Vichito 8
8
1Chinchijha, Saulo wadakondwelechedwa ni kujha kuphedwa kwa Sitefano.
Saulo waavuticha wandhu amkhulupilila Kilisito
Kuyambila siku lijha wandhu adamkhulupilila Kilisito kujha ku Yelusalemu adayamba kuvutika kupunda. Wandhu wonjhe yawo adamkhulupilila Kilisito, kusiya atumwi, adamwazika ku malo yonjhe ya Yudea ni Samaliya. 2Wandhu yawo adamkhulupilila Amnungu adamzika Sitifano ni kumlilila kupunda.
3Ndhawi imeneyo Saulo wamatowavuticha wandhu yawo adamkhulupilila Kilisito. Wadapita kila nyumba niwaakwekweta wandhu yawo adamkhulupilila Kilisito, wachikazi ni wachimuna ni kwaaika mundende.
Filipo walalikila uthenga wabwino ku Samaliya
4Wajha wandhu adamkhulupilila Kilisito adamwazika, adalalikila ujha Uthenga Wabwino kila kumalo. 5Filipo wadachikilila ku mujhi wa Samaliya, wadaalalikila wandhu uthenga wa Kilisito. 6Wandhu yapo adamvela Filipo ni kuona ivo vozizwicha wadachita, adavechecha ivo wadakamba. 7Viwanda vidaachoka wandhu kwa kukweza mvekelo waukulu, wandhu wopuwala ni wovuwala adalamichidwa. 8Chimwecho, wandhu amujhi umenewo adakondwela kupunda.
9Padali mundhu mmojhi jhina lake Simoni uyo wamachita ufiti kwa ndhawi yaitali mu mujhi umenewo, niwaadabwicha wandhu wonjhe a Samaliya. Wadajhiona kuti iye ni mundhu wamkulu, 10ni wandhu ambili, waakuluakulu kwa waang'onoang'ono adamuvechecha ni kukamba, “Mundhu uyu wali ni mbhavu za Mnungu izo zitanidwa, ‘Mbhavu Zambili.’” 11Adamvechela iye ndande wadaanyenga kwa ndhawi yaitali kupitila ufiti wake. 12Nambho Filipo wadalalilkila Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mnungu ni jhina la Yesu Kilisito, wandhu wonjhe adakhulupilila ni adabatizidwa, waachimuna kwa waachikazi. 13Simoni nayo wadakhulupilila Uthenga Wabwino ni kubatizidwa. Wadamchata Filipo kila kumalo, niwadabwa vizindikilo ni vodabwicha ivo wadaviona.
14Atumwi yawo adali mu Yelusalemu adavela kuti wandhu a ku Samaliya avomela mau la Mnungu, chimwecho adaatuma kumeneko Petulo ni Yohana. 15Yapo adafika kumeneko, wadaapembhela wajha wandhu adamkhulupilila Yesu amlandile Mzimu Woyela. 16Mzimu Woyela udali ukali wosafika kwa waliyonjhe pakati pawo, nambho angobatizidwape kwa jhina la Ambuye Yesu. 17Petulo ni Yohana wadaasanjika manja wajha wandhu adamkulupilila Yesu, nawo adalandila Mzimu Woyela.
18Pamenepo Simoni wadajhiwa kuti kwakwasanjika manja ya Atumwi yao akhulupilila alandila Mzimu Woyela. Chimwecho wamafuna kwaapacha ndalama Yohana ni Petulo, 19niwakamba, “Munipache ni ine chinchijha mbhavu zimenezo, kuti kila mundhu uyo nimusanjika manja walandile Mzimu Woyela.”
20Nambho Petulo wadamuyangha, “Iwe ni ndalama zako mtaikile kutali, pakuti uganiza kuti ukhoza kugula mbhaso ya Mnungu kwa ndalama! 21Iwe siudalamulidwe kuchita utumiki uwu, pakuti mtima wako siudavomelezeke pamaso pa Mnungu. 22Chipano lapa machimo yako, ni upembhele kuti Ambuye akulekelele maganizo yako yoipayo. 23Niona wajhala njhanje kupunda ni wamangidwa ni machimo.”
