Vichito 21
21
Poolo wapita ku Yelusalemu
1Yapo tidaalaila, tidakwela sitima nikuyamba ulendo kupita ku mujhi wa Kosi. Mawa lake tidafika ku mujhi wa Lode, ni kuchokela kumeneko tidapita ku mujhi wa Patala. 2Kumeneko tidaikomana sitima iyo imayomboka kupita ku Foneike. Chimwecho ditakwela ni kuyamba ulendo. 3Yapo tidachiona chilumba cha Kipulo, tidachizungulila ni kuchipita kubendeka la kumwela, tidayendekela mbaka ku Siliya, kumeneko tidakweza pa dooko la Tilo, yapo sitima ijha imafunika ipakulidwe katundu wake. 4Tidaakomana ochatila a Yesu kumeneko, tidakhala pamojhi nawo kwa ndhawi ya jhuma imojhi. Ochatila ameneo amakamba kwa mbhavu za Mzimu Oyela, adamkambila Poolo kuti siwadapita ku Yelusalemu. 5Nambho ndhawi yathu yokhala nianyiiwo yapo idatha, tidachoka ni kuyendekela ni ulendo wathu. Ochatila wonjhe pamojhi ni achakazao ni wana wao adapita pamojhi ni ife kunyanja, uko taonjhe tidapembhela. 6Ndiipo tidalailana, nafe tadayendekela ni ulendo kwa Sitima, anyiiwo adabwelela kukhomo.
7Tidayendekela ni ulendo wathu kuchokela ku Tilo ni tidafika ku Tolemai kwa sitima, tidaalonjela abale wathu okhulupilila ni kukhalanao kwa siku limojhi. 8Siku lochatila tidayendekela ni ulendo ni kufika ku mujhi wa Kaisaliya. Kujha tidakhala kwa mlaliki mmojhi uyo wamatanidwa Filipo, mmojhi wa wandhu wajha saba adasanghidwa. 9Filipo wadali ni anamwali mbeta anayi yawo adali alosi. 10Yapo tidakhala kujha kwa masiku yochepa, wadachika mlosi mmojhi kuchokela ku Yudea, jhina lake Agabasi. 11Wadafika kwaife nikutenga lamba la Poolo ni kujhimanga mmanja ni mmiendo mwake niwakamba, “Mzimu Woyela wakamba, ‘Umu nde umo Ayahudi aku Yelusalemu siammangile mundhu mwene lamba ili ni kumpeleka kwa wandhu osati Ayahudi.’”
12Yapo tidavela mau yameneyo ife tidampembha Poolo wasadapita ku Yelusalemu. 13Nambho Poolo wadayangha, “Mfuna kunigoola mtima kwa misozi yanu? Ine nili tayali osati kumangidwa mndendepe kumeneko ku Yelusalemu, nambho nili tayali ata kupedwa ndande ya Ambuye Yesu.”
14Yapo tidalepela kumdyelekezela kuti wasapita ku Yelusalemu, tidamsiya ni tidakamba, “Ambuye achite ngati umo afunila.”
15Pambuyo pakukhala masiku yochepa kujha, tidakonjeka ni kupita ku Yelusalemu. 16Wokhulupilila wina kuchokela ku Kaisaliya adachogozana ni iife ni kutipeleka ku nyumba ya Mnasoni, uyo timapita kukhala naye kwa masiku yochepa. Iye wadali mundhu wa ku Kipulo, wadali mmojhi wa oyaluzidwa wa kalekale.
Poolo wamuyendela Yakobo
17Yapo tidafika ku Yelusalemu abale okhulupilila anjhatu adatilindila kwa chimwemwe. 18Siku lakawili Poolo wadapita ni ife kukambana ni Yakobo, ni azee onjhe agulu la Wandhu amkhulupilila Kilisito adalipo pampajha. 19Pambuyo pa kwalonjela, Poolo wadayamba wadakambila mokwanila vonjhe ivo vidachitika kwa wandhu osati Ayahudi kupitila utumiki wake. 20Wajha wandhu yapo adavela nghani zimenezo adamtamanda Mnungu. Ndiipo adamkambila Poolo, “Mbale wathu, ukhoza kuona unyinji wa Ayahudi yawo akhulupila, ni saino wonjhe achata thauko la Musa. 21Nambho avela kuti iwe wayaluza Ayahudi akhala ni wandhu yawo osati Ayahudi, asagwila thauko la Musa ni saadaachita wana wao mdulidwe ni sadachata chikhalidwe cha Ayahudi. 22Chipano sikhale bwanji? Pakuti wandhu sapate nghani kuti iwe wathokujha pano pa Yelusalemu. 23Chipano chita ngati umo tikukambila, wandhu anayi pakati pathu ayika chilanga cha kumchochela Mnungu. 24Ulunjane nawo ni kwalipila vilanga vawo ivo adalumbila kwa Mnungu ukaachochele yonjhe yawo yafunika ndiipo ametedwe machichi yawo. Akachita chimwecho, sajhilangize achinawene kuti nghani zako izo avela ni zamthila, ni saajhiwe kuti iwe ni mundhu uyo ugwila Thauko. 25Nambho wajha wandhu akhulupilila, yawo osati Ayahudi, taalembela kalata kwaakambila kuti saadadya chakujha chilichonjhe icho chapelekedwa kwa vifanifani, kapina kudya mwazi, kapina nyama iliyonjhe iyo yapopotoledwa, ni asadachita chigololo.”
26Chimwecho mawa lake, Poolo wadaatenga wandhu wajha ni kukhala dala akhoze kuvomelezeka kwa chikalidwe chakulambila. Ndiipo wadalowa mu Nyumba ya Mnungu kupeleka uthenga dala masiku yao ya kukhala kuvomelezeka kwa mapembhelo yakwanile, ni njhembe idakachochedwa ndande ya kila mmojhi wao.
Poolo wagwilidwa
27Masiku saba yapo yamawandikila kutha, Ayahudi wina yawo adachokela ku mujhi wa Asiya adamuona Poolo pa Nyumba ya Mnungu. Adalikhwilizila gulu lonjhe amipile Poolo ni kumgwila. 28Adabula phokoso niakamba, “Anyiimwe wandhu a ku Izilaeli, tithangatilieni! Uyu nde mundhu uyo wapita kila kumalo kuyaluza mayaluzo yayo yachuchana ni wandhu aku Izilaeli ni yayo yachuchana ni Thauko la Musa ni Nyumba ya Mnungu. Ata chimwecho waayaluza wandhu anyiyao asati Ayahudi pa Nyumba ya Mnungu ni kupadecha pamalo yoyela!” 29Anyiiwo adakamba chimwechi ndande adamuona Tilofimo, mundhu wa ku Efeso, uyo wadali mu mujhi pamojhi ni Poolo, niaganiza kuti Poolo wadamulovya pa Nyumba ya Mnungu.
30Wandhu wonjhe adakwiya kupunda, adamgwila Poolo ni kumchocha kubwalo kwa mujhi. Pamwepo vicheko va nyumba ya Mnungu vidachekedwa. 31Gulu lijha la wandhu yapo limafuna kumpha Poolo, nghani idamfikila wamkulu wa asikali wa ku Loma kuti, mujhi wonjhe wa Izilaeli wajhala chiwawa. 32Ndhawi imweyo wamkulu wa asikali yujha wadaatenga waasikali anjake, ni waakulu amagulu miyamiya ya asikali. Wandhu yapo adamuona wamkulu wa asikali pamojhi ni asikali wake, adasiya kuchita chiwawa. 33Wamkulu wa asikali yujha wadapita yapo wadali Poolo ni kumgwila, wadalamula kuti wamangidwe maunyolo yawili. Ndiipo wadaafunjha, “Uyu ni yani, ni wachita chiyani?” 34Wandhu wina mgulu mujha adabula phokoso, wina amakamba ichi, ni wina amakamba chijha. Wamkulu wa asikali yujha yapowadaona siwakhoza kujhiwa uzene ndande ya chiwawa chijha, wadalamula kuti Poolo wapelekedwe ku nyumba ya maasikali. 35Yapo adafika pa makwelelo yolowela mnyumba ya asikali, asikali adalamula kumnyakula Poolo ndande chiwawa cha wajha wandhu chidali chahikulu. 36Pakuti gulu la likulu limachata uku niabula phokoso niakamba, “Umphele uko! Umphele uko!”
Poolo watojhiteteza
37Yapo amamlovya Poolo mu nyumba ya asikali, Poolo wadampembha wamkulu wa asikali, “Bwanji, nikhoza kukukambila kalikonjhe?”
Wamkulu wa asikali yujha wadamfunjha, “Bwanji, ujhiwa kukamba Chigiliki?” 38“Bwanji, iwe osati Mmisili yujha wadayambicha chiwawa masiku yathaya, niwachogoza wandhu akupha elufu zinayi yawo adali ni vida vanghondo mphululu?”
39Poolo wadayangha, “Ine ni Myahudi uyo nabadwila ku Taso ya ku Kilikiya, mundhu wa mmujhi uwo ujhiwika kupunda. Chonde, nilole kuti nikambe ni wandhu.”
40Yapowadapata chilolezo kuchoka kwa yujha wamkulu wa asikali, Poolo wadaima pa makwelelo ni kukweza jhanja kuti wandhu akhale chete. Nawo adakhala chete ni Poolo wakamba ni wandhu kwa mkambo wa Chieblaniya.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Vichito 21: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: