Vichito 11

11
Petulo wafotokoza umo watumidwila kwa wandhu osati Ayahudi
1Atumwi ni okhulupilila wina a mu Yudea, adavela kuti wandhu osati Ayahudi nawo chinchijha adalandila mawu la Mnungu. 2Ndiipo Petulo wadapita ku Yelusalemu, wajha Ayahudi adakhulupilila Yesu amafuna wandhu yawo osati Ayahudi achitidwe mdulidwe, adayamba kumtutumila iye niakamba, 3“Iwe udapita mmakhomo mwa wandhu yawo sadachitidwe mdulidwe ni udadya pamojhi nawo!” 4Chimwecho Petulo wadaafotokozela vindhu vonjhe ivo vidachitika nyumba kwa nyumba niwakamba,
5“Siku limojhi yapo nidali mmapembhelo ku mujhi wa Yopa, nidaona masombhenya. Nidaona chindhu chachikulu ngati njhalu ya njhonga zinayi nichichika panjhi kuchokela kumwamba, ni kuima pafupi ni ine. 6Nidapenyechecha mkati mwake, nidaona muli zinyama za miyendo inayi, zinyama za kuthengo, zinyama zokwawa ni mbalame. 7Ndiipo nidavela mvekelo niyanikambila, ‘Petulo uka uphe ni udye!’ 8Nambho ine nidakamba, ‘Notho Ambuye! Sinidadyepo chakudya chalichonjhe icho chakanizidwa kudyedwa kapina icho sichifunika mkamwa mwanga.’ 9Mvekelo udavekanjho kuchokela kumwamba, ‘Vindhu ivo vavomelezedwa ni mnungu kudyedwa iwe sidavitana vindhu sivifunika.’ 10Vindhu ivi vidachitika katatu, nimathelo yake vindhu vonjhe vidatengedwa kupita kumwamba. 11Ndhawi imweijha wandhu atatu yawo adatumidwa kuchokela ku Kaisaliya adafika pa nyumba iyo nimakhala. 12Mzimu woyela udanikambila nichogozane nawo popande kukhaikila. Nawo anyiwajha adamkhulupilila Yesu anjanga sita adachatana nane ku Kaisaliya ni kulowa mnyumba ya Konelio. 13Wadatikambila umo mtumwi wa kumwamba wa Mnungu wadaimila pa nyumba yake ni kumkambila, ‘Atume wandhu ku Yopa akamtane mundhu uyo watanidwa Simoni Petulo. 14Iye siwakukambile mawu yayo siyakuombole iwe pamojhi ni nyumba yako yonjhe.’ 15Yapo nidayamba kukamba, Mzimu Woyela udaachikila ngati umo udachitila kwa ife poyamba. 16Ndiipo nidakumbukila yajha adakamba Ambuye, ‘Yohana wadabatiza kwa majhi, nambho anyiimwe simubatizidwe kwa Mzimu Woyela.’ 17Ijhiwika kuti Mnungu wadaapacha wandhu osati Ayahudi utumiki wofanana ni uwo tidapachidwa ife yapo tidaakhulupilila Ambuye Yesu Kilisito, ine nidali yani kuti nimchuche Mnungu?”
18Yapo adavela chimwechi, adasiya kwaachucha ni kuyamba kumkweza Mnungu, niakamba, “Mnungu waapacha wandhu osati Ayahudi malo yolapa kuti apate umoyo wamuyaya.”
Wandhu adamkhulupila Kilisito ku Antiokia
19Wokhulupilila wina yawo adamwazika ndande ya mavuto yayo yadachitika yapo wadaphedwa Sitifano, adapita kutali mbaka ku Fonesiya, Kipulo ni ku Atioki, nauzila uthenga wa Mnungu kwa Ayahudipe. 20Nambho wokhulupilila anjake yawo adachokela ku Kipulo ni Kilene, adapita ku Antiokia ni kukambilana ni wandhu osati Ayahudi, niwaakambila uthenga wabwino wa nghani za Ambuye Yesu. 21Ambuye wadachogoza kwa mbhavu yake, ni gulu la wandhu ambili lidakhulupilila ni kumng'anamukila Ambuye.
22Nghani za wandhu wajha zidafika mbaka kwa wandhu adamkhulupilila Yesu a ku Yelusalemu, chimwecho adamtuma Banaba wapite ku Antiokia. 23Yapo wadafika kumeneko ni kuona umo Mnungu wadaapachila mwawi wandhu, wadakondwa kupunda ni wadaapembha ayendekele kukhala okhulupilika kwa Ambuye. 24Banaba wadali mundhu wabwino, wachogozedwa ni mbhavu za Mzimu Woyela ni chikhulupililo, ndande ya Banaba wandhu ambili amachuluka kwa Ambuye.
25Ndiipo Banaba wadapita ku mujhi wa Taliso kukamfunafuna Saulo. 26Yapo wadampheza, wadapitanayo ku Antiokia. Wonjhe awili adakhala ni gulu ilo lidamkhulupilila Kilisito kwa chaka cha mbhumbhu, uku niayaluza gulu lalikulu la wandhu. Kumeneko ku Antiokia nde kwa mala yoyamba wandhu adayamba kutanidwa Akilisito.
27Ndhawi imweyo alosi wina adachoka ku Yelusalemu adajha ku mujhi wa Antiokia. 28Basi Mundhu mmojhi uyo watanidwa Agabasi, wadaima ni kulosa kwa mbhavu za Mzimu Woyela kuti njala yaikulu siijhe pa jhiko lonjhe lapanjhi. Njala imeneyo idajha ndhawi ya ulamulilo wa mfumu Tibelio. 29Wajha ochatila kila mmojhi wadachocha mthandizo kwa okhulupilila anjao yawo amakhala ku Yudea ngati umo adakhozela. 30Nikwaatuma Banaba na Sauli apeleke njhembe kwa waakulu agulu la wandhu yawo amkhulupilila Kilisito.

ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖

Vichito 11: NTNYBL2025

គំនូស​ចំណាំ

ចែក​រំលែក

ចម្លង

None

ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល