Yohana 20

20
Yesu wahyuka
Matayo 28:1-8; Maluko 16:1-8; Luka 24:1-12
1Jhumaapili umawamawa, kukali kosache, Maliya uyo wadachokela ku Magidala wadapita kuchiliza, wadapheza mwala wachochedwa pakhomo la chiliza. 2Ndiipo wadathamanga msanga mbaka kwa Petulo ni oyaluzidwa mwina uyo wadakondedwa ni Yesu, wadamkambila, “Alichocha thupi la Ambuye pachiliza, sitijhiwa uko aliika.”
3Petulo pamojhi ni yujha oyaluzidwa mwina adapita kuchiliza. 4Onjhe awili adathamanga, nambho yujha mwina wadathamanga msanga kulekana ni Petulo, wadachoghola kufika kuchiliza. 5Yapo wadakwatama ni kuzuzumila mkati, wadaona sandape zaikidwa, nambho siwadalowe mkati. 6Simoni Petulo wadajha, wadalowa mchiliza, mmenemo wadaona sandape zaikidwa, 7ni chitambaa icho wadamangidwa Yesu kumutu. Sichidaikidwe pamojhi ni sanda, nambho chavilingidwa ni kuikidwa pachokha. 8Ndiipo oyaluzidwa mwina uyo wadachoghola pa chiliza, wadalowa mkati wadaona ni kukhulupilila. 9Adali akali osajhiwe Malembo Yoyela yayo yadakamba kuti idali lazima wahyuke. 10Chimwecho oyaluzidwa adabwela kukhomo.
Yesu wamtulukila Malia uyo wadachokela ku Magidala
Matayo 28:9-10; Maluko 16:9-11
11Nambho Malia wadaima pabwalo pa chiliza, wamatolila. Yapo wamalila, wadakwatama ni kuzuzumila mchiliza, 12wadaona atumiki akumwamba Amnungu awili avala njhalu zoyela mbee, akhala yapo lighonekedwa thupi la Yesu, mmojhi kumutu mwina kumyendo. 13Atumiki akumwamba achameneo adamfunjha malia, “Maye, ndande yanji mulila?”
Wadamkambila, “Waachocha Ambuye wanga, sinijhiwa ukoaikidwa!”
14Yapo wadakamba yameneyo, wadang'anamuka kumbuyo, wadamuona Yesu waima pamenepo, nambho siwadajhiwe kuti nde Yesu. 15Yesu wadamfunjha, “Maye, ndande yanji mulila? Mumfunafuna yaani?”
Malia wamaganiza osunga busitani, wadamkambila, “Olemekezedwa ngati imwe nde mwaatenga, pepani nipembha munilangize ukomwamuika, sinimtenge.”
16Yesu wadamkambila, “Malia!”
Malia nayo wadang'anamuka, wadamkambila kwa Chihebulania, “Laboni” Mate yake “Oyaluza.”
17Yesu wadamkambila, “Usadanigwila, ndande nikali osapite kumwamba kwa Atate. Nambho mapita kwachabale wanga ukaakambile. Nipita kumwamba kwa Atate wanga ni Atate wanu, Amnungu wanga ni Amnungu wanu.”
18Chimwecho Malia uyo wadachokela ku Magidala wadapita kwaapacha nghani oyaluzidwa naona Ambuye, ni kuti wadamkambila chimwecho.
Yesu waachokela oyaluzidwa wake
Matayo 28:16-20; Maluko 16:14-18; Luka 24:36-49
19Idali ujhulo siku lo yamba la jhuma. Oyaluzidwa wake adakomana pamojhi mkati mwanyumba, vicheko vidachekedwa ndande ya kwaopa achogoleli wa Ayahudi. Ndiipo Yesu wadajha kuima pakati pao, wadakambila, “Mtendele ukhale kwanu!” 20Yapo wadakamba yameneyo, wadalangiza manja yake ni ndhiti yake. Chimwechi oyaluzidwa wake adali ni chimwemwe kupunda kwaona Ambuye. 21Yesu wakambilanjho, “Mtendele ukhale kwanu! Ngati Atate adanituma ine, nane nikutumani anyiimwe.” 22Yapo wadakamba yameneyo, wadaapumbuzila mpuyo ni kwakambila, “Landilani Mzimu Oyela. 23Mkaalekelela wandhu machimo yao, wandhu achameneo sialekeleledwe, mkasia kwalekelela volakwa vao nawo salekeleledwa.”
Yesu wamtulukila Tomaso
24Nambho Tomaso, uyo wamatanidwa Mawila mmojhi wa oyaluzidwa anyiwajha khumi ni awili, siwadali pamojhi nao yapo wadajha Yesu. 25Ndiipo, oyaluzidwa wina adamkambila, “Taona Ambuye.” Nambho iye wadaakambila, “Nikasiya kuona mawala ya mizumali mmanja mwake ni kubiza chala changa mmawala ya mizumaliyo ni kubiza jhanja langa mundhiti mwake, sinikhulupilila.”
26Chimwecho, pambuyo pa masiku nane oyaluzidwa adalinjho pamojhi mujha munyumba, ni Tomaso wadali pamojhi nao. Vicheko vidamangidwa ni kuima pakati pao wadakamba, “Mtendele ukhale kwanu!” 27Ndiipo wadamkambila Tomaso, “Jhanacho chala chako upenye manja yanga, jhanalo jhanja lako ubize mundhiti mwanga. Msadakhaikila, nambho khulupilila!”
28Tomaso wadayangha, “Ambuye wanga ni Amnungu wanga!”
29Yesu wadammbila, “Bwanji unikhulupilila ndande waniona? Apachidwa mwawi anyiiwo sadanione, nambho akhulupilila.”
Ndande ya kulemba chikalakala ichi
30Yesu wadachita vizindikilo vina vambili pachogholo pa oyaluzidwa wake ivo sividalembedwe mu chikalakala ichi. 31Nambho ivi valembedwa dala mkhulupilile kuti Yesu nde Kilisito, Mwana wa Amnungu ni kumkhulupilila mkhale ni umoyo wa muyaya kwa kukhala mkati mwake.

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Yohana 20: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល