Alom 8
8
Kukhala kwa mbhavu za Mzimu wa Mnungu
1Chipano palibe lamulo la chilango kwa anyiwajha yao muukhalo wao alunjana ni Kilisito. 2Pakuti thauko la Mzimu ilo lipeleka umoyo kwa kulanjana ni kilisito Yesu, yanilekelela kuchokela mthauko la machimo ilo lipeleka nyifa. 3Mnungu wadachita chindhu chijha thauko silidakhoze kuchita, ndande ya kuchepekela kwa Mundhu. Mnungu wadamtuma Mwana wake uku wali ni thupi ngati umo tili ife, dala wayachoche machimo kwa thupi lake, ni kwa thupi limwelo wayachoche machimo. 4Mnungu wadachita chimwecho kuti tikhoze kuchita yajha yafunika ni thauko, kwa kumkhulupilila mzimu wa Mnungu pambuyo pa kuyavela makhumbilo ya matupi yathu. 5Pakuti anyiwajha akhala kwa kulichata thupi, achogozedwa ni maganizo ya thupi, nambho anyiwajha akala ngati ufunila mzimu wa Mnungu, achogozedwa ni maganizo ya mzimu. 6Maganizo yayo yachogozedwa ni thupi yapeleka nyifa, nambho maganizo yayo yachogozedwa ni Mzimu yapeleka umoyo ni mtendele. 7Mundhu uyo wachogozedwa ni maganizo ya thupi ni mdani wa Mnungu, siwachata thauko la Mnungu ni siwakhoza kulivela. 8Wandhu yao achata umo lifunila thupi, sakhoza kumkwadilicha Mnungu.
9Nambho anyiimwe simchogozedwa ni thupi, ila mchogozedwa ni Mzimu, ikhalape ngati Mzimu wa Mnungu ukhala mkati mwanu. Chimwecho waliyonjhe uyo walibe Mzimu wa kilisito mmeneyo osati wake Kilisito. 10Nambho ngati Kilisito wali mkati mwanu, matupi yanu siyamwalile ndande ya machimo, nambho Mizimu yanu yamoyo ndande mwachitidwa kukhala Amnungu. 11Ngati Mzimu wa Mnungu udamuhyukicha Kilisito ukhala mkati mwanu, chimwecho wadamuhyukicha kilisito siwayapache umoyo mathupi yanu yayo yamwalila, siwachite chimwecho kwa kupitila Mzimu wake uyo wakhala mkati mwanu.
12Chimwecho achaabale wanga, tili ni njhito nambho sitifunika kukhala ngati umo lifunila thupi. 13Pakuti mkakhala ngati umo lifunila thupi, zenedi simmwalile. Nambho ngati mkakhala mkati Mzimu muyaipha machitidwe yanu ya chithupi kwa chizimu simkhale moyo. 14Wonjhe achogozedwa ni Mzimu wa Mnungu ni wana wa Amnungu. 15Pakuti simdalandile Mzimu wakukuchitani anyiimwe akapolo ni kukupachani mandha, nambho mwalandila Mzimu wakukuchitani anyiimwe wana a Mnungu, ni mwa Mzimu umeneo ife timtana Mnungu, “Aba” Mate yake, “Tate!” 16Nawo Mzimu wene ulangiza mkati mwa mitima yathu, kuti ife ni wana a Mnungu. 17Chipano ndande ife ni wana wa a Mnungu, sitilandile mwawi wonjhe uwo Mnungu wadaikila wandhu wake, ni sitilandile vindhu vimenevo pamojhi ni Kilisito, zenedi tikavutika pamojhi niiye, sitipate ulemelelo pamojhi ni iye
Ulemelelo uwo ukujha
18Niyaona mavuto ya ndhawi ino osati chindhu, ngati tikalinganicha ni ulemelelo uwo siulangizidwe kwatu mchogolo. 19Pakuti voumbidwa vonjhe vilindilila kwa khumbilo, Mnungu yapo siwaajhiwiche wana wake. 20Pakuti voumbidwa vonjhe vidaikidwa mosajhikozela, osati kwa kufuna kwao, nambho vidachitidwa chimwecho ngati umo wadafunila Mnungu. Ata chimwecho chilipo chikulupililo, 21pakuti voumbidwa vimenevo navo siviomboledwe kuchokela muukapolo wa kuwangika, ni kupachidwa ufulu wa ulemelelo wa wana a Mnungu. 22Pakuti tijhiwa mbaka chipano, voumbidwa vonjhe vilila kwa kupweteka ngati kujhimasula kwa wamkazi. 23Osati voumbidwa vimenevo voka, nambho ata ife tili ni mzimu umeneo, uwo uli woyamba wa mbhaso ya Mnungu, ife nafe tidandaula mkati mwathu, uku ni tilindilila tichitidwe kukhala wana a Mnungu, ni mitima yathu iomboledwe. 24Pakuti kwa kukhulupila kumeko ife taomboledwa. Nambho kukhulupilila kulibe mate ngati tichiona chijha tichikhulupilila. Pakuti yani wakhulupilila chijha wachiona? 25Ngati tichikhulupila icho tilibe, chimwecho sitichilindile kwa kuchilimbila mtima.
26Ife tilibe mbhavu nambho Mzimu wa Amnungu utithangatila. Pakuti sitijhiwa umo ifunika kupembela, nambho Mzimu wene utipembhela kwa Mnungu kwa kubuula ukosikukambika. 27Niiye Mnungu uyo wapenya mbaka mkati mwa mitima ya wandhu, wayajhiwa maganizo ya Mzimu umenewo, pakuti Mzimu umenewo wapembhela wandhu kwa Mnungu kuchatana ni umo wafunila Mnungu.
28Tijhiwa kuti pavindhu vonjhe, Mnungu wachita njhito pamojhi ni wonjhe wakonda pa kwapacha vabwino, yani wajha waadatana kuchokana ni dala lake. 29Wandhu wajha Mnungu wadaasangha kuyambila mmayambo, nde yawo wadaapatula alingane ni Mwana wake, kuti wakhale woyamba pakati pa achabale ambili. 30Chipano anyiwajha Mnungu wadaasangha nde anyiawo wadaatana, ni wadachita akhale ovomelezeka, ni nde anyiyawo wadaapacha ulemelelo.
Chikondi cha Mnungu kupitila Kilisito Yesu
31Kuchokana ni yameneyo, sitikambe chiyani? Ngati Mnungu wali pamojhi ni ife, yani wakoza kutichucha? 32Mnungu siwadamchekeleze ata Mwana wake wa yokha, ila wadamchocha ndande ya ife wonjhe, ngati wadachita chimwecho, bwanji, siwatipacha mwawi wonjhe? 33Niyani siwapache mlandu wandhu asanghidwa ni Mnungu? Mnungu mwene wachochela kulakwa kwao! 34Niyani uyo siwalamule kwa kwalanga? Palibe! Pakuti Kilisito nde uyo wadamwalila, ni wadahyuka ni wakhala kumalo ya ulamulilo kwa Mnungu iye watipembhela. 35Niyani wakhoza kutiika patali nichikondi cha Kilisito? Bwanji ni kulaga, kapina mavuto, kapina njala, kapina kutedwa njhalu, kapina kuofyedwa kuphedwa? 36Ngati umo malembo ya Mnungu yakambila,
“Ndande yako, tifunidwa ni nyifa usana ni usiku,
tawelengedwa ngati mbelele zopedwa.”
37Nambho pa vindhu vimenevo vonjhe, tikhoza ndande tithangatilidwa ni Klisito uyo watikonda. 38Pakuti nijhiwa uzene kuti palibe chindhu chikhoza kutipatula ni chikondi cha Mnungu ikhakhala nyifa kapina umoyo, kapina atumiki a akumwamba kapina mbhavu zina za kumwamba, kapina yayo yachokela saino, kapina yayo siyachokele pambuyo, kapina ulamulilo, 39kapina jhiko la kumwamba kapina jhiko la panjhi kupunda. Palibe choumbidwa chalichonjhe chikhoza kutiika patali ni chikondi cha Mnungu mkati mwa Kilisito Yesu mbuye wathu.
Currently Selected:
Alom 8: NTNYBL2025
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.