Vichito 24
24
Ayahudi ampacha mlandu Poolo
1Pambuyo pa masiku yasano, mjhukulu wamkulu Ananiya wadafika ku Kaisaliya pamojhi ni azee akumojhi ni mundhu mmojhi uyo wamajhiwa thauko la Musa uyo wamatanidwa Tetulo. Anyiiwo adajha kwa Felikisi ni milandu ya Poolo. 2Ndiipo Poolo wadatanidwa mkati, Tetulo wadayamba kuchocha milandu yake niwakamba,
“Wolemekezeka Felikisi, mwatichogoza bwino niife tikhala kwa mtendele masiku yonjhe, mwachita mang'anamukilo ya yakulu kwa pindhu la jhiko lathu. 3Ndhawi zonjhe ni kila kumalo tayalandila yaya yonjhe kwa chimwemwe ni tikuyamikani kupunda imwe. 4Sinifuna kutaya ndhawi yanu yambili, nambho nipembha kuti mtiveleko pang'aono. 5Tavumbula kuti mundhu uyu ni wochaucha, uyo wachochelela chiwawa pakati pa Ayahudi kujhiko lonjhe lapanjhi. Iye ni mchogoleli wa gulu la Anazaleti, 6wamayesanjho kuchita vindhu ivo sivifunika pa Nyumba ya Mnungu, nambho tidamkaniza. Timafuna kumlamula kwa umo likambila lamulo lathu. 7Nambho Lisiya wamkulu wa asikali, wadajha, wadamlanda Poolo kwa mbhavu kuchokela mmanja mwathu. 8Ndiipo wadalamula wajha adampacha mlandhu ajhe pachogolo pako. Ukamfunjha mundhu uyu iwe umwene. Siuone kuti icho tikamba kwa iye ni chazene.” 9Ayahudi wina adavomela ni kunena kuti ivo wapachidwa mlandhu Poolo ni vazene.
Poolo wajhiteteza pachogolo pa Felikisi.
10Ndiipo wamkulu wa jhiko wadamlangiza chizindikilo kuti Poolo wayambe kukamba. Naye Poolo wadakamba,
“Nijhiwa kuti imwe mwakhala alamuli wathu kwa vyaka vambili, chimwecho nijhiteteza kwa chimweme pachogolo panu. 11Mkhoza kuchimikiza kuti siyadafike masiku khumi niyawilipe kuyambila yapo nidapita kupembhela ku Yelusalemu. 12Ayahudi siadanipheze ine ninichuchana ni mundhu waliyonjhe mu Nyumba ya Mnungu. Saadanipheze ninachocholela wandhu kuchita chiwawa mu nyumba zokomanilana Ayahudi, kapina pamalo paliponjhe mmujhi muno. 13Sakoza kukuchimizila uzene wa vindhu ivo anipachila mlandu kwaiwe. 14Icho ine nivomela ni ichi, ine nimlambila Mnungu wa achaatate wathu, ni kukhala kuchatana ni njila iyo anyiyawa Ayahudi aitana kuti njila ya mayaluzo ya mthila. Nambho nikhulupililanjho mu kila chindhu icho chalembedwa ni Thauko ni chijha icho chalembedwa mu vikalakala va alosi. 15Ine nili ni chikhulupi ngati icho alinacho wandhu anyiwa, kuti wandhu yawo avomelezeka pachogolo pa Mnungu ni oyipa wonjhe sahyukichidwe. 16Chimwecho masiku yonjhe niyesa kukhala ni mtima wa bwino pachogolo pa Mnungu ni wandhu wonjhe.”
17“Pambuyo pa kukhala kutali kwa vyaka vambili, nidabwela ku yelusalemu dala natangatile wandhu ajhiko langa, tandizo limenelo hasa kwa osauka ni kuchocha njhembe kwa Mnungu. 18Yapo nidamaliza kujhiika bwino pachogolo pa Mnungu kwa chikalidwe cha kulambila, ndeyapo adanipeza Mnyumba ya Mnungu. Sikudalipo ni gulu la wandhu pamojhi ni ine ni sinimakwilizile wandhu kuchita chiwawa. 19Nambho kudali ni Ayahudi wina yawo adachokela ku Asiya, ameneo nde yawo amafunika akhale pano pachogolo panu kuchocha mlandu nikukamba ngati kuli ni chilichonjhe choipa icho nachita, 20kapina waalole anyiyawa aima pano akukambileni ngati apheza cholakwa yapo adaniimicha pa bwalo lao lalikulu la milandu. 21Yangho limojhi ilo nidaayangha yapo nidali pachogolo pao ni ili, ‘Munipacha mlandu lelo ndande nikhulupilila kuti wandhu siahyuke.’”
22Ndiipo Felikisi, mundhu uyo wamaijhiwa bwino Njila ijha, wadaimicha mlandu ni kukamba, “Lusiya Wamkulu wa asikali yapo siwafike pano nde yapo sinilamule chochita.” 23Ndiipo wadamlamula mkulu wa gulu la asikali wamtenge Poolo ni kumlonda, ndiipo yujha mkulu wa asikali wadalamula poolo watengedwe ni kulondedwa, nambho walolezedwe kuchita vindhu vina pang'ono ni acha bwenji wake sadakanizidwa kumpacha icho wachifuna.
Felikisi ni Dulusila avechela mlandu wa Poolo
24Yapo yadapita masiku yochepa Felikisi wadafika pamojhi ni mkazi wake Dulusila, uyo wadali Muyahudi, wadaatuma wandhu kuti amtane Poolo ni kumvela ngati umo wadakambila mate ya kumkhulupilila Yesu Kilisito. 25Nayo Poolo yapo wamakamba nghani zo vomelezeka ni kujhichekeleza, ni lamulo ilo likujha, Felikisi wadali ni mandha ni kukamba, “Basi, ukhoza kuchoka! Yapo sinikhale ni ndhawi sinikutane” 26Ndhawi imweijha Felikisi wamalindilila kuti Poolo siwampache chindhu dala wamsiilile. Chimwecho wamamtana kila nyengo ni kukamba nayo.
27Pambuyo pa vyaka viwili, Polikio Fesito wadalowa muulamulilo pamalo pa Felikisi, nambho pakuti Felikisi wamafuna kwaakondwelecha Ayahudi, wadamusiya Poolo mundende.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Vichito 24: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.