Mk. 5:25-26
Mk. 5:25-26 BLY-DC
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaazunzika zedi ndi asing'anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M'malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira.




