Alom 7

7
Chifani cha ukwati
1Anya abale wanga, chipano nikamba ni anyiwajha alijhiwa thauko, simjhiwa kuti thauko likhala ni ulamulilo kwa mundhu wakakhala wamoyo? 2Kwa chifani, wamkazi uyo wakwatiwa wamangidwa ni thauko ndhawi yonjhe yapo mmunake wakhala wamoyo, nambho mmunake wakamwalila, thauko limenelo silimmanganjho wamkazi mmeneyo. 3Chimwecho wamkazi mmeneyo wakakwatiwa ni wammuna mwina ndhawi iyo mmunake wali wamoyo, siwatanidwe wachighololo. Nambho mmunake wakamwalila, wamkazi mmeneyo siwamangidwanjho ni thauko la ukwati, ni wakakwatiwa ni wammuna mwina siwatanidwa wachighololo. 4Mchimwecho acha abale wanga, anyiimwe mdalekeledwa kuchokela thauko ngati umo mmakhalila kale, anyiimwe ni malo ya thupi la kilisito, chipano muli wa yujha wadahyukichidwa kuti mkhoze kuchita vichito vabwino ndande ya Mnungu. 5Pakuti yapo timakhala ngati wandhupe umo akhalila, makumbilo yayo yadasongezeledwa ni machimo yamachita njhito mmatupi yathu, ni kupeleka nyifa. 6Kalepo tidamangidwa ni thauko, nambho saino tamwalila pamojhi kilisito, mchimwecho tamasulidwa kuchokela mthauko. Chipano sitimtumikila Mnungu kwa njila ya kale ya kugwila thauko ilo lidalembedwa, nambho timtumikila Mnungu kwa njila ya chipano ya kuchogozedwa ni mzimu wa wake.
Thauko ni machimo
7Chipano tikambe bwanji, tikambe kuti thauko ni mchimo? Notho! Nambho popande thauko, ine sinidakayajhiwa machimo ni chindhu chanji. Pakuti sinidakajhiwa mate yokumbila voipa, ngati thauko silidakakamba, “siudakhumbila” 8Nambho kwa kutumila thauko limenelo, lidabala mkati mwanga kila mtundu wa khumbilo loipa. Pakupi popande thauko machimo ni chindhu cho mwalila. 9Masiku ya mmbuyo yapo sinimalijhiwe thauko la Mnungu nimakhala umo nimafunila, nambho yapo nidajhiwa kuti thauko lifuna chiyani nidajhijhiwa kuti ine nili ni machimo. 10Chimwecho thauko ilo limafunika kupeleka umoyo kwaine, lapeleka nyifa. 11Pakuti machimo yadapata malo mthauko, chipano machimo yadaninyenga kwa njila ya lamulo limenelo ni kunipelekela lamulo la nyifa.
12Chimwecho thauko lene lachoka kwa Mnungu, ni lamulo lene lachoka kwa Mnungu, ni yali ngati umo yafunikila ni yabwino 13Bwanji ichi chilangiza chijha chili cha bwino chapeleka lamulo la nyifa yanga? Ata pang'ono! Ni chimwechi kuti machimo dala yaoneke padanga kuti ni machimo yachitumia chijha chili cha bwino ni kupeleka lamulo la nyifa yanga. Chimwecho machimo, kwa njila ya lijha lamulo, yadajhilangiza mokwanila umo ili yoipa kupunda.
Nghondo mkati mwa mundhu
14Tijhiwa kuti thauko ni lachizimu, nambho ine osati wa Chizimu, ine naghulichidwa dala nikhale kapolo wa machimo. 15Sinichijhiwa icho nichichita, pakuti chijha nichifuna sinichichita, nambho icho sinichifuna ndeicho nichichita. 16Ngati nichita chijha sinichifuna ine kuchita, pamenepo nivomela kuti lijha thauko ni la bwino. 17Nambo kwa uzene osati inenjho nichita chijha sinichifuna, nambho ni yajha machimo yakhala mkati mwanga nde yayo yanichita nichite icho sinichifuna. 18Nijhiwa kuti palibe chabwino chalichonjhe mkati mwanga, kuchokana ni umundhu wanga, pakuti nifuna kuchita chindhu chabwino nambho sinikhoza kuchita. 19Pakuti chijha chindhu chabwino nichifuna sinichichita, nambho choipa icho sinichifuna nde icho nichichita, 20chipano ngati nichita icho sinichifuna, osati ine nichita nambho yajha machimo yakhala mkati mwanga nde yayo yachita.
21Chipano najhiwa chimwechi, kuti nifuna kuchita chindhu chabwino, nambho nijhipeza kuti chijha chilichoipa nde ichonisangha. 22Mumtima wanga, nilikondwela thauko la Mnungu. 23Nambho niona kuti mkati mwanga kuli thauko lina ilo lichita njhito ilo lichuchana ni maganizo yanga ya bwino. Thauko limenelo linichita kukhala kapolo wa thauko la machimo yayo yachita njhito mthupi mwanga. 24Chindhu ichi chinidandaula kupunda! Yani siwaniombole kuchokela mthupi lino linipeleka kunyifa? 25Nimuyamika Mnungu uyo waniombola kupitila kwa Yesu kulisito!
Chimwechi nde umo nili ine, kwa njelu zanga, nilitumikila thauko la Mnungu, nambho kwa thupi langa liniguza kuchata machimo.

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Alom 7: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល