Vichito 28
28
Vindhu ivo wadavichita Poolo ku chilumba cha Malita
1Yapo tidafika kumtunda popande vuto, ndiipo tidajhiwa kuti jhina la chilumba chijha ni Malita. 2Wandhu yawo amakhala pa chilumba chijha adali abwino kupunda kwathu. Mvula imanya ni kudali kozizila kupunda, chimwecho adasongha moto ni kutikambila taonjhe tiothe. 3Poolo wadatondola mtolo wa nghuni ni kuziika pamoto. Nambho yapo wamaziika pamoto, njoka iyo idali ni sumu idasolomoka kuchokela mumtolo ni kujhivilinga mmanja mwake. 4Wandhu amchilumba mujha yapo adaiona ijha njoka niilendelela mmanja mwa Poolo, adakamba, “Mundhu uyu siwakhale wakupha! Walepela kufa mmajhi, nambho minungu yathu yovomelezeka siimusiya wakhale wamoyo.” 5Nambho Poolo wadaikung'undhila njoka ijha pa moto, ni siwadapate vuto lalilonjhe. 6Wandhu amatokhulupilila kuti watupe kapina kugwa panjhi kuti wamwalile pamwepo. Adalindilila ni kumpenyechecha kwa ndhawi yaitali, nambho padalibe choipa chilichonjhe icho chidamchokela. Chimwecho adang'anamula maganizo yawo, niakamba kuti Poolo ni mmojhi wa minungu.
7Ndiipo pafupi ni malo yajha padali ni minda ya wamkulu wa chilumba uyo wamatanidwa Pabulio. Wadatilandila kukhomo kwake ni wadatitumikila bwino kupunda, ni tidakhala kukhomo kwake kwa masiku yatatu. 8Atate wake Pabulio adali agona pachitala, niadwala mmimba ni kupesa mwazi. Nambho Poolo wadapita kukhomo kwake ni kumpembhelela. Wadamsanjika jhanja, nayo wadalama. 9Yapo yadachitika yaya, wodwala wina wonjhe muchilumba adajha kwa Poolo, nayo wadaapemhelela nawonjho adalama. 10Wajha wandhu adatipacha mbhaso zambili, ni yapo tidayamba ulendo, adatipacha mbhaso zambili ndande yo langiza mayamiko.
Ulendo wochokela ku chilumba cha Malita ni kupita ku Loma
11Pambuyo pa myezi itatu tidayamba ulendo kwa sitima, iyo idaima pachilumba chimenecho nyengo yonjhe yozizila. Tidakwela sitima iyo imachokela ku Alekizandiliya, iyo idaikidwa chizindikilo cha minungu ya mawila iyo itanidwa, “Kasitoli ni Polukusi.” 12Tidafika ku mujhi wa Silakusa ni tidakhala kumeneko kwa masiku yatatu. 13Tidachoka kumeneko, ni kufika ku mujhi wa Legio. Siku lochatila mbhepo imaputa kuchokela ku dela la kumwela, chimwecho tidaendekela ni ulendo, siku lakawili tidafika ku mujhi wa Puteoli. 14Pajha, tidaapeza okhulupilila anjathu, adatipembha kuti tikhale nawo kwa jhuma limojhi. Umu nde umo tidafikila ku Loma. 15Okhulupilila amakhala ku Loma yapo adavela nghani zathu, adafika kutilandila pa malo pokomanilana wandhu ambili patanidwa Apio, ni “Nyumba zitatu zodyela alendo.” Poolo yapo wadaaona wadamuyamika Mnungu ni kwathila mtima.
Poolo ku mujhi wa Loma
16Yapo tidafika ku Loma, Poolo adamulola kuti wakhale yokha uku wali ni asikali mmojhi wakumlonda.
17Pambuyo pa masiku yatatu Poolo wadaasonghanicha pamojhi achogoleli wa Ayahudi. Yapo adasonghana, Poolo wadayamba kwaakambila, “Achaabale wanga, sinidachite chilichonjhe chochuchana ni wandhu wathu kapina lochuchana ni mthethe wa azee wathu. Nambho nidamangwidwa ku Yelusalemu ni kupelekedwa kwa Aloma. 18Adanifunjha mafunjho yambili, nambho sidaone cholakwa chalichonjhe icho nachichita ivo chinichiticha kuniphela. Chimwecho amafuna kunisiyilila. 19Nambho Ayahudi yapo adakana chindhu chimenecho, nidafunika kupembha kuti mlandu uwu upelekedwe kwa Mfumu wamkulu wa ku Loma. Ingakhale sinifuna kwapacha mlandu wandhu ajhiko langa kwa chindu chalichonjhe. 20Ndendande nidapembha nikomane ni kukambana ni iwe. Namangidwa maunyolo yaya ndande ya chikhulupililo cha Izilaeli.”
21Anyiiwo adamuyangha Poolo, “Palibe kalata iyo tadalandila kuchokela kwa Ayahudi iyo ikamba nghani za iwe. Palibe myahudi mnjhatu waliyonjhe uyo wadachokela kumeneko ku Yudea ni kutikambila nghani zako kapina kutikambila kuti wachita choipa chilichonjhe. 22Nambho tifuna kuvela maganizo yako. Tijhiwa kuti wandhu ambili malo yonjhe alichucha gulu ili.”
23Adasangha siku lo pezana ni Poolo. Siku limenelo Ayahudi ambili adakomana ni Poolo mnyumba mwake. Wadakamba nawo nghani za Ufumu wa kumwamba kwa siku la mbhumbhu, niwadyelekezela wandhu kukhulupilila nghani za Yesu kuchokela mu thauko la Musa ni vikalakala va alosi. 24Wina adakhulupilila vijha wadakamba Poolo, nambho wina siadakhulupilile. 25Chimwecho kudachokela kosavane pakati pao, ni kuyamba kuchoka, Poolo wadaakambila chindhu chimojhi, “Mzimu Woyela udaakambila uzene kwa achatate wanu, kupitila mlosi Isaya kuti, 26Pakuti Mnungu wadakamba,
‘Pita kwa wandhu anyiyawa ukakambile,
Anyiimwe simuvechele, nambho simuvana navo,
Simupenye, nambho simujhiwa,
27Pakuti wandhu anyiyawa njelu zao zazelezeka,
acheka makutu yao,
athimila maso yao
ngati osati chimwecho, adakapenya kwa maso yao,
Adavela kwa maku yao,
adakajhiwa kwa njelu zao.
Ni kuning'anamukila,
Nane nidakaalamicha.’”
28Chimwecho poolo wadakamba, “Nifuna anyiimwe Ayahudi mjhiwe kuti, Mnungu waupeleka uomboli wake kwa wandhu osati Ayahudi. Nianyiiwo sauvechele!” 29Nayo yapo wadamaliza kukamba yameneyo, Ayahudi adachoka uku niafunjhana mafunjho yambili achinawene kwa achinawene.
30Poolo wadakhala kwa vyaka viwili mu nyumba yake iyo wadapanga mwene, uku niwadaalandila wandhu wonjhe yawo amajha kumuyendela. 31Wadaalalikila wandhu nghani za ufumu wa Mnungu ni kuyaluza nghani za Ambuye Yesu Kilisito, kwa mbhavu zonjhe ni popande kuopa ni palibe uyo wadamchekeleza.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Vichito 28: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.