24Ndiipo Simoni wadaayangha Petulo ni Yohana, “Munipembhelele kwa Ambuye kuti pa yonjhe mwayakamba silidanikomana ata limojhi.”
25Petulo ni Yohana yapo adamaliza kuchocha umboni wa kulalikila uthenga wa Ambuye, adabwelela ku Yelusalemu. Yapo amabwela adalalikila Uthenga Wabwino muvijhijhi vambili va Samaliya.
Filipo wambatiza wamkulu wa ku Isiopiya
26Ndiipo mtumiki wa kumwamba wa Ambuye wadamkambila Filipo, “Konjeka upite ku dela la kumwela, ku njila ya phululu iyo ichoka ku Yelusalemu kupita ku Gaza.” 27Chimwecho, Filipo wadakonjeka ni kupita. Yapo wadali mnjila, wadakomana ni mchogoleli mmojhi wa Isiopiya, uyo wadali towashi, uyo wadali woimilila chuma cha Kandake, mfumu wa mkazi wa ku Isiopiya. Wamkulu mmeneyo wamapita ku Yelusalemu kukalambila Mnungu. 28Yapo wamabwela kukhomo, wadakhala ngolo niwasoma chikalakala cha mlosi Isaya. 29Mzimu Woyela udamkambila Filipo, “Sendela pafupi ni ngolo ni uchogozane nayo.” 30Ndiipo Filipo wadaithamangila ni kuiwandiikila ijha ngolo ni wadamuvela wamkulu yujha niwasoma chikalakala cha mlosi Isaya. Filipo wadamfunjha, “Bwanji, uvananavo ivo usoma?”
31Wamkulu yujha wadayangha, “Nivananavo bwanji ngati palibe mundhu wonifotokozela ivo valembedwa?” Chimwecho wadamkambila Filipo wakwele mungolo mujha nikukhala pamojhi ni iye. 32Wamkulu mmeneyu wamasoma malembo yaya,
“Wadachogozedwa ngati mwana mbelele iyo ipita kuphedwa,
wadakhala chete ngati mwana mbelele yapo wadulidwa mabweya,
iye siwadachoche mvekelo ata pang'ono.
33Wadalengechedwa njhoni ni kumanidwa kuvomelezeka.
Palibe uyo siwakhoze kukamba kuusu mbadwa wake,
pakuti umoyo wake wachochedwa pajhiko.”
34Yujha wamkulu wadamfunjha Filipo, “Nipembha unikambile, uyu mlosi wakamba nghani za yani? Nghani zake mwenewake kapina nghani za mundhu mwina?” 35Ndiipo Filipo wadayamba kumkambila kupitila yajha malembo wamayasoma, pakumkambila Uthenga wa Yesu. 36Yapo amayendekela ni ulendo adafika malo yayo yadali ni majhi, yujha wamkulu wadakamba, “Pano pali majhi. Chindhu chanji icho sichinichekeleze nisidabatizidwa?” 37Filipo wadamuyangha, “Ngati siumkhulupilile Yesu kwa mtima wako wonjhe, siubatizidwe.” Yujha mundhu wadayangha, “Nikhulupilila kuti Yesu Kilisito ni Mwana wa Mnungu.”#8:37 Malembo ina yalibe mzele uno
38Wamkulu wadalamula kuti ngolo ijha iyimichidwe. Adachika, adabila mmajhi wonjhe awili, ni Filipo wadambatiza yujha wamkulu. 39Yapo adachuuka mmajhi, Mzimu wa Ambuye udamnyakula Filipo, nayo wamkulu yujha siwadamuonenjho, nambho wadayendekela ni ulendo wake uku niwakondwa. 40Filipo wadajhipheza wali mmujhi wa Azoto, yapo wamayenda mnjila wamalalikila Uthenga Wabwino mmijhi yonjhe mbaka ku Kaisaliya.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Vichito 8: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.