Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti,
“ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni.’
Ndiponso,
“ ‘Iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ”
Koma Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ”