1
Yesaya 11:2-3
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu, Mzimu wauphungu ndi wamphamvu, Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova. Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa.
Compare
Explore Yesaya 11:2-3
2
Yesaya 11:1
Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.
Explore Yesaya 11:1
3
Yesaya 11:4
koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo, adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi. Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake; atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.
Explore Yesaya 11:4
4
Yesaya 11:5
Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.
Explore Yesaya 11:5
5
Yesaya 11:9
Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga pa phiri lopatulika la Yehova, pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.
Explore Yesaya 11:9
6
Yesaya 11:6
Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi, mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.
Explore Yesaya 11:6
7
Yesaya 11:10
Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero.
Explore Yesaya 11:10