Vichito 19
19
Poolo walalikila wandhu ku jhiko la Efeso
1Apolo yapo wadali mmujhi wa Kolinto, Poolo wamayendela mijhi ina, wadafika ku Efeso. Yapo wadafika kumeneko, wadakomana ni wandhu wina yawo adaakhulupila Ambuye, 2wadaafunjha, “Bwanji, mudamulandila Mzimu Woyela yapo mudamkhulupilila Yesu?”
Ochatila wajha adamuyangha, “Notho, sitidavelepo kuti kuli Mzimu Woyela.”
3Ndiipo Poolo wadaafunjha, “Bwanji, mudabatizidwa kwa ubatizi wanji?”
Anyiiwo adayangha, “Ubatizi uwo wadayaluza Yohana.”
4Poolo wadakamba, “Ubatizi uwo wamayaluza Yohana udali wa kulapa, wadaakambila wandhu amkhulupilile iye uyo wakujha pambuye pake, yaani Yesu.”
5Ochatila achameneo yapo adavela chimwecho, adabatizidwa mujhina la Ambuye Yesu. 6Poolo wadaasanjika manja, ni Mzimu Woyela adachikila anyiiwo, ni kuyamba kukamba mikambo yachilendo ni adayamba kuuzila Uthenga wa Mnungu. 7Wandhu achamenewo adali ngati waachimuna khumi ni awili.
8Kwa ndhawi ya mwezi itatu, Poolo wadalowa mu nyumba yokomanilana Ayahudi, wamakambila wandhu aukhulupilile Ufumu wa Mnungu. 9Nambho wina wao saadavomele ivo wamakamba Poolo. Adakana kuukhulupilila uthenga wa Yesu. Wina adakamba mau yoipa pagulu la wandhu ndande ya kwaakhulupilila a Ambuye Yesu. Chimwecho Poolo wadaasiya ni wadaatenga wokhulupilila, ni kila siku wamakambilana ku chumba cho yaluzila cha Tulano. 10Nghani izi zidayendekela kwa vyaka viwili, mbaka wandhu wojhe yawo amakhala ku Asiya pamojhi ni Ayahudi ni wandhu yawo osati Ayahudi adavela mawu la Ambuye.
Wana wachimuna a Sikewa
11Munugu wadachita vodabwicha vambili kupunda kupitila Poolo. 12Wandhu adatenga njhalu ni vitambaa ni kupitanavo kwaapacha wodwala wao, ni wodwalao adalama ni viwanda vidaachoka. 13Ata chimwecho Ayahudi wina amaingwa uku ni uko niayesa kwaachocha wandhu viwanda. Ayahudi achamenewo adayesa kutumila jhina la Ambuye kuvichocha viwanda. Anyiiwo adavikambila viwanda, “Kwa jhina la Ambuye Yesu uyo walalikidwa ni Poolo, tikulamulani mchoke.” 14Yawo amachita chimwecho adali wana saba a mundhu mmojhi mchogoleli wa ajhukulu waakulu, jhina lake Sikewa.
15Nambho chiwanda chidaayangha, “Nimjhiwa Yesu, nimjhiwanjho Poolo, nambho anyiimwe ni achiyani?”
16Ndiipo mundhu yujha wadali ni viwanda wadaahundukila kwambhavu ni kwaakhoza wonjhe. Wadaapweteka kupunda ni kuzing'amba njhalu zao. Chimwecho anyiiwo adathawa mnyumba mujha uku ali maliseche ni mabala. 17Ayahudi ni wandhu yawo osati Ayahudi yawo amakhala ku Efeso adajhiwa nghani izi, ni wonjhe adaopa, ni jhina la Ambuye Yesu lidapachidwa ulemu waukulu. 18Wandhu ambili yawo adamkhulupilila Yesu adayamba kulapa machimo yao padanga niakamba vindhu vonjhe voipa ivo adavichita. 19Wina yawo amachita ufiti kumbuyoko, adalapa, adatenga vikalakala vao va ufiti ni kuvibucha pamaso pa wandhu wonjhe. Vikalakala vimenevo vidali va mtengo waukulu. 20Umu nde umo mau la Ambuye lidaendekela kuwanda kwa mbhavu, nikukhala ni mbhavu kupunda.
Wandhu akangana ku mujhi wa Efeso
21Yapo yadatha yameneyo, Poolo wadalamula kupita ku Yelusalemu. Wadamanga ulendo kupitila mijhi ya Makidoniya ni Akaya, niwakamba, “Nikathofika ku Yelusalemu, ifunikanjho nipite ku Loma.” 22Poolo wadali ni athandizi wake awili, Timoseo ni Elasito. Wadaatuma amchogolele kupita ku Makidoniya. Nambho iye wadakhalila ku Asiya kwa ndhawi yochepa.
23Nyengo imeneyo kudachokela mkangano waukulu ku Efeso ndande ya nghani ya Ambuye. 24Kudali mundhu mmojhi uyo watanidwa Demetilio wosula madini ya ndalama ni kukonja viboliboli ivo vilingana ngati nyumba ya nungu wa mkazi uyo wamatanidwa Atemi. Wandhu yawo amachita njhito imeneyo imaalovyela ndalama zambili kupunda wosulawo. 25Dametilio wadaasonghanicha pamojhi wandhu wina yawo amachita njhito ngati yake ni kwakambila, “Anyiimwe mwachanjanga mujhiwa kuti kupata kwathu kuchokana ni njhito iyi. 26Nambho penyani icho wachita mundhu uyu. Iye wakamba kuti minungu iyo yakonjedwa ni wandhu osati minungu ya zene ata pang'ono. Iye wadyelekezela wandhu ambili mu Efeso ni Asiya kulambila minungu yawo. 27Chimwecho, mnungu wa wathu wa Atemi siwadeleldwe. Osati chimwechope, nambho ata nyumba ya Atemi siideleledwe. Mnungu uyo walambilidwa ni wandhu wonjhe mu Asiya ni jhiko lonjhe lapanjhi, ulemelelo wake siuchochedwe.”
28Yapo adavela chimwecho, wandhu adakwiya kupunda, adabula phokoso niakamba, “Atemi, nungu waku Efeso nde wamkulu!” 29Pampajha mujhi wonjhe udajhala chiwawa, adamgwila Gayo ni Alisitako, wandhu aku Makidoniya yawo adali pa ulendo ni Poolo, adaapeleka kwa chisanga pa malo yapo wandhu a mmujhi akomanilana. 30Poolo wamafuna kulowa pakatikati pa gulu la wandhu, nambho wandhu yawo amkhulupilila Yesu adamkaniza. 31Anjake awandhu waakulu a mmujhi wa Asiya, yawo adali achabwenji a Poolo, adaatuma wandhu kumkambila Poolo kuti wasadalowa pa malo pamenepo. 32Wandhu ambili amabula phokoso, kila mmojhi wamakamba icho wadaganiza kukamba. Wandhu ambili siadajhiwe kuti ali pa malo yajha kwa ndande iti. 33Ayahudi adamchogoza Alekizanda pachogolo. Wandhu wina pa msonghano adakweza mvekelo kumuyelekeza icho wamafunika kukamba. Ndiipo Alekizanda wadakweza jhanja lake kuti akhale chete. 34Nambho yapo adajhiwa kuti Alekizanda wadali Myahudi, wandhu wonjhe adabula phokoso kwa pamojhi ndhawi ya saa mbili, niakamba, “Atemi, nungu wamkazi wa ku Efeso nde wamkulu!”
35Pambuyo pa ndhawi, mchogoleli mmojhi wa mujhi ujha wadaakhalicha chete wandhu. Iye wadakamba, “Anyiimwe wandhu aku Efeso, bwanji, simjhiwa kuti wandhu a mmujhi wa Efeso nde yawo alonda nyumba ya nungu Atene uyo wali wamkulu, ni mwala wake udagwa kuchokela kumwamba? 36Palibe uyo wakhoza kukana vindhu vimenevo. Chimwecho, mukhale chete ni msadachita chindhu chilichonjhe kwa msanga. 37Mwajhanawo wandhu anyiyawo pano, nambho sadainyoze nyumba ya nungu wathu Atemi kapina iye mwene wake. 38Ndiipo ngati Demositilio ni wandhu wake anjhito ali ni chindhu chilichonjhe kwa wandhu anyiawa, mabwalo yamilandu yalipo ni athandizi amalamulo alipo, akhoza kumasula milandu. 39Nambho ngati kuli chindhu china icho mchifuna, pelekani ku bwalo ilo livomelezeka. 40Pakuti pa vindhu ivo vachitika lelo, tili pachiofyezo chakupachidwa mlandu kuti tachita chiwawa. Sikudakhale ni ndande yokhala kwa kubula phokoso ni sitikhoza kujhiteteza ndande yochita mlandhu.” 41Yapo wadamaliza kukamba mawu yameneyo, wadaakambila wandhu wajha adali pa msonghano, achoke.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Vichito 19: NTNYBL2025
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: