Yohana 15

15
Yesu Mzabibu wa Uzene
1Ndiipo Yesu wadakamba, “Ine ni mzabibu wa zene, ni Atate nde amlimi. 2Ndhawi yaliyonjhe iyo siibala vipacho mkati mwanga, Atate aidula, ni ndhawi iyo ibala aikonjezela ijhipunda kubala. 3Anyiimwe mwatho elechedwa muuzimu ndande ya uthenga uwo nidakuyaluzani. 4Khalani mkati mwanga, ngati umo ine nikhalila mkati mwanu. Ngati umo ndhawi ya mzabibibu siikhoza kubala yokha vipacho popande kukhala mumtengo wa mzabibu, chimwecho anyiimwe simukhoza kuchita chijha achifuna Amnungu ngati simukhala mkati mwanga.”
5“Ine ni mzabibu, anyiimwe ni ndhawi. Yao akhala mkati mwanga, nane nikakhala mkati mwao, achameneo sachite vindhu vabwino vambili, popande ine simukhoza kuchita kandhu. 6Mundhu wakasiya kukhala mkati mwanga wataidwa kubwalo ngati ndhawi ni kuuma. Ndhawi ngati zimenezo wandhu azikusa ni kuzitaya pamoto zipyelele. 7Anyiimwe mkakhala mkati mwanga ni mawu yanga yakakhala mkati mwanu, chipano, pembhani chilichonjhe icho mfuna namwe simpachidwe. 8Atate wanga apachidwa ulemelelo yapo mchita vindhu ivo vakwadilicha Amnungu, namwe simukhale oyaluzidwa wanga. 9Ine nikukondani anyiimwe ngati umo Atate adanikondela ine. Khalani muchikondi changa. 10Mkachita ngati umo afunila Atate ni kukhala muchikondi changa, ngati ine umo nichitila umo afunila Atate wanga ni kukhala mu chikondi chao.”
11“Nakukambilani vindhu ivi dala chimwemwe changa chikale mkati mwanu, ni chimwemwe chanu chikwanile. 12Lamulo langa nde ili, mkondane ngati ine umo nidakukondelani anyiimwe. 13Palibe chikondi chachikulu kupunda kusiyana ni chikondi cha mundhu uyo wachocha umoyo wake ndande ya bwenji lake. 14Anyiimwe achabwenji langa mkachita yayo nikulamulani. 15Sinikutananinjhoni mbowa, ndande mbowa siwajhiwa icho wachita wamkulu wake. Nambho ine nakutanani anyiimwe bwenji, ndande nakujhiwichani yonjhe yayo nayavela kuchoka kwa Atate. 16Anyiimwe simudanisanghe ine, nambho ine nidakusanghani anyiimwe nakutumani mkachite ivo avifuna Amnungu, ni njhito azifuna Amnungu izo sizikhaliche siku zonjhe. 17Chipano, lamulo langa kwanu nde ili, kondanani anyiimwe kwa anyiimwe.”
Wandhu a pajhiko sakuipileni
18“Ngati jhiko la panjhi likakuipilani anyiimwe, kumbukilani kuti lidaniipila ine likali kukuipilani anyiimwe. 19Ngati mudakali wandhu ajhiko, jhiko lidakakukondani ngati wandhu wake. Pakuti anyiimwe osati ajhiko, nambho ine nakusanghani kuchoka mujhiko, ndendande wandhu ajhiko akuipilani. 20Kumbukilani uthenga uwo nakukambilani, mbowa osati wamkulu kupitilila wamkulu wake. Ngati anivuticha ine, namwe sakuvuticheni, ngati adauchitila njhito uthenga wanga, siauchitile njhito uthenga wanu. 21Nambho sakuchitileni yonjheyo ndande anyiimwe ni ochatila wanga, pakuti samjhiwa uyo wanituma. 22Ngati sinidakajha ni kukamba mawu ya Amnungu sadakakhala ni machimo, nambho alibe chinamizilo kuti alibe machimo. 23Uyo waniipila ine, waipila Atate. 24Ngati nidakasiya kuchita vizindikilo pakati pao ivo sividachitidwepo ni mundhu waliyonjhe, sadakali ni machimo, chipano aviona vozizwicha nambho akali kuniipila ine ni Atate wanga. 25Dala likwanile mawu ilo lidalembedwa mu malembo lao, ‘Aniipila popande cholakwa.’
26“Yapo siwajhe othandiza uyo sinimtume kuchoka kwa Atate, Mzimu wauzene uyo wachokela kwa Atate, siwanichochele umboni. 27Namwenjho simunichochele umboni pakuti mudali ni ine kuyambila mmayambo.”

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Yohana 15: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល