Yohana 4
4
Yesu ni wamkazi Msamaliya
1Afalisayo adavela kuti Yesu wamaachita wandhu ambili kukhala woyaluzidwa wake ni kwaabatiza kusiyana ni Yohana, 2ata ngati uzene Yesu siwamabatize wandhu iye mwenewake, nambho oyaluzidwa wake nde anyiyawo amabatiza. 3Chimwecho, Yesu yapo wadavela yameneyo, wadachoka ku Yudea kubwela ku jhiko la Galilaya, 4muulendo wake idafunika wapitile ku Samaliya.
5Ndiipo, wadafika ku Sikali, mujhi uwo upezeka Msamaliya, pafupi ni munda ujha Yakobo wadampacha mwana wake uyo wamatanidwa Yusufu. 6Ndeuko kudali ni chithime cha Yakobo, idali saa sita za usana, nayo Yesu kuchokana ni kulema kwa ulendo, wadapumulila mbhepete mwa chitime.
7Ndiipo, wamkazi mmojhi kuchokela ku Samaliya wadajha pamenepo kutunga majhi. Yesu wadamkambila, “Nipache majhi nimwe.” 8Ndhawi imeneyo oyaluzidwa wake adapita kumujhi kughula chakudya.
9Wamkazi mmeneyo wadayangha Yesu, “Iwe Muyahudi, ine Msamaliya! Unipembha bwanji majhi?” Wadayangha chimwecho ndande Ayahudi adalibe mgwilizano ni Asamaliya motumikila vindhu.
10Yesu wadamuyangha, “Ngati udakajhiwa mbhaso ya Mnungu iye ni yani uyo wakukambila umpache majhi wamwe, udakampembha iye, nayo wadakakupacha majhi yayo siyakuchite ukhale moyo wa muyaya.”
11Wamkazi yujha wadayaangha, “Ambuye, imwe mulijhe msomelo, ni chithime chachitali, siupate kuti majhi ya umoyo wa muyaya? 12Bwanji, iwe wamkulu kupunda kusiyana ni Ambuye watu Yakobo, uyo wadatipacha chithime ichi? Iye mwene wake ni wana wake ni viweto vake adamwa majhi kuchokela mchitime ichi.”
13Yesu wadayangha, “Waliyonjhe uyo siwamwe majhi yaya siwaonenjho lujho. 14Nambho uyo siwamwe majhi yayo sinimpache, siwaona lujho muyaya. Majhi yayo sini mpache mkati mwake simukhale viwila va majhi ya umoyo ni kumpacha umoyo wa muyaya.”
15Wamkazi mmeneyo wadakamba, “Ambuye, nipacheni majhi yameneyo sinidaonanjho lujho, ni sinidajhanjho pano kutunga majhi.”
16Yesu wadamkambila, “Mapita ukamtane mmunako ujhe nayo pano.”
17Yujha wamkazi wadakamba, “Nilibe wa mmuna.”
Yesu wadamkambila, “Yapo wakamba kuti ulibe wa mmuna wakamba uzene.” 18Ndande udakwatiwa ni wachimuna asano, ni uyo ukhala nayo chipano osati mmunako. Wakamba uzene.
19Wamkazi yujha wadakamba “Atate, niona kuti imwe amlosi. 20Azee wathu Asamaliya adaalambila Amnungu pa phili lino, nambho anyiimwe Ayahudi mukamba kuti tikalambile ku Yelusalemu.”
21Yesu wadamkambila, “Iwe maye nikhulupilile, ndhawi siijhe iyo simwalambila Atate wanu pa phili lino, kapina Kuyelusalemu. 22Anyiimwe Asamaliya mlambila icho simuchijhiwa, nambho ife taajhiwa Amnungu yawo taalambila, ndande uomboli wachokela kwa Ayahudi. 23Ndhawi ikujha, ni chipano ilipo, wandhu azene yapo samlambile Mnungu kwa kuchogozedwa ni Mzimu ni zene. Amnungu waafuna anyiyao alambila mtundu uwu. 24Amnungu ni Mzimu, ni wonjhe amlambila afunika kumlambila muchizimu ni zene.”
25Wamkazi mmeyo wadamkambila, “Nijhiwa kuti Mesiya, uyo watanidwa Kilisito, wakujha. Yapo siwajhe siwatijhiwiche kila kandhu.”
26Ndiipo Yesu wadamkambila, “Ine nikamba nawe nde mmeneyo.”
27Ndhawi imweyo oyaluzidwa wake adabwela, adadabwa kupunda yapo adampheza Yesu niwakambana ni wamkazi. Nambho palibe uyo wadamkambila wamkazi, “Ufuna chiyani?” Kapina kumfunjha Yesu, “Ndande yanji ukambana ni wamkazi?”
28Ndiipo wamkazi yujha wadausia mchuko wake pamwepo, ni kupita kumujhi kwaakambila wandhu, 29“Majhani mkamuone mundhu uyo wanikambila vindhu vonjhe ivo nachita! Bwanji, ikhozekana kuti iye nde Kilisito?” 30Chimwecho wandhu adachoka kumujhi, ni kumchata Yesu.
31Ndhawi imweyo oyaluzidwa wake amampembelela Yesu, “Oyaluza, madyani ata pang'onope.”
32Ndiipo Yesu wadaakambila, “Ine nili ni chakudya icho simuchijhiwa.”
33Oyaluzidwa wake adamfunjha, “Bwanji, pali ni mundhu uyo wampelekela chakudya?”
34Yesu wadayangha, “Chakudya changa nde ichi, kuchita icho wafuna uyo wanituma ni kuimaliza njhito yake. 35Anyiimwe mukamba kuti, ‘Yakhalila miyezi inayipe, ndhawi yokolola ikujha!’ Nambho ine nikukambilani, penyani minda vokolola umo vakwimila ndhawi yokolola yakwana! 36Okolola walandila mkokolo kuchokana ni njhito yake, ni wokolola wakusa vokolola ndande ya umoyo wa muyaya, chimwecho uyo wavyala ni uyo wakolola sakondwele pamojhi. 37Chimwecho mkambo uwo ukamba, ‘Mmojhi wavyala ni mwina wakolola,’ ni wazene. 38Ine nakutumani mkakolole vokolola ivo simuvipotele njhito, anyiyawo adapota njhito wina, nambho anyiimwe mpata phindu kuchokana kwa mavuto ya njhito zao.”
39Asamalia ambili amujhi ujha, adamkhulupilila Yesu ndande ya umboni wa maye ameneo yapo wadakambila kuti, “Wanikambila vindhu vonjhe ivo nachita.” 40Chimwecho Asamalila adamchota Yesu adampembha wakhale nao, ndiipo wadakhala pamenepo kwa siku ziwili.
41Wandhu ambili kupunda adamkhulupilila Yesu ndande ya uthenga wake, 42adamkambila wamkazi mmeneyo, “Chipano takhulupilila, osati ndande ya mawu yakope, tachinawefe tavela, ni tijhiwa kuti uyu nde muomboli wa jhiko la panjhi.”
Yesu wamlamicha mwana wa wamkulu
43Pambuyo pa masiku yawili Yesu wadachokapo pamenepo ni kupita ku Galilaya, 44pakuti Yesu wadathokamba padanga kuti, “Mlosi siwapheza ulemu mujhiko lake.” 45Ndiipo yapo wadafika ku Galilaya, wandhu aku Galilaya adamlandila, pakuti naonjho adali pwando la Pasaka. Chimwecho adayaona yonjhe yayo wadachita Yesu ku Yelusalemu pa pwando limenelo.
46Chimwecho Yesu wadafikanjho mbaka Kukana ya ku Galilaya, kujha wadang'anamula majhi kukhala divai. Kudalipo mchogoleli mmojhi uyo wadali ni mnyamata wake uyo wamadwala kujha ku Kapelinaumu. 47Chimwecho mchogoleli yujha yapo wadavela kuti Yesu wafika ku Galilaya kuchokela ku Yudea, wadamchota ni kumpembha wakamlamiche mwana wake uyo wamadwala pafupi kumwalila. 48Yesu wadamkambila, “Ukalepela kuona vizindikilo ni vodabwicha siukhulupilila.”
49Mchogoleli mmeneyo wadamkambila, “Waakulu, pepani tiyeni mwana wanga wakali osafe.”
50Ndiipo Yesu wadamkambila, “Mapita pe, mwana wako walama.”
Yujha mundhu wadakhulupilila mawu ya Yesu ni kupita. 51Yapo wadali mnjila wadapezana ni mbowa zake, zidamkambila, “Mwanawako walama!”
52Chimwecho wadafunjha ndhawi iyo mwana wadalama, adamkambila kuti, “Jhulo ndhawi ya saa saba za usana, nde yapo wadalama.” 53Ndiipo atate wake mwanayo adakumbukila kuti, ndhawi idali ijha Yesu wadamkambila, “Mwana wako walama.” Ndiipo iye ni achabale wake onjhe apakhomo lake adakhulupilila.
54Ichi chidali chizindikilo chakawili icho wadachichita Yesu, yapo wamachoka ku Yudea kupita ku Galilaya.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Yohana 4: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: