Vichito 6

6
Athandhizi saba a atumwi asanghidwa
1Yapo idapita ndhawi yochepa, chiwelengelo cha wandhu chimayendekela kukula kupunda, padachokela madandaulo pakati pa oyaluzidwa a Yesu yao amakamba mkambo ya chigiliki ni oyaluzidwa a Yesu yao amakamba mkambo wa Chiebulaniya, kuti wachikazi wao yawo asiidwa ni wachimuna wao adaiwalidwa pa kugawa chakudya cha kila siku. 2Atumwi khumi ni awili wajha adaasonghanicha pamojhi oyaluzidwa wonjhe ni kukamba, “Siikhala bwino kwa ife kusiya kuliuzila mau la Mnungu kuti tigawe vakudya. 3Chimwecho achabale, sanghani wandhu saba pakati panu yawo ajhiwika kuti ali ni ekima, ali ni ukhalo wa bwino ni yawo ali ni Mzimu Woyela, kuti taaike aimilile njhito imeneyo. 4Ife taachinawene wake, sitikhale ni ndhawi yambili kwaapembha Amnugnu ni kuchita njhito ya kulalikila.”
5Wandhu wonjhe adakondwela ni vijha vidakambidwa ni atumwi wajha, nawo adamsangha Sitifano, uyo wadajhala chikhulupililo ni Mzimu Woyela. Adamsanghanjho Filipo, ni Pulokolo, ni Nikanoli ni Timoni ni Palimena ni Nikolao kuchokela ku Atiokia uyo wadang'anamuka kulowa mchikhululipililo cha Ayahudi. 6Adaimika wandhu ameneo pachogolo pa atumwi, adaapembhela ni kwapacha mwawi kwa kwaikila manja.
7Mau la Mnungu lidayendekela kuenela kupunda. Wandhu adamkhulupilila Yesu mu mujhi wa Yelusalemu adayendelekela kuchuluka, ni gulu lalikulu la ajhukulu adamkhulupilila Kilisito.
Sitifano wagwilidwa
8Sitifano, mundhu uyo wapachidwa mwawi ni Mnungu ni kujhala mbhavu, wadachita vodabwicha ni vizindikilo vambili pakati pa wandhu. 9Nambho ata chimwecho, adachokela wandhu wina kuti achuchane ni Sitefano. Akumojhi wa wandhu ameneo adachokela ku nyumba yokomanilana Ayahudi iyo itanidwa, Nyumba ya ufulu. Wandhu ameneo adachokela ku Kilene ni a Isikandiliya, wandhu wina adachokela ku Kilikiya ni ku Asiya. 10Nambho Mzimu Woyela udampacha Sitifano ekima, chimwecho yapo wamakamba, anyiiwo siadakhoze kumkhoza. 11Chimwecho adaaguza wandhu kuti akambe, “Ife tidamuvela niwakamba mawu yomtukwana Musa pamojhi ni Mnungu!” 12Pokamba chimwecho, wadaakhwilizila wandhu, azee ni oyaluza a thauko, adapita kumgwila Sitefano ni kumpeleka pachogolo pa bwalo la milandu. 13Ndipo adajhanawo wandhu kuti akambe mthila niakamba, “Mundhu uyu wapunda kuendekela kuitukwana nyumba yoyela ya Mnungu ni thauko la Musa. 14Tidamvela niwakamba kuti uyu Yesu wa ku Nazaleti siwaiwanange nyumba ya Mnungu ni kung'anamula mwambo yonjhe yayo tidapachidwa ni Musa.” 15Wandhu wonjhe yawo adakhala pa bwalo la milandu pajha, adampenyechecha Sitifano, adaona nghope yake niinga'azikila ngati nghope ya mtumiki wa kumwamba wa Amnungu.

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Vichito 6: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល