Izi zidachitika monga zidaalembedwera m'buku la mneneri Yesaya kuti,
“Liwu la munthu wofuula m'chipululu:
akunena kuti,
‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye,
ongolani njira zoti adzapitemo.
Dzazani chigwa chilichonse,
chepetsani phiri lililonse ndi mtunda uliwonse.
Ongolani njira zokhotakhota,
salazani njira zazigolowondo.
Motero anthu onse adzaona chipulumutso
chochokera kwa Mulungu.’ ”