Yohana 12

12
Maliya wamnyeka Yesu mafuta yo nunghila
Matayo 26:6-13; Maluko 14:3-9
1Zakhalalila siku sita kufikila phwando la Pasaka, Yesu wadafika ku Besania uko wamakhala Lazalo, uyo wadamuhyucha. 2Kumeneko adamkonjela chakudya cha ujhulo, ni Masa nde wamatumikila. Lazalo nayo wadali pomojhi ni wajha adakhala pamojhi ni Yesu. 3Ndiipo, Maliya wadatenga nusu lita ya mafuta ya Nalido ya mtengo wa ukulu, wadamnyeka Yesu mmyendo ni kumchangula kwa machichi yake. Nyumba yonjhe idakhala ni mnunghilo wa mafuta yameneyo. 4Ndiipo, Yuda Isikaliyote, mmojhi wa anyiwajha ochatila khumi ni awili uyo siwamng'anamuke Yesu, wadakamba, 5“Ndande yanji mafuta yaya siyadaghulidwe kwa ndalama iyo ilingana ni mkokolo wa mbowa uyo wamanga nyumba kwa siku miya mojha, ni kupachidwa osauka?” 6Yuda wadakamba chimwecho osati ndande ya kwaasamala osauka, nambho ndande wadali osunga azina, ni mnghungu, mala zambili wadaba muazinayo.
7Nambho Yesu wadakamba, “Msidamchaucha maye uyu! Msiyeni wayaike mafuta yaya ndande ya siku langa lozikidwa. 8Osauka muli nao siku zonjhe, nambho ine simukhala nane siku zonjhe.”
Ayahudi afuna kumpha Lazalo
9Ayahudi ambili yapo adavela kuti Yesu wadali ku Besania. Adafika osati ndande ya kumoona Yesu pe, nambho ndande ya Lazalo uyo Yesu wadamuhyucha kuchokela kwa akufa. 10Ndiipo ajhukulu waakulu adapanga kumpha Lazalo, 11chimwecho, ndande ya kuhyuka kwa Lazalo, Ayahudi ambili adakana kwavechela achogoleli wao, adamkhulupilila Yesu.
Yesu walowa ku Yelusalemu kokondwa
Matayo 21:1-11; Maluko 11:1-11; Luka 19:28-40
12Mawa lake gulu lalikulu la wandhu anyiyao adajha ku pwando la Pasaka, adavela kuti Yesu wali mnjila kujha ku Yelusalemu. 13Ndiipo adatenga ndhawi za zing'onozing'ono za mitengo ya mitende, ni kupita kumlandila, adakweza mvekelo ni kukamba, “Uelekelo! Wapachidwe mwawi uyo wakujha kwa jhina la Ambuye. Wapachidwe mwawi Mfumu wa Izilaeli!”
14Ndiipo Yesu wadamwona mwana wa phunda, wadakhala pamsana pake ngati umo yakambila malembo.
15“Simudaopa wandhu a ku Yelusalemu!
Vechelani, Mfumu wanu watokujha,
Wakwela mwana wa phunda!”
16Vindhu vimenevo oyaluzidwa wake samavijhiwe kuyambila mmayambo, Yesu yapo wadapachidwa ulemelelo, nde yapo adakumbukila kuti wadalembedwela yameneyo, ni wandhu amchitila iye.
17Wandhu anyiyao adalipo ndhawi iyo Yesu wamamtana Lazalo kuchokela kuchiliza, ni kumuhyucha, adamchochela umboni. 18Chimwecho gulu limenelo la wandhu lidamlandila, mate yake onjhe adavela kuti Yesu wadachita chizindikilo chimenecho. 19Ndiipo Afalisayo adakambilana, “Mvela? Sitikhoza kuchita kandhu! Penyani jhiko lonjhe la panjhi limchota iye.”
Yesu walosela nyifa ni kuhyuka kwake
20Kudaliko ni Agiliki wina pakati pa wandhu anyiyao adafika Ku Yelusalemu kulambila ndhawi ya phwando limenelo. 21Achameneo adamchata Filipo wa Ku Betisaida ya ku Galilaya, adakamba, “Olemekezedwa tifuna kumuona Yesu.”
22Filipo wadapita kumkambila Andulea, ni onjhe awili adapita kumkambila Yesu. 23Yesu wadakambila, “Ndhawi yopachidwa ulemelelo Mwana wa Adamu yafika! 24Uzene nikukambilani, mbewu ya ngano ikasiya kugwa pa ndhaka ni kufa ni kuphuka, ikhala mbeupe. Nambho ikafa ibala vipacho vambili. 25Uyo waukonda umoyo wake, siwautaize, uyo wauipila umoyo wake mujhiko lino la panjhi, siwauike ndande ya umoyo wa muyaya. 26Uyo wafuna kunitumikila lazima wanichate, ni paliponjhe yapo nili ine nde yapo sakhale ni atumiki wanga. Mundhu waliyonjhe uyo wanitumikila, Atate wanga sampache ulemu.”
Yesu waapembha Amnungu ndande ya nyifa yake
27“Chipano mtima wanga uchauchika, nikambe bwanji? Kapina nikambe, ‘Atate, munilamiche kuchoka ku mavuto yaya?’ Notho ndendande najha kuti nimwalile ndande ya wina. 28Atate, munipache ulemelelo wa jhina lanu.”
Ndiipo mawu kuchoka kumwamba yadaveka niyakamba, “Nalipacha ulemelelo jhina langa, ni sinilipachenjho ulemelelo.”
29Gulu la wandhu ilo lidaima pamenepo adavela mvekelo umeneo ujha, wina adakamba ntungulu wa mbhambe. Nambho wina adakamba, “Mtumiki wa kummwamba wa Amnungu wakamba nayo!”
30Nambho Yesu wadaakambila, “Ntungulu umeneo siudachokele ndande ya ine, nambho ndande yanu. 31Iyi nde ndhawi ya wandhu a jhiko la panjhi kulamulidwa, chipano mfumu wa jhiko lino siwalandidwe ulamulilo wake. 32Nane yapo sinipachikidwe pamtanda, siniaguze wandhu wonjhe ajhe kwanga.” 33Yesu wadakamba chimwecho kulangiza umo siwafele.
34Ndipo, gulu la wandhu lidamuyangha, “Ife tavela kuchokela mu Thauko lathu kuti Kilisito uyo wasanghidwa ni Amnungu siwakhale muyaya. Ukhoza bwanji, kukamba kuti Mwana wa Mundhu ifunika wapachikidwe pamtanda? Mwana wa Mundhu mmeneyo nde yani?”
35Ndiipo Yesu wadaakambila, “Dangalila limenelo likali namwe kwa ndhawi yochepa. Endekeleni kuyenda molinga kuli ni dangalila dala mdima siudakuphezani, pakuti uyo waenda mumdima siwajhiwa uko wapita. 36Ndhawi iyo muli ni dangalila khulupililani dandalila limenelo dala mkhale wana a amdangalila.”
Ayahudi akana kumkhulupilila Yesu
Yapo wadamaliza kukamba mawu yameneyo, Yesu wadachoka ni kupita kujhibisa.
37Atangati Yesu wadachita vizindikilo vonjhe ivi pachogolo pao, anyio sadamkhulupilile. 38Chimwecho mawu yayo wadakamba mlosi Isaya yadakwanila,
“Ambuye, yani wakhulupila uthenga wathu?
Ni nghongono zoombola za Amnungu walangizidwa yani?”
39Chimwecho sadakhoze kukhulupilila, ndande Isaya wadakamba pamalo pina,
40“Amnungu ayathimicha maso yao,
azichita njelu zao zidajhiwa
ni maso yao siyadapenya,
kujhiwa kwa mitima yao siadanikhulupilila,
nane nalamiche.”
41Isaya wadakamba mawu yameneyo ndande adauona ulemelelo wa Yesu, wadakamba nghani zake.
42Ata chimwecho, achogholeli ambili wa Ayahudi adamkhulupila Yesu. Nambho ndande ya Afalisayo, siadamvomele pa ndhandala kwa kuopa kuti siatopoledwe mnyumba yo pezanilana Ayahudi. 43Adakonda kuelekeledwa ni wandhu ni wandhu kupitilila kuelekeledwa ni Amnungu.
Yesu wadajha kwalamicha wandhu ajhiko la panjhi
44Ndiipo Yesu wadaakamba kwa mvekelo wa ukulu, “Uyo wanikhulupilila ine, siwanikhulupilila ine ndekha, nambho wamkhulupilila ni uyo wanituma. 45Uyo waniona ine wamuona uyo wanituma. 46Ine nde dangalila la chizimu, najha pajhiko la panjhi dala onjhe akhulupilila siadakhalila mumdima kwa kulepela kujhiwa uzene wa Amnungu. 47Uyo wayavela mawu yanga nambho siwayavomela, ine sinimlamula, ndande sinidajhe kulamula jhiko la panjhi nambho kuliombola. 48Walipo uyo siwamlamule uyo wayakana mawu yanga, mawu yajha nakamba nde yayo siyamlamule siku lothela. 49Ine sinidakambe kwa lamulo langa namwene, nambho atate yao anituma ni nde yao anilamula kuti nikambe chiyani. 50Nane nijhiwa kuti lamulo lake ni umoyo wa muyaya. Chimwecho ine nikambape yayo Atate anilamula niyakambe.”

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Yohana 12: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល