Vichito 27
27
Poolo wapelekedwa ku Loma
1Yapo adalamula kuti sitimange ulengo mbaka ku Italiya kwa njila ya nyanja, adamchata Poolo pamojhi ni amndende wina, panjhi pa ulonda wa Yulio uyo wadali pa gulu la asikali ilo limatanidwa, “Gulu la Mfumu wamkulu wa Ku Loma.” 2Tidayamba ulendo kwa kukwela sitima iyo imachokela ku mujhi wa Adilamitio, iyo imamanga ulendo kwa kupitila madoko ya mujhi wa Asiya. Alisitaliko, mundhu wa ku Makedoniya uyo wamachokela ku Sesalonike wadali pamojhi ni ife. 3Siku lochatila tidafika kumujhi wa Sidoni. Juliyasi wadamchitila Poolo vabwino kwa kumlola waone abwenji wake ni kuti ampache ivo wamafuna. 4Tidachoka pajha ni kupita pafupi ni chilumba icho chitanidwa Kipulo ndande mbhepo imapula niitichekeleza. 5Yapo tidayomboka nyanja iyo idali mdela la Kilikiya ni Pamfiliya, tidafika mmujhi wa Mila, uwo uli mkati mwa jhiko la Lukia. 6Yapo tidafika kujha, wamkulu wa asikali wadapeza sitima iyo imachokela mu mujhi wa Isikandiliya iyo imapita ku Italiya, ni wadatikweza mmenemo.
7Tidayenda pang'onopang'ono ulendo wathu kwa ndhawi ya siku zambili, ni kwa mavuto tidafika ku mujhi wa Nido kwa mavuto. Ndande mbhepo idali ikali niichekeleza, Sitidakhoze kuyendekela kupitila njila imeneyo, chimwecho tidayendekela ni ulendo kupitila kudela la kumwela kwa chilumba cha Kilete, pafupi ni Salumone. 8Tidayenda mmbhepete kwake pang'ono pang'ono mbaka tidafika pa malo yamojhi yayo yatanidwa, “Dooko Labwino,” ilo lidali pafupi ni mujhi wa Liseya.
9Ndhawi yaitali idalowa, ni ulendo wathu mnyanja udali wa mavuto, ndande ndhawi imeneyo idali pambuyo pa siku lo manga kudya. Chimwecho Poolo wadaonya niwakamba, 10“Achaabale wanga, niona kuti ulendo uwu sikukhale ni mavuto yambili. Osati kwa katundupe nambho kila kandhu yako kali mkati mwake, ni umoyo wathu ukhoza kutaika.” 11Nambho mchogoleli wa gulu la asikali wadavomela mwambo wa woyendecha sitima, pamojhi ni mwene sitima, ni kusiya kuvela ivo wadakamba Poolo. 12Pakuti dooko limenelo silidali pamalo pabwino, wandhu ambili adalamula tiendekele ni ulendo, ni kukala kumeneko nyengo yo zizila. Ikakhozeka mbaka ku Foinike ku Dooko la Kilete iyo ipita kuvuma ni kumpoto ni adakakhoza kukala kumeneko nyengo yo zizila.
Mwela uvundula mnyanja
13Ndiipo mbhepo yabwino idayamba kuputa kuchokela kumwela, ni wandhu adaganiza kuti apata mbhepo iyo imaifuna, Chimwecho adaguza ndondowe ni kuyendekela ulendo ni kufika mmbhepete mwachilumba cha Kilete. 14Nambho ikali yosapite dhawi ya itali mbhepo yambhavu kupunda iyo itanidwa “Mbhepo ya kuvuma” kuchokela kujha chilumba cha Kilete idayamba kupita. 15Mbhepo idaibula ijha sitima, ni ndande siidakhoze kulimbana ni mbhepo ijha, tidaiisiya sitima ibwanyizilidwe kujha mbhepo imapita. 16Tidapelekedwa chisanga mbaka pachilumba chaching'ono icho chitanidwa Kauda. Tidakhoza kuuombola bwato wa ung'ono uwo udali msitima kwa kulimba. 17Opota njhito msitima adauguza bwato ujha ni kuulovya msitima, adaumanga pamojhi ni sitima. Adaopa kuti sitima idakakhoza kupakamwa kumchenga wambili uwo uli doko la Libiya. Chimwecho adachicha ndondowe ni kuisiya sitima kuti ijhisewa ni mbhepo. 18Mbhepo idayendekela kuputa kwa mbhavu mbaka ni kuichita sitima ijhindenganga, mawa lake wandhu adalamula kutaya vindhu vakumojhi mmajhi, 19ni siku ilo lidachatila adalamula kutaya vichulo va sitima mmajhi kwa manja yao achinawene. 20Kwasiku zambili tidakoze kuliona jhuwa kapina ndhondwa, ni mbhepo idayendekela kuomba kwa mbhavu. Mbaka tidataya mtima wa kukhalnjho amoyo, timaganiza timwalila.
21Yapo tidakala kwa ndhawi yaitali popande kudya chakudya, Poolo wadaima ni kukamba, “Achaabale wanga, mudakanivechela yapo nidakukambilani kuti tisadaendekela ni ulendo kuchoka ku Kilete sitima siidakawanangika ni sitidakataya makatundu. 22Nambho nikupembhani kuti, limbani mtima. Palibe uyo siwamwalile ata mmojhi, sitimape nde iyo siiwanangike. 23Mnungu yujha uyo ine ni wake ni uyo nimtumikila, jhulo usiku wadamtuma mtumiki wa kumwamba wa Mnungu, wadanichokela, 24nayo wadakamba, ‘Poolo usadopa, pakuti ufunika uime pachogolo pa Mfumu wamkulu ku Loma. Amnungu akuchitila ubwino ndande yaiwe Mnungu siwaombole wandhu wonjhe ali paulendo pamojhi niiwe kuti sadayomwa.’ 25Chimwecho limbani mitima, pakuti nimkhulupilila Mnungu kuti siikhale ngati umo wanikambila. 26Nambho sitima asiipakamwe mbaka mbhepete mwa chilumba china.”
27Masiku khumi ni yanayi tidali tikali kubwanyizidwa ni mbhepo mnyanja ya Meditelaniya. Usiku pakati woyendecha sitima amaganiza tili pafupi ni pamtunda. 28Chimwecho anyiiwo adaponya chingwe icho adamanga chichulo cholemela. Adaona kuti kunyowa kwake ni meta alubaini. Pambuyo adapimanjho ni kupata meta ishilini ni sita. 29Tidaopa kuphwanyidwa ku myala, adachicha ndondowe zinayi kumbuyo kwa sitima, uku niapembhela kuti kuche msanga. 30Ndiipo woyendecha amafuna kutawa, adachicha ujha bwato udali msitima mmajhi uku niajhinamiza kuti apita kuchicha ndondowe kuchogolo kwa sitima. 31Nambho Poolo wadamkambila wamkulu wagulu la asikali ni asikali wake, “Ngati wandhu anyiyawa saakhalila musitima, simukhoza kuomboka.” 32Ndiipo asikali adadula chingwe ni kuusiya bwato ujhisewa.
33Mmachelo, Poolo wadaatila mtima wandhu wonjhe kuti adye chakudya, niwakamba, “Kwa masiku khumi ni yanayi mwakhala mandha, ni simudadye kandhu mbaka ndhawi zino. 34Chipano nikupembhani mudye chakudya kuti chikuthangatileni kukhala amoyo. Palibe ata mmojhi pakati panu uyo siwapwetekedwe.” 35Pambuyo pa kukamba yameneyo, Poolo wadatenga bumunda, wadamuyamika Mnungu pachogolo pao, wadalibandhula ni kuyamba kudya. 36Ndiipo wonjhe adatilidwa mtima, adayamba kudya chakudya. 37Yapo tidali mkati mwa sitima, taonjhe pamojhi tidalipo wandhu mia mbili ni sabini ni sita. 38Kila yapo wadadya ni kukhuta, adataya ngano ni vakudya vakumojhi mnyanja dala kuchepecha kulemela kwa sitima.
Mwela uwananga sitima
39Yapo kudacha, siadalijhiwe jhiko lijha. Adaona dooko lili ni guba adalamula kuipakamwiza sitima pamchenga. 40Chimwecho adadula vingwe ni kuzisiya ndondowe mnyanja. Pamenepo adamasula vingwe ivo vidamanga mshikano, adaimika thanga la kuchogolo kuti apite kumtunda. 41Nambho sitima idabwanyizidwa ni majhi ni kufika pamalo yapo imapezana myeza iwili, kuchogolo kwa sitima kudapakamwa pa mchenga ni siidakhoze kuyendanjho. Nambho kumbuyo kwa sitima kudayamba kuwanangika ndande ya yajha mafunde.
42Asikali wajha adapanga kuwapha omangidwa kwakuopa kuti akhoza kutawa kwa kusambilila. 43Nambho wamkulu wa asikali siwamafune kuti Poolo waphedwe. Chimwecho wadaakaniza asikali wajha kuti wasadaapha. Wadaakambila wandhu yawo akhoza kusambilila kuti abile mmajhi ni kupita kumtunda. 44Niwina adakakhoza kufika kumtunda kwa mbao kapina vidufya va sitima ivo vidaduka. Chimwecho wandhu wonjhe adafika pamtunda kwa mtendele.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Vichito 27: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: