Luka 14
14
Yesu wamlamicha mundhu wadatupa thupi lonjhe
1Siku limojhi Lopumula, Yesu yapo wadalalikidwa kupita kudya chakudya kunyumba ya achogoleli mmojhi wa Afalisayo, uku wandhu na amatomnyemelela. 2Pachogolo pa Yesu padali mundhu mmojhi uyo wadali ni utenda wothupa thupi. 3Yesu wadafunjha woyaluza thauko ni Afalisayo, “Bwanji, ni bwino kulamicha wandhu siku Lopumula kapina notho?” 4Nambho anyiiwo adakhala chete. Chimwecho, Yesu wadamgwila janja ni kumlamicha, ni kumkambila wapite kukhomo lake. 5Ndiipo wadaafujha, “Yani pakati panu ngati mwana wake kapina ng'ombe ikabila mjhenje pasiku Lopumulila wasidabila kumchocha msangu ndande ni siku Lopumulila?” 6Nianyiiwo adakhala chete
Kujhikweza ni kujhichicha
7Yesu yapo wadaona alendo yao alalikidwa akhala mipando ya ulemu, ndipo wadayaluza chifani ichi, 8“Ngati mundhu siwakakulalike ku ukwati, usadakhala pa mpando wa ulemu, pakuti ikhozeka pali mundhu mwina wa ulemu kupitilila iwe, yawo waikilidwa mpando umeneo, 9ngati wakhala pamenepo, ni yujha wakulalikani, wakajha ni kukamba, ‘Patuka msiile uyu mpando wako.’ Ndiipo iwe siulenge njhoni, siifunike kukhala pampando wosalemekezeka. 10Mmalo mwake yapo ulalikidwa kupwando, kakhale pampando wopande ulemu, dala kuti yapo wakujha uyo wakulalika, wakukambile, ‘Bwenji langa, pita ukakhale pa malo ya ulemu.’ Pamenepo siukhale wapachidwa ulemu pamaso pa alendo wonjhe yawo alalikidwa pamojhi ni iwe. 11Pakuti kila mundhu uyo wajhiika wamkulu, siwakhale wamng'ono, ni uyo wajhiika wang'ono siwakhale wamkulu.”
12Ndiipo wadamkambila yujha wadaalalika, “Ngati ukonja chakudya cha usana kapina ujhulo, usadaalalika achabwenji wako, kapina achabale wako, kapina apafupi wako wopata, pakuti ukachita chimwecho, naonjho akhoza kukulalika kwao ni kukubwezela icho udaachitila. 13Mmalo mwake yapo ukonja phwando, waalalike wosauka, wovuwala ni ndendele ni wosapenya, 14pakuti siukhale ni mwawi ingakhale achamenewo alibe kandhu kakukubwezela. Mnungu siwakubwezele siku ilo saahyuke wandhu yawo avomelezedwa ni Mnungu.”
Chifani cha phwando lalikulu
Matayo 22:1-10
15Ndiipo yapo wadavela yameneyo, mundhu mmojhi pakati pa wandhu wajha adakhala ni Yesu wadamuyangha, “Wali ni mwawi mundhu uyo siwadye chakudya cha phwando la Ufumu wa Mnungu!”
16Yesu wadamuyangha, “Padali mundhu mwina uyo wamakonjekela phwando lalikulu, wadaalalika wandhu wochuluka. 17Ndhawi ya phwando yapo idafika, wadaatuma mbowa zake zikaakambile wandhu wajha alalikidwa, ‘Majhani, kila kandhu kali tayali.’ 18Nambho wonjhe adayamba kukana pa kuchocha ndande yakulepela kufika. Woyamba wadamkambila mbowa mmeneyo, ‘Nagula munda, chimwecho nifuna nipite nikauone, nipembha muniloleze.’ 19Wina wadakamba, ‘Nagula ng'ombe khumi zolimila, chipano nifuna nipite nikaziyese, chonde nipembha muniloleze.’ 20Ni mwinanjho wadakamba, ‘Ine nakwata chipano yapa, chimwecho sinikhoza kujha.’ 21Mbowa mmeneyo wadabwela ni kumkambila bwana wake nghani imeneyo. Mbuye yujha wadakwiya kupunda, wadamkambila mbowa wake yujha, ‘Pita msanga mnjila zazikukulu ni njila za mmikwakwa ya mujhi, okajhenawo osauka, wovuwala, osapenya ni andendele ajhe.’ 22Pambuyo pake mbowa yujha wadakamba, ‘Mbuye, yayo mdanituma nayachita, nambho yakhalila malo mnyumba ya phwando.’ 23Ndiipo mbuye yujha wadamkambilanjho mbowa wake, ‘Pita mnjila zazikulu ni njila zazing'onozingono za mikwakwa ya mujhi, ni kwaahimiza wandhu ajhe, kuti nyumba yanga ijhale. 24Pakuti nikukambilani, palibe ata mmojhi wa wandhu wajha alalikidwa ni kukana, uyo siwalowe ni kudya chakudya changa paphwando.’ ”
Yayo yafunika dala ukhale woyaluzidwa wa yesu
Matayo 10:37-38
25Gulu lalikulu la wandhu lidali pamojhi ni Yesu paulendo. Ndiipo iye wadaang'anamukila wandhu ni kwaakambila, 26“Ngati mundhu waliyonjhe wafuna kukhala woyaluzidwa wanga, ifunika wanikonde ine kupitilila umo waakondela atate wake na amake, mkazake ni wana, achakulu wake ni achalongo wake, ata kupitilila umo wajhikondela mwene wake. Ngati siwachita chimwecho, siwangakhoze kukhala woyaluzidwa wanga. 27Mundhu waliyonjhe uyo siwavemela kuvutika ni kumwalila yapo wanichata, siwakhoza kukhala woyaluzidwa wanga. 28Pakuti, yani pakati panu uyo wafuna kumanga nyumba zanjwela, siwakhala panjhi ni kuganizila kuchuluka kwa ndalama zokhoza kumalizila kumanga? 29Pakuti wakamaliza kumanga msingi ni kulepela kumanga nyumba imeneyo, wandhu wonjhe yawo aiona sayambe kumseka, 30niakamba, ‘Mundhu uyu wadayamba kumanga nyumba, nambho walepela kumalizila.’ 31Nikambe chifani china, bwanji, mfumu yuti uyo wakhoza kumenyana nghondo ni mfumu mwina, uyo siwakhoza kukhala panjhi nikuganiza kuti asikali wake elufu khumi, siakhoze kumenyena nghondo ni mfumu yujha wakujha ni asikali elufu ishilini? 32Ni wakajhiwa kuti siwakhoza, basi siwaatume athenga wake kuti apite kwa yujha mfumu mwina wakali kutali, akampembhe kuvomelezana. 33Chimwecho, palibe mundhu waliyonjhe pakati panu uyo siwakhale woyaluzidwa wanga ngati siwaleka kila kandhu yako walinako.”
Mchele osakoma
Matayo 5:13; Maluko 9:50
34“Mchele ni wabwino, nambho mchelewo ngati siukomecha, siuthilidwemo chiyani kuti ukomeche? 35Siufunika, ingakale kwa dothi kapina kwa kuchita chayila, wandhu autaya. Mchate yayo nikukambilani!”
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Luka 14: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.