Alom 3
3
1Chipano kukhala Muyahudi kuthangatila chiyani? Kapina kuchita mdulidwe kuthangatila chiyani? 2Zenedi, kukhala Muyahudi kuthangatila kupunda. Poyambila Mnungu wadapacha Ayahudi Uthenga wake. 3Nambho siikhale bwanji ngati akumojhi wake sadakhulupilile? Bwanji, chindhu chimenecho sichichoche kukhulupilika kwa Mnungu? 4Notho! Mnungu wakhala wokhulupilikape, ata ngati kila mundhu ni wamthila. Ngati umo yalembedwa mamalembo ya Mnungu,
“Ndhawi zonjhe yapo mkamba, mawu yanu ni uzene,
ni Pamalamulo, imwe mkhoza.”
5Wandhu akhoza kufunjha kuti voipa vathu vilangiza kuti Mnungu wakamba uzene, Bwanji, tikambe kuti walakwila kutilanga? 6Notho! Ngati Mnungu siwadakakhala wauzene, wadakakhoza bwanji kulilamula jhiko?
7Wandhu akhoza kukamba, ngati kosa khulupilile kwatu kwachita wandhu wina aone kuti Mnungu ni wazene, chipano Mnungu siwafunika kutitana ife kuti woyomwa, ni siwafunika kunilanga! 8Kumeneko ni sawa ni kukamba kuti, “Tiyeni tiyendekele kuchita voipa kuti tipate vabwino!” Wandhu wina atinamizila ata ife kuti tiyaluza chimwecho. Wandhu yawo akamba chimwecho salangidwe kwa voipa vawo!
Wandhu wonjhe achita machimo
9Tikambe chiyani chipano? Bwanji, ife Ayahudi tili bwino kupitilila wina? Notho! Pakuti nathokamba poyamba, kuti Ayahudi ni wandhu amaiko yina wonjhe ali panjhi pa ulamulilo wa machimo. 10Ngati umo yalembeledwa Mmalembo ya Mnungu,
“Palibe ata mundhu mmojhi uyo wachita yayo yamkwadilicha Mnungu!
11Palibe mundhu waliyonjhe uyo wamlambila Mnungu, ni palibe mundhu uyo wamfunafuna Mnungu.
12Wandhu wonjhe amsiya Mnungu,
palibe uyo wachita ivo vifunika kwa Mnungu,
palibe ata mmojhi.
13Makamwa yawo yajhala mawu yoipa,
Malilime yao yajhala unami,
Mkamwa mwao yachoka mau yayo yali ni sumu ngati ya njoka.
14Makamwa yao yajhala mawu ya kwalesa wandhu wina ni mawu yayo yapweteka.
15Wandhu amenewo ayangukila kupita kupha wandhu,
16paliponjhe yapo akhala ni wandhu, awananga ni kwaavutiticha wina.
17Ayiiwo saajhiwa kukhala ni wandhu wina kwa mtendele,
18samulemekeza Mnungu ata pang'ono.”
19Tijhiwa kuti thauko lili ndande ya wandhu ali panjhi pa thauko limeneno, ni sakhoza kukhala ni chilichonjhe cho namizila. Ni jhiko lonjhe lili panjhi pa lamulo la Mnungu. 20Pakuti palibe mundhu waliyonjhe siwavomelezeke kuti ni wokhulupilika pachogolo pa Mnungu, kwa kuligwila thauko, njhito ya thauko ni kumlangizape mundhu kuti wachita machimo.
Kuvomelezedwa kwa njila ya kukhulupilila
21Nambho chipano njila ya kwachita wandhu avomelezeke kwa Mnungu ili padanga, popande kukhulupilila thauko, osati ngati umo lidakambila thauko la Musa ni malembo ya alosi a Mnungu vonjhe vikambilila chindhu chimenecho. 22Mnungu waavomela wandhu kuti ni woyela kwa njila ya chikhulupi chao kwa Yesu Kilisito, Mnungu wachita chimwecho kwa wonjhe akhulupilila, siwapatula Ayahudi ni wandhu yawo osati Ayahudi. 23Wandhu wonjhe achita machimo, palibe uyo wali wabwino ni wonjhe ataiza kulemekezedwa ni Mnungu. 24Nambho kwa mbhaso ya ubwino wa Mnungu, wandhu wonjhe avomelezedwa kuti ni abwino pachogolo pa Mnungu kwa njila ya Yesu Kilisito uyo wadaombola. 25Mnungu wadamchocha Yesu kuti, kwa mwazi wake wakhale njila ya kwachochela wandhu machimo yao kwa kumkhulupilila. Wadachita chimwecho dala wakhoze kulangiza kuti iye ni woyela. Kale Mnungu wadalimbila mtima popande kwaalanga machimo yao, 26Nambho saino wayachucha machimo ya wandhu, kuti wakhoze kulangiza ubwino wake. Wachita chimwecho, dala walangize kuvomelezeka kwake ndhawi ino, iye wavomela wandhu wajha amkhulupilila Yesu.
27Chipano tikhoza kujhidama chiyani? Palibe chojhidamila! Ndande ife sitiwelengedwa kukhala wovomelezeka pachogolo pa Mnungu nambho kwa kumkhulupilila Yesu. 28Pakuti, tiona kuti Mnungu wawelengedwa kukhala woyela kwa njila yomkhulupilila Yesu, nambho osati kwa kuchita umo lifunila Thauko. 29Bwanji, Mnungu ni Mnungu wa Ayahudipe kapina ni Mnungu wa maiko yonjhe? Notho, ni Mnungu wa amaiko yonjhe, nawonjho ni Mnungu wao. 30Mnungu ni mmojhi, naye siwachite Ayahudi kukhala abwino kwa kumkhulupilila iye, ni wandhu amaiko yina kwa kumkhulupilila. 31Bwanji, yapo tisisitiza chikhulupi, bwanji, mate yake thauko ili lilibe phindu? Notho! Nambho tikakhala ni chikhulupi sikwaniliche yonjhe yayo yaagizidwa ni Thauko.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Alom 3: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.