnungu.”
Yohana Mbatizi wakamba nghani za Yesu
22Pambuyo pa yameneyo, Yesu wadapita ku Yudea pamojhi ni oyaluzidwa wake. Wadalongeza nao kumeneko, niwabatiza wandhu. 23Yohana nayo wamato kwa batiza wandhu kumeneko ku Ainoni, pafupi ni ku Salimu, pakuti kumeneko ndeuko kudali ni majhi yambili. Wandhu amapita kumeneko ni kubatizidwa. 24Ndhawi iyi Yohana wadali wakali osamangidwe mndende.
25Padachokela mtafu pakati pa oyaluzidwa akumojhi a Yohana ni Myahudi mmojhi kuusu chikhalidwe cha kusamba pa kuvomelezeka kumlambila Mnungu. 26Ndiipo, oyaluzidwa achameneo adamchata Yohana, ni kumkambila, “Oyaluza, mundhu yujha wadali pamojhi namwe muchija la mchinje Yolodani yujha mdamchochela umboni, nayo wabatiza ni wandhu onjhe atomchota!”
27Ndiipo, Yohana wadaayangha, “Mundhu siwakhoza kulandila chilichonjhe popande kupachidwa kuchokela kumwamba kwa Amnungu. 28Mwachinawene mkhoza kunichochela umboni kuti nidakamba, ‘Ine osati Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu, nambho natumidwa kuti ni mchogholele!’ 29Wammuna wa ukwati nde uyo wamkwata mwali wa ukwati. Nambho bwenji wa uyo wakwata uyo waima pafupi naye ni kumvechela, wakondwa kupunda yapo wavela mvekelo wake. Iyi nde Ndande ya kukwanila kwa chimwemwe nchanga 30Kilisto uyo wasanghidwa ni Amnungu ifunika walemekezedwe kupunda, ine nichike.”
Uyo wakujha kuchoka kumwamba
31Uyo wasanghidwa ni Amnungu kuchokela kumwamba ni wamkulu kupitilila vonjhe, uyo wachokela pajhiko la panjhi ni wapajhiko la panjhi, niwakamba vindhu va pajhiko la panjhi. Nambho uyo wachokela kumwamba ni wamkulu kupitilila vonjhe. 32Iye wakamba yajha wayaona ni kuyavela, nambho palibe mundhu uyo wavomela umboni wake. 33Nambho mundhu walionjhe uyo wavomela uthenga wake, wachimikiza kuti Amnungu ni azene. 34Uyo watumidwa ni Amnungu wakamba mawu ya Amnungu, mate yake Amnungu ampacha mundhu mmeneyo Mzimu wao popande chipimo. 35Atate amkonda Mwana ni amningha vindhu vonjhe. 36Uyo wamkhulupilila Mwana wa Amnungu wali ni umoyo wa muyaya, uyo siwamvela Mwana siwakhala ni umoyo wa muyaya, nambho siwakhale mumkwiyo wa Amnungu.

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Yohana 3: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល