1
Mk. 9:23
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.”
مقایسه
Mk. 9:23 را جستجو کنید
2
Mk. 9:24
Pomwepo bambo wa mwana uja adanena mokweza mau kuti, “Ndikukhulupirira, koma mpang'ono chabe. Thandizeni kuti ndikhulupirire kwenikweni.”
Mk. 9:24 را جستجو کنید
3
Mk. 9:28-29
Yesu atakaloŵa m'nyumba, ophunzira ake adamufunsa ali paokha, kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?” Yesu adayankha kuti, “Mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera mpamene mungautulutse.”
Mk. 9:28-29 را جستجو کنید
4
Mk. 9:50
Mchere ndi wabwino, koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Moyo wanu ukhale ngati wothiridwa mchere, ndipo muzikhala ndi mtendere pakati panu.”
Mk. 9:50 را جستجو کنید
5
Mk. 9:37
“Aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino osati Ineyo, koma Atate amene adandituma.”
Mk. 9:37 را جستجو کنید
6
Mk. 9:41
Aliyense amene akupatsani chikho cha madzi chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Mk. 9:41 را جستجو کنید
7
Mk. 9:42
“Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamuponya m'nyanja.
Mk. 9:42 را جستجو کنید
8
Mk. 9:47
“Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi bwino kuti ukaloŵe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti akakuponye ku Gehena uli ndi maso onse aŵiri.
Mk. 9:47 را جستجو کنید