Yohana 13

13
Yesu waachuka myendo oyaluzidwa wake
1Yapo lidawandikila siku la pwando la Pasaka, Yesu wadajhiwa kuti ndhawi yake yochoka pajhiko lapanjhi ni kupita kwa Atate ya kwana. Kila ndhawi wadaakonda wandhu wake anyiyao ali pajhiko, chimwecho wadaakonda mbaka kuuchocha umoyo wake!
2Yesu wadali ni oyaluzidwa wake adakhala kudyaa chakudya cha ujhulo. Satana wadathomthila Yuda, mwana wa Simoni, mtima wa kumng'anamuka Yesu. 3Yesu uku ni wajhiwa kuti Atate ampacha kila kandhu muulamulilo wake, ni kuti wadachoka kwa Amnungu ni kubwela kwa Amnungu. 4Ndiipo, wadasiya kudya chakudya, wadavula njhalu yake ya kubwalo, wadatenga chitambaa chochangulila ni kujhimanga muchiuno. 5Ndiipo Yesu wadapungulila majhi mbeseni ni kuyamba kwa kwasambiza oyaluzidwa wake mmyendo ni kwachangula kwa chitambaa icho wadajhimanga. 6Chimwecho yapo wadafika kwa Petulo, Petulo wadafunjha, “Ambuye simunichuke niine mmyendo?”
7Ndiipo Yesu wadayangha, “Siuchijhiwa icho nichita chipano, nambho pambuyo siujhiwe.”
8Petulo wadamkambila, “Siunichuka myendo muyaya!”
Yesu wadayangha, “Nikasia kukuchuka siukhalanjho ni mgwilizano ni ine.”
9Simoni Petulo wadamkambila, “Ambuye, nichukeni, osati mmyendo pe nambho ni manja ni mutu wanga.”
10Yesu waadakambila, “Mundhu wakathosamba mthupi walibe haja yosambanjho, nambho wafunika kusamba mmyendo, ndande wathoyela thupi lonjhe. Anyiimwe mwayela, nambho osati mwaonjhe.” 11Yesu wadamjhiwa uyo siwamng'anamuke, nde ndande wadakamba, “Anyiimwe mwayela, nambho osati mwaonjhe.”
12Yapo wadathokwasambiza mmyendo ni kuvalanjho njhalu yake ni kukhalanjho pachakudya, wadaafunjha, “Bwanji, mwayajhiwa yayo nakuchitilani? 13Anyiimwe munitana Oyaluza ni Ambuye, mwakamba mwauzene ine nde mmeneyo. 14Chipano, ngati ine nili Ambuye ni Oyaluza wanu, nakuchukani anyiimwe myendo, namwe ifunika muchukane myendo. 15Nakupachani chifani kuti namwe mchite ngati umo nachitilani ine. 16Zenedi nikukambilani, mbowa osati wamkulu kumpitilila wamkulu wake, ni mtumwi osati wamkulu kusiyana ni uyo wamtuma. 17Chipano, ndande mwayajhiwa yaya, Amnungu siakupacheni mwawi mkayachita.”
18“Sinikamba chimwecho kwa mwaonjhe. Naajhiwa anyiyao naasangha. Nambho kuti malembo yakwanile, yayo yakamba, ‘Uyo wadya chakudya changa wang'anamuka kunihundukila.’ 19Ine nikukambilani vindhu ivi chipano vikali vosachokele, dala yapo siyachokele mkhulupilile kuti, ‘Ine nde mmeneyo.’ 20Zene nikukambilani, uyo wamlandila uyo wanituma wanilandila ine, ni uyo wanilandila ine wamlandila uyo wanituma.”
Yesu wakamba umo siwang'anamukidwe
Matayo 26:20-25; Maluko 14:17-21; Luka 22:21-23
21Yapo wadakamba yameneyo, Yesu wedadandaula mumtima, wadakamba popande kubisa, “Zene nikukambilani, mmojhi wanu siwaning'anamuke!”
22Ndiipo oyaluzidwa wake adapenyana, osakhozeletu kumjhiwa yani uyo wamkamba. 23Oyaluzidwa mmojhi, uyo Yesu wamamkonda kupunda, wadakhala pafupi ni Yesu. 24Ndiipo Simoni Petulo wadamfotokozela kwa chizindikilo, “Mfunjhe, wamkamba yani?”
25Oyaluzidwa mmeneyo, uku wanyikizila chidale cha Yesu, wadamfunjha, “Ambuye, yani uyo siwakung'anamukeni?”
26Yesu waadayangha, “Uyo sinimpache chibandhu cha bumunda icho sinisunjhe mmbale, nde mwene.” Ndipo wadatenga chibandhu cha bumunda, wadachisunjha mmbale, wadampacha Yuda, mwana wa Simoni Isikaliyote. 27Yuda yapo wadalandila chibandhu chimenecho, satana wadamulowa. Ndipo Yesu wadamkambila, “Ichoufuna kuchita, chichite chisanga!” 28Nambho padalibe waliyonjhe wa anyiyao adakhala pachakudya uyo wadajhiwa ndande yanji Yesu wadamkambila chimwecho Yuda. 29Pakuti Yuda wadali wosunga chuma hazina, wina amaghaniza kuti Yesu wamamkambila Yuda waghule ivo vifunikana pa phwando, kapina wakaapache kandhu osauka.
30Chimwecho Yuda pambuyo polandila chibandhu cha bumunda, wadatuluka kubwalo msanga. Ni idali usiku.
Malamulo ya Chipano
31Yuda yapo wadachoka, Yesu wadakamba, “Chipano Mwana wa Mundhu wapachidwa ulemelelo, ni Amnungu apachidwa ulemelelo mkati mwake.”
32“Ikakhala ulemelelo wa Mnungu wavunukulidwa kupitila Mwana wa Mundhu, ndiipo nawo Amnungu siauvunukule ulemelelo wa Mwana mkati mwake mwene wake, ni siwachite chimwecho mwamsanga. 33Wanawanga, nikali namwe kwa ndhawi yochepa pe. Simunifunefune, nambho chipano nikukambilani yayo naakambila achogholeli wa Ayahudi, ‘Uko nipita ine anyiimwe simukhoza kupita!’ 34Nikupachani lamulo la chipano, ngati umo nakukondelani anyiimwe, namwenjho mkondane mwachinawene kwa mwachinawene. 35Mkakondana, wandhu onjhe sajhiwe kuti anyiimwe nde oyaluzidwa wanga.”
Yesu walosa kuti Petulo siwamkane
Matayo 26:31-35; Maluko 14:27-31; Luka 22:31-34
36Simoni Petulo wadamfunjha Yesu, “Ambuye, mpita kuti?”
Yesu wadayangha, “Uko nipita siukhoza kunichota chipano, nambho siunichote pambuyo.”
37Petulo wadamkambila, “Ambuye, ndande yanji sinikhoza kukuchotani chipano. Ine nili tayali kumwalila ndande yanu!”
38Yesu wadayangha, “Bwanji, zenedi ulitayali kumwalila ndande ya ine? Uzene nikukambila, tambala wakali osalile, siunikane katatu kuti siunijhiwa.”

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Yohana 13: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល