Alom 9
9
Mnungu ni wandhu wake Aizilaeli
1Nikamba uzene okhaokha, ine nalunjana ni kilisito. Mtima wanga uku ni uchogozedwa ni Mzimu wa Mnungu ulangiza kuti sinikamba unami. 2Nifuna kukamba chimwechi nili ni chisoni chachikulu ni kupwetekedwa kwa kukulu mumtima mwanga, 3ndande ya achaabale wanga yawo ali a jhiko langa! Ngati chindhu ichi chidakathangatila anyiiwo, nidakavomela kulesedwa ni kupatulidwa ni Kilisito. 4Achameneo nde wandhu a Kuisilaeli yao Mnungu wadasanghula akhale wana wake, wadaachita akhale pamojhi ni ulemelelo, wadachita chipangano ni anyiiwo, wadapacha thauko lake, kulambila kwa zene ni yajha wadakambila kuti siwapache. 5Achamenewo Aizlaeli ni ajhukulu a mambuye, niiye Kilisito kwa kubadwa ngati mundhu, wachoka ku fuko lao. Mnungu walamulile pamwamba pa yonjhe, ni watamandidwe muyaya! Ikhale chimwecho.
6Osati kuti mau la Mnungu lang'anamulidwa, pakuti osati wandhu wonjhe a ku Isilaeli apatulidwa ni Mnungu. 7Osati mibadwa yonjhe ya Ibulahimu ni wana wake a zene. Nambho, ngati umo yalembedwa mmalembo ya Mnungu, “Mibadwa yake siichokane ni Isaka.” 8Mate yake kuti, osati wajha abadwa ngati wandhu umo abadwila nde Wana a Mnungu, nambho ni anyiwajha abadwa kuchokana ni ahadi ya Mnungu nde satanidwe wana a Ibulahimu. 9Pakuti mawu wadakamba Mnungu nde yaya, “Ndhawi ngati ino pachaka sinibwele, niiye Sala siwapate mwana wa mmuna.”
10Osati yameneyope, chinchijha Labeka naye siwapate wana amawila kwa tate mmojhi, yani Isaka tate wathu. 11Nambho dala Mnungu aoneke kuti ali ni ufulu osangha, wana amawila amenewo akali sadabadwe, ni akali saadajhiwe kuchita chindhu cha bwino kapina choipa, 12Labeka wadakambidwa kuti yujha mwana wa woyamba siwamtumikile yujha wambuyo. Chimwecho kusanghula kwa Mnungu uchokana ni umo wafunila mwene, niosati machitidwe ya wandhu. 13Ngati umo malembo ya Mnungu yalembedwa, “Yakobo nidamkonda, nambho Esau nidamuipila,”
14Chipano tikambe chiyani? Bwanji Mnungu siwachita umo ifunikila? Notho! 15Pakuti Mnungu wadamkambila Musa, “Sinimlengele lisungu mundhu waliyonjhe uyo sinifune kumlengela lisungu, sinimlengele lisungu mundhu waliyonjhe uyo nimfuna.” 16Chimwecho yonjhe yakhulupila lisungu la Mnungu, nambho siya khulupilila bidii kapina kufuna kwa mundhu. 17Pakuti malembo ya Mnungu yakamba chimwechi kwa nghani ya Falao, “Nidakuchita kukhala mfumu kuti kupitila iwe, nilangize mbhavu zanga, ni jhina langa lijhiwike.” 18Chimwecho Mnungu wamlengela lisungu mundhu wafuna kumlengela lisungu, niwakafuna kumchita mundhu wakhale wambuli wachita chimwecho.
Mbhwayi ya Mnungu ni lisungu la Mnungu
19Kapina siunifunjhe, “Ngati vindhu vili chimwecho, Mnungu wakhoza kumlaumu mundhu? Yani wakhoza kuchuchana ni umo wafunila iye?” 20Nambho iwe mundhu iwe ni yani ata uyesa kumfunjha Mnungu? Bwanji mphika ukhoza kumfunjha uyo wauumba, “Ndande yanji waniumba chimwechi?” 21Uyo waumba mphika wakhoza kulipotela njhito dothi umo wafunila ni kuumba miphika iwili kwa dothi limwelijha, umojhi kwa kutumila kwa ulemu, ni china ku kutimia kwa kawaida.
22Chimwecho nde umo ili kwa Mnungu. Wamafuna kutilangiza mbhwayi yake ni kutijhiwicha mbhavu zake. Wamaembekeza ni kwaalimbila mtima kupunda anyiwajha wamafunika kuphezana ni mbhwayi yake? 23Mnungu waadafuna kulangiza kuchuluka kwa ulemelelo wake uwo wadatipungulila kwa kutilengela lisungu, ife wadatikonjekela kwa kulandila ulemelelo wake. 24Pakuti ife nde achameneo adaatana, osati kuchoka kwa Ayahudipe nambho kuchoka kwa wandhu amaiko yonjhe. 25Pakuti nde umo wakambila mchikalakala cha mlosi Osea,
“Wandhu anyiwajha adali osati wanga
sinaatane ‘Wandhu wanga!’
Ni jhiko ilo sinidalikonde,
sinilitane ‘Wokondwedwa wanga!’
26Nipajha adakambidwa ni Mnungu, ‘Anyiimwe osati wanga’
pamenepo satanidwe wana wa Mnungu uyo wali wamoyo.”
27Niiye mlosi Isaya, kwa nghani ya Izilaeli wadakweza mvekelo niwakamba, “Ata ngati mbadwa a Izilaeli ni ambili ngati mchenga wa mumtunda wa nyanja, ni ochepape yao salamichidwe, 28Pakuti Mnugu siwalamule chisanga jhiko lonje.” 29Ngati mlosi wa Mnungu Isaya wadakamba poyambila, “Mbuye wa mbhavu zonjhe siwadakatisiilila wana akumojhi a Isilaeli, tidakatokala ngati Sodoma ni tidakatokhala ngati Gomola.”
Kosakhulupilile kwa Izililaeli
30Chipano tikambe chiyani? Wandhu anyiawo osati a Izilaeli siadafunefune kukhala ovomelezedwa ni Mnungu, apachidwa kuvomelezeka kwa njila ya chikhulupi. 31Nambho a Izilaeli yao adafunafuna thauko la kwachita kukhala ovomelezeka ni Amnungu, siadalipate. 32Ndande ya kukhulupila vichito vao pambuyo pa kukhulupilila chikhulupi. Chimwecho, adajhikwala pamwamba pa mwala ujha “Ukwiicha.” 33Ngati umo yalembedwela mmalembo ya Mnungu yalembela,
“Penya siiniike kumeneko kusayuni mwala wa kujhikwala,
mwala uwo siwachite wandhu agwe.
Nambho uyo siwamkhulupilile siwapata njhoni!”
Currently Selected:
Alom 9: NTNYBL2025
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.