Luka 22
22
Mpango womphela Yesu
Matayo 26:1-5; Maluko 14:1-2; Yohana 11:45-53
1Yapo lidawandikila mphwando la mabumunda yosathila amila, iyo itanidwa Pasaka. 2Achogoleli ni ajhukulu ni oyaluza mathauko amafunafuna njila yomubhela Yesu, niianyio amachita chimwecho kwa chisisi ndande amaopa wandhu.
Yuda wavomela kumng'anamukila Yesu
Matayo 26:14-16; Maluko 14:10-11
3Ndiipo, Satana wadamlowa Yuda, uyo wamatanidwa Isakaliyoti, mmojhi wa atumwi khumi ni awili. 4Yuda wadapita wadakambana ni ajhukulu wakulu ni alonda umo siwamng'anamukile Yesu. 5Anyiiwo adakondwa kupunda ni kuvomelezana nayo kuti ampache ndalama. 6Yuda wadavomela ni wadayamba kufunafuna njila ya bwino ya kumng'anamukila ndhawi iyo siwali pamojhi ni wandhu.
Pwando lo thela la Pasaka la Yesu
Matayo 26:17-25; Maluko 14:12-21; Yohana 13:21-30
7Yapo lidafika siku la pwando la mabumunda yosathila amila. Siku limenelo nde lidali siku lakupedwa kwa mwanambelele wa Pasaka. 8Yesu wadatuma Petulo ni Yohana wadakambila, “Pitani mkatikonjele chakudya cha Pasaka kuti tikhoze kuidya.” 9Anyiiwo adamfunjha Yesu, “Bwanji, mfuna tiikonjekele kuti.” 10Yesu wadakambila, “Velani, yapo simulowe mmujhi, simumkomane wammuna mmojhi uyo watenga mchuko. Mchateni iye mbaka mu nyumba iyo siwalowe. 11Mkambileni mwene nyumbayo kuti, ‘Oyaluza atofunjha, chumba cha alendo chili kuti, icho ine ni oyaluzidwa wanga sitidyele chakudya cha Pasaka?’ 12Iye siwakulangizeni chumba chachikulu kugolofa, icho chakonjekeledwa bwino. Mmenemo nde umo mkatikonjele.”
13Anyiiwo adapita ni adakomana kila kandhu chili ngati umo adakambilidwa ni Yesu, naonjho adakonjekela chakudya cha Pasaka.
Chakudya cha Ambuye
Matayo 26:26-30; Maluko 14:22-26; 1 Akolinso 11:23-25
14Yapo ndhawi idakwana, Yesu wadakhala kudya chakudya pamojhi ni atumwi wake. 15Ndiipo iye wadakambila, “Nakhumbila kupunda kudya chakudya cha Pasaka iyi pamojhi ni anyiimwe ikali yosafike ndhawi ya kuvutichidwa kwanga. 16Nikukambilani chimwechi, sinidyanjho chakudya cha Pasaka mbaka yapo Mnungu siwaombole wandhu wake wonjhe ni kwalamula.”
17Pambuyo wadatenga chikho, wadayamika ni kukamba, “Landilani chikho ichi, mmwele mwawonjhe. 18Nikukambilani, kuyambila chipano sinamwanjho divai ya chipacho cha zabibu, mbaka yapo siukwanile Ufumu wa Mnungu.”
19Ndiipo, wadatenga bumunda, wadayamika, ni kuubandhula, wadapacha atumwi ni kukamba, “Ili ni thupi langa ilo lichochedwa ndande ya anyiimwe. Mjichite chimwechi ponikumbukila ine.” 20Chimwecho, yapo adamaliza kudya, wadachita chimchijha wadatenga chikho chija ni kukamba, “Divai iyi ili mchikho ni chipangano cha chipano icho chichitidwa kwa mwazi wanga, uwo umwazika ndande yanu.”
21“Nambho mujhiwe mudhu uyo siwaning'anamukile wali pampano pa chakudya pamojhi ine. 22Ine mwana wa Mundhu nipita kuphedwa ngati umo wadakondela Mnungu. Nambho, siwavutike mundhu oyo siwaning'Sanamukile.”
23Pamwepo adayamba kufunjhana achinawene wake, yani uyo siwamng'anamukile.
Mkangano kuusu ukulu
24Padachokela mkangano pakati pao kuti yani uyo wali wamkulu kuposa wina. 25Yesu wadakambila, “Mafumu ajhiko walamula wandhu wao kwa mbhavu, nawo afuna kutanidwa wandhu othangila wina. 26Nambho isadakhala chimwecho kwa anyiimwe, nambho uyo wali wamkulu pakati panu ifunika wakale ngati wang'ono wa wandhu wonjhe, ni uyo walamulila wakhale ngati mbowa. 27Yani uyo wali wamkulu, yujha wakhala pachakudya kapina yujha watumikila? Zenedi ni yujha wakhala panjhi ni kudya chakudya. Nambho ine nili pamojhi na anyiimwe ngati mbowa wanu.”
28“Anyiimwe mwakhala pamojhi ni ine pa ndhawi yonjhe yakuyesedwa kwanga. 29Ngati umo adanipachila ufumu Atate wanga, chimwecho nanenjho nikupachani ufumu anyiimwe. 30Kuti mkhoze kudya ni kumwa pa ufumu wanga. Simukhale mmipando ya ufumu ni kuyalamula mafuko khumi ni yawili yaku Izilaeli.”
Yesu walosela kuti siwakanidwe ni Petulo
Matayo 26:31-35; Maluko 14:27-31; Yohana 13:36-38
31Yesu wadakamba, “Simoni, Simoni! Satana wampembha kukupetani anyiimwe ngati umo wandhu apetela mpunga kuti wajhiwe ngati simuyendekele ni chikhulupililo. 32Nambho ine nakupembhelela iwe Simoni, kuti chikulupililo chako chisadachepekela, ni yapo siunibwelele waathile mtima achanjako.” 33Petulo wadayangha, “Ambuye ine nakonjeka kupita namwe kundende, ni mbaka kumwalila.”
34Nambho Yesu wadamuyangha, “Nikukambila iwe Petulo, usiku wa lelo, tambala wakali osalila siukhale wanikana katatu kuti siunijhiwa.”
Mjhikonjekele kwa nghondo
35Ndiipo, Yesu wadafunjha oyaluzidwa wake, “Yapo nidakufunani mpite popande thumba cha ndalama, kapina chikwama njhalu ni cha malapasi, bwanji mdachepekedwa ni chiyani?”
Anyiiwo adamuyangha, “Notho!”
36Iye wadakambila, “Nambho chipano, uyo wali ni thumba la ndalama watenge ni uyo wali ni chikwama watengenjho. Ni uyo walibe upanga, waguliche khoti lake wakagule upanga. 37Ndande, malembo yoyela yakamba, ‘Wadaikidwa gulu limojhi ni wandhu woipa.’ Niine nikukambilani chimwechi, chindhu ichi chalembedwa kuniusu ine chifunika chikwanilichidwe.”
38Oyaluzidwa wake adamkambila, “Penyani Ambuye, pano tili ni maupanga yawilipe!”
Nayenjho wadayangha, “Yakwana.”
Yesu wapembhela kuphili la Mizeituni
Matayo 26:36-46; Maluko 14:32-42
39Yesu, ngati umo idali mthethe wake, wadachoka ni kupita ku Phili la Mizeituni, nawo oyaluzidwa wake adamuchata. 40Yapo wadafika ku phili, wadaakambila, “Mjhipembhela kuti musadalowa mmayeso.” 41Iye wadajhipatula ni kupita patali pang'ono, wadagwada ni kuyamba kupembhela, niwakamba, 42“Atate, ngati ikhozekana, mavuto yaya yasadanipata, nambho osati ngati umo nifunila ine, nambho ikhale ngati umo mfunila imwe.” 43Pamwepo, atumiki akumwamba a Mnungu adamtulukila kuti amthile mtima. 44Ni Yesu wali mkati mwa kupweteka kwakukulu, wadapembhela kupunda. Chitukuta chake chidali ngati mitondho ya mwazi iyo imasililika panjhi.
45Yapo wadamaliza kupembhela, wadaima ni kwaachata oyaluzidwa wake, wadaakomana agona ndande adali ni chisoni. 46Iye wadaafunjha, “Bwanji mwagona? Ukani mupembhele kuti musadalowa mumayeso.”
Yesu wagwilidwa
Matayo 26:47-56; Maluko 14:43-50; Yohana 18:3-11
47Yesu yapo wadali kuyendekela kukamba, gulu lalikulu wa wandhu lidajha, nilichogozedwa ni Yuda mmojhi wawajha atumwi khumi ni awili. Yuda wadamuwandikila Yesu ni kumbusu. 48Nambho Yesu wadamfunjha Yuda, “Bwanji, umng'anamuka mwana wa Mundhu kwa kumbusu?”
