YouVersion Logo
Search Icon

Lk. 3

3
Za uthenga wa Yohane Mbatizi
(Mt. 3.1-12; Mk. 1.1-8; Yoh. 1.19-28)
1Pa chaka cha khumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio, mfumu ya ku Roma, Ponsio Pilato anali bwanamkubwa ku Yudeya. Herode ankalamulira ku dera la Galileya. Filipo, mbale wake, ankalamulira ku dera la Itureya ndi ku dera la Trakoniti. Lisaniasi ankalamulira ku dera la Abilene, 2ndipo Anasi#3.2: Anasi: Onani pa Yoh. 11.49. ndi Kayafa#3.2: Kayafa: Onani pa Mt. 26.57; Yoh. 11.49. Aroma adaaika Kayafa kuti akhale mkulu wa ansembe onse m'malo mwa Anasi, koma kwa Ayuda mkulu wao wa ansembe onse anali Anasi ndithu. anali akulu a ansembe onse. Pa nthaŵi imeneyo Mulungu adampatsira uthenga Yohane uja, mwana wa Zakariya, m'chipululu. 3Choncho Yohaneyo adayendera dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yordani, akulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima ndi kubatizidwa, kuti Mulungu akukhululukireni machimo anu.” 4#Yes. 40.3-5 Izi zidachitika monga zidaalembedwera m'buku la mneneri Yesaya kuti,
“Liwu la munthu wofuula m'chipululu:
akunena kuti,
‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye,
ongolani njira zoti adzapitemo.
5Dzazani chigwa chilichonse,
chepetsani phiri lililonse ndi mtunda uliwonse.
Ongolani njira zokhotakhota,
salazani njira zazigolowondo.
6Motero anthu onse adzaona chipulumutso
chochokera kwa Mulungu.’ ”
7 # Mt. 12.34; 23.33 Anthu ambirimbiri ankabwera kuti iye aŵabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthaŵe chilango cha Mulungu chikudzachi? 8#Yoh. 8.33Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. Ndipo m'mitima mwanu musayambe zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu. 9#Mt. 7.19Pali pano nkhwangwa ili kale patsinde pa mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, adzaudula nkuuponya pa moto.”
10Pamenepo anthu aja adafunsa Yohane kuti, “Tsono ife tizichita zabwino zanji?” 11Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.” 12#Lk. 7.29Kudabweranso okhometsa msonkho kuti Yohane aŵabatize. Iwo adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ife tizichita zabwino zanji?” 13Iye adati, “Musamakhometsa msonkho moonjezera pa zimene adakulamulani.” 14Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.”
15Chiyembekezo cha anthu chidayamba kukula, ndipo onse ankaganiza za Yohane kuti kapena ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja. 16Tsono Yohane ankaŵauza onse kuti, “Ine ndimakubatizani ndi madzi, koma akubwera wina woposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto. 17Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.”
18Yohane ankalalikira anthu Uthenga Wabwino pakuŵalangiza motero, ndiponso mwa njira zina zambiri. 19#Mt. 14.3, 4; Mk. 6.17, 18Komanso adadzudzula mfumu Herode#3.19: Mfumu Herode: Ameneyu anali Herode Antipa. Iyeyu adaalanda mkazi wa mbale wake Filipo. Onani dzina la Herode pa Matanthauzo a Mau. (Mt. 14.1-4.) chifukwa chokwatira Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndiponso chifukwa cha zoipa zina zambiri zimene ankachita. 20Pambuyo pake, kuwonjezera pa zonsezi, Herode adatsekera Yohaneyo m'ndende.
Yesu abatizidwa
(Mt. 3.13-17; Mk. 1.9-11)
21Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka, 22#Gen. 22.2; Mas. 2.7; Yes. 42.1; Mt. 3.17; Mk. 1.11; Lk. 9.35ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi ngati la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”
Makolo a Yesu
23Yesu anali ndi zaka ngati makumi atatu pamene adayamba ntchito yake ya kuphunzitsa. Anthu ankamuyesa mwana wa Yosefe, amene anali mwana wa Eli, 24mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe, 25mwana wa Matatiasi, mwana wa Amosi, mwana wa Nahumu, mwana wa Hesili, mwana wa Nagai, 26mwana wa Mahati, mwana wa Matatiasi, mwana wa Semeini, mwana wa Yoseke, mwana wa Yoda, 27mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Salatiele, mwana wa Neri, 28mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elimadama, mwana wa Ere, 29mwana wa Yose, mwana wa Eliezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi, 30mwana wa Simeoni, mwana wa Yudasi, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu, 31mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natamu, mwana wa Davide, 32mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Sala, mwana wa Nasoni, 33mwana wa Aminadabu, mwana wa Adimini, mwana wa Arini, mwana wa Hesiromu, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda, 34mwana wa Yakobe, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahoro, 35mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Ebere, mwana wa Sela, 36mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki, 37mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani, 38mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, amene anali mwana wa Mulungu.

Currently Selected:

Lk. 3: BLY-DC

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in