Zek. 9

9
Chauta aweruza adani a Yuda
Mau olosa
1 # Yes. 17.1-3; Yer. 49.23-27; Amo. 1.3-5 # Yes. 23.1-18; Ezek. 26.1—28.26; Yow. 3.4-8; Amo. 1.9, 10; Mt. 11.21, 22; Lk. 10.13, 14 Mau a Chauta akudzudzula dziko la Hadaraki,
ndiponso mzinda wa Damasiko.
Paja mizinda yonse ya ku Aramu njake ya Chauta,
chimodzimodzi ngati mafuko onse a Aisraele.
2Ndi wa Chautanso mzinda wa Hamati,
umene ukuchitana malire ndi maikowo,
chimodzimodzinso Tiro ndi Sidoni
ngakhale ndi anzeru kwambiri.
3Tiro adadzimangira linga.
Adaunjika siliva ngati dothi,
adakundika golide ngati chifwilimbwiti cham'miseu.
4Koma taimani, Chauta adzamlanda chuma chonsechi,
adzachitaya m'nyanja,
iyeyo adzapserera ndi moto.
5 # Yes. 14.29-31; Yer. 47.1-7; Ezek. 25.15-17; Yow. 3.4-8; Amo. 1.6-8; Zef. 2.4-7 Mzinda wa Asikeloni nawonso udzaziwona zimenezo,
nkuchita mantha.
Gaza adzakhwinyata ndi mantha,
Ekeroninso chimodzimodzi,
chifukwa zimene ankayembekeza zidzasokonezeka.
Mfumu ya ku Gaza idzachotsedwa,
ku Asikeloni kudzakhala kopanda anthu.
6Ku Asidodi kudzakhala anthu achimsakaniza.
Chauta akuti, “Ndidzathetsa kunyada kwa Filistiya.
7Anthu ake sadzadyanso nyama yamagazi,
kapena nyama yoletsedwa iliyonse.
Otsala onse adzakhala anthu anga,
adzasanduka ngati fuko la ku Yuda.
Nawonso Aekeroni adzakhala ngati Ayebusi.#9.7: Ayebusi: Nzika zoyambirira za mu Yerusalemu. Davide atagonjetsa ndi kulanda mzindawo, anthu ameneŵa adakhala mu ulamuliro wa Davide.
8Pamenepo Ine ndidzakhala mlonda wa dziko langalo,
kuti wina asamadutsepo kapena kuloŵamo.
Palibe adani amene adzaŵapambane,
pakuti zimenezi ndikuzisamala Ine ndemwe.”
Mfumu yamtendere
9 # Mt. 21.5; Yoh. 12.15 Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni.
Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu.
Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu.
Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani.
Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu,
bulu wake kamwana tsono.
10 # Mas. 72.8 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuremu
ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu.
Uta wankhondo adzauthyola.
Mfumu yanu idzachititsa mtendere
pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Adzalamulira kuchokera ku nyanja ina
mpaka ku nyanja ina,
ndiponso kuchokera ku Mtsinje wa Yufurate
mpaka ku mathero a dziko lapansi.
11 # Eks. 24.8 Chauta akuti,
“Tsono kunena za inu,
chifukwa cha chipangano changa ndi inu,
chimene nsembe zamagazi zidachitsimikiza,
ndidzaŵatulutsa m'dzenje lopanda madzi
anthu anu amene ali ngati akapolo.
12Bwererani ku linga lanu lolimba,
inu akapolo amene tsopano muli ndi chikhulupiriro.
Lero ndi tsiku limene ndikulengeza
kuti ndidzakubwezerani zabwino moŵirikiza.
13“Ndidzakoka Yuda ngati uta wanga,
Efuremu adzakhala ngati muvi wake.
Ndidzatenga ana ako, iwe Ziyoni,
kuti alimbane ndi ana ako, iwe Grisi;
ndidzakugwira ngati lupanga la wankhondo wamphamvu.”
14Tsono Chauta adzaonekera anthu ake,
ndipo mivi yake adzaiponya ngati zing'aning'ani.
Ambuye Chauta adzaliza lipenga,
ndipo adzayenda m'kamvulumvulu wochokera kumwera.
15Chauta Wamphamvuzonse adzakhala chishango chao.
Iwowo adzapambana ndi kugonjetsa adani ao
poponya miyala chabe.
Adzamwa magazi ao nkumafuula ngati okhuta vinyo.
Magaziwo adzachita kuyenderera ngati magazi a nsembe,
othira ndi mkhate pa guwa popembedza.
16Tsiku limenelo Chauta, Mulungu wao, adzaŵapulumutsa,
pakuti anthu akewo ali ngati nkhosa.
M'dziko laolo anthuwo adzakhala onyezimira
ngati miyala ya mtengo wapatali ya pa chisoti chaufumu.
17Dzikolo lidzakhaladi lokongola kwambiri.
Tirigu adzalimbitsa anyamata,
ndipo vinyo watsopano adzakometsa anamwali.

اکنون انتخاب شده:

Zek. 9: BLY-DC

های‌لایت

کپی

مقایسه

به اشتراک گذاشتن

None

می خواهید نکات برجسته خود را در همه دستگاه های خود ذخیره کنید؟ برای ورودثبت نام کنید یا اگر ثبت نام کرده اید وارد شوید