49Nambho anyiwajha ochatila wake yapo adaona yameneyo, adakamba, “Atate, timdule kwa maupanga yathu?” 50Ni mmojhi wao wadamdula mbowa wa wamkulu wa ajhukulu khutu lake lakwene kwa upanga. 51Nambho Yesu wadakamba, “Lekani ikwana!” Nayo wadaligafya khutu la mundhu yujha ni kumlamicha.
52Ndiipo, Yesu wadaakambila achogoleli wa ajhukulu, wakuluakulu wa alonda a nyumba ya Mnungu ni azee yawo adajha kumgwila, wadaafunjha, “Bwanji mwafika ni maupanga ni vibonga kunigwila, ngati kuti ine ni wopanduka? 53Masiku yonjhe nidali namwe mu khumbi la mnyumba ya Mnungu, nambho simudanikgwile. Nambho iyi ni ndhawi yanu ya ulamulilo wa mdima.”
Petulo wamkana Yesu
Matayo 26:57-58; Maluko 14:53-54,66-72; Yohana 18:12-18,25-27
54Ndiipo, adamgwila Yesu ni kupita naye mbaka kukhomo kwa wamkulu wa ajhukulu. Nambho Petulo wamachota mbuyombuyo kwapatali. 55Yapo adasongha moto pakatikati pa seli lijha ni kukhala pamojhi, Petulo nayo wadajha kukhala pamojhi ni anyiiwo. 56Mbowa mmojhi wamkazi yapo wadamuona Petulo wakhala pafupi ni moto, wadampenyechecha kupunda ni kukamba, “Mundhu uyunjho wadali pamojhi ni Yesu.” 57Nambho Petulo wadakana pokamba, “Iwe maye! Sinimjhiwa mundhu mmeneyo.” 58Pambuyo pang'ono, mundhu mwina wadamuona Petulo ni wadakamba, “Iwe nawenjho ni mmojhi wao.” Nambho Petulo wadayangha, “Iwe mundhu, ine osati mmojhi wa anyiiwo!”
59Yapo idapita ngati saa imojhi, mundhu mwina wadachimikiza niwakamba, “Zenedi mundhu uyu nayo wadali pamojhi ni Yesu, pakuti iye nayonjho ni Mgalilaya.” 60Nambho Petulo wadayangha, “Iwe mundhu, ine sinijhiwa icho ukamba!” Ndhawi imweyo wali mkati mokamba, tambala wadalila.
61Ambuye naonjho adang'anamuka ni kumpenyecha Petulo. Ndiipo Petulo wadakumbukila mawu yajha wadakambilidwa ni Ambuye, “Lelo siunikane katatu tambala wakali osalile.” 62Iye wadatuluka kubwalo uku ni wapwetekedwa mumtima ni kuyamba kulila kupunda.
Alonda amkwiicha Yesu
Matayo 26:67-68; Maluko 14:65
63Wandhu wajha adamgwila Yesu adayamba kumkwiicha ni kumbula. 64Adammanga chitambala kumaso ni kumfunjha, “Losa! Yani uyo wakubula!” 65Anyiiwo adayendekela kumkambila mawu yambili ya matukwano.
Yesu pachogolo pa bwalo la Ayahudi
Matayo 26:59-66; Maluko 14:55-64; Yohana 18:19-24
66Yapo kudacha umawa, bwalo la azee awandhu pamojhi ni ajhukulu waakuluakulu ni oyaluza athauko adakomana pamojhi. Adampeleka Yesu pachogolo pa bwalo limenelo. 67Adamkambila, “Tikambile, ngati iwedi nde Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu?” Nambho Yesu wadayangha, “Ata ngati nikakukambilani simunikhulupilila, 68ni ata ngati nikakufunjhani funjho simuniyangha. 69Nambho kuyambila saa ino, ine Mwana wa Mundhu sinikhale bendeka la ulemu la Mnungu Wambhavu Zonjhe.”
70Wandhu wonjhe adamfunjha, “Iwe nde Mwana wa Mnungu?” Iye wadayangha, “Yetu, icho mwakamba anyiimwe ni chauzene.” 71Nianyiiwo adakamba, “Ndande yanji tifunefune umboni winanjho yapa? Tamvela taachinawefe niwakamba kuchokela mkamwa mwake.”
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Luka 22: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.