YouVersion Logo
Search Icon

Mt. 16

16
Afarisi ndi Asaduki apempha chizindikiro chozizwitsa
(Mt. 12.38-39; Mk. 8.11-13; Lk. 11.16; 12.54-56)
1 # Mt. 12.38; Lk. 11.16 Tsiku lina kudabwera Afarisi ndi Asaduki ena kwa Yesu. Adampempha kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba.#16.1 Chizindikiro…chochokera kumwamba: Ndiye kuti chotsimikizira kuti Mulungu ndiye adamtuma. Pakutero ankangofuna kumutchera msampha. 2Koma Yesu adaŵauza kuti, “Pamene dzuŵa likuloŵa, mumati, ‘Maŵa kucha bwino, popeza kuti kumwamba kuli psuu.’ 3Ndipo m'maŵa mumati, ‘Lero ndiye kugwa mvula yamkuntho, popeza kuti kumwambaku kwachita mitambo yabii.’ Mumatha kutanthauzira m'mene kukuwonekera kumwambaku, koma osatha kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi zino. 4#Mt. 12.39; Lk. 11.29Anthu a mbadwo woipa ndi wosakhulupirika amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzaona chizindikiro china kupatula chokha chija cha mneneri Yona.”#16.4 Chizindikiro…cha mneneri Yona: Onani pa Mt. 12.39-40. Atatero, Yesu adaŵasiya nachokapo.
Za zophunzitsa zonama za Afarisi ndi Asaduki
(Mk. 8.14-21; Lk. 12.1)
5Pamene ophunzira aja adakafika kutsidya, anali ataiŵala kutenga buledi. 6#Lk. 12.1Yesu adaŵauza kuti, “Muchenjere nacho chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi Asaduki.” 7Apo ophunzirawo adayamba kukambirana nkumati, “Akuterotu chifukwa sitidatenge buledi.” 8Yesu adaadziŵa zimene iwo ankanena. Ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukukambirana zakuti mulibe buledi, inu a chikhulupiriro chochepanu? 9#Mt. 14.17-21 Kodi mpaka pano simunamvetsebe? Kodi simukukumbukira kuti ndi buledi msanu ndidadyetsa anthu zikwi zisanu? Nanga mudaadzaza madengu angati ndi zotsala? 10#Mt. 15.34-38 Sujanso ndi buledi msanu ndi muŵiri ndidadyetsa anthu zikwi zinai? Nanga mudaadzaza madengu angati a zotsala? 11Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindimanena za buledi? Chenjera nachoni chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi Asaduki.” 12Pamenepo iwo adazindikira kuti Yesu sankaŵauza kuti achenjere ndi chofufumitsira buledi, koma kuti achenjere ndi zophunzitsa za Afarisi ndi Asaduki.
Zimene Petro adanena za Yesu
(Mk. 8.27-30; Lk. 9.18-21)
13Pamene Yesu adafika ku madera a ku Kesareya-Filipi, adafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthune ndine yani?” 14#Mt. 14.1, 2; Mk. 6.14, 15; Lk. 9.7, 8Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu Yeremiya kapena mmodzi mwa aneneri.” 15Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” 16#Yoh. 6.68, 69Simoni Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu wamoyo.” 17Yesu adamuuza kuti, “Ndiwe wodala, Simoni mwana wa Yona, pakuti si munthu wakuululira zimenezi ai, koma ndi Atate anga amene ali Kumwamba. 18Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro,#16.18 Petro: Limeneli ndi dzina lachigriki. Pa Chiyuda amati Kefa. Tanthauzo lake ndiye kuti, Thanthwe kapena mwala. ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa. 19#Mt. 18.18; Yoh. 20.23Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.” 20Yesu atanena zimenezi, adalamula ophunzira aja kuti asauze munthu aliyense kuti Iye ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Yesu aneneratu za kufa ndi kuuka kwake
(Mk. 8.31-33; Lk. 9.22)
21Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kudziŵitsa ophunzira ake kuti, “Ndiyenera kupita ku Yerusalemu, kumeneko akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzandizunza kwambiri. Ndidzaphedwa koma mkucha wake ndidzauka.” 22Apo Petro adamtengera pambali nayamba kumdzudzula. Adati, “Pepani Ambuye, zisatero ai. Mulungu asalole zimenezi.” 23Koma Yesu adacheuka namdzudzula. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Ufuna kundilakwitsa. Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”
Za kusenza mtanda ndi kutsata Yesu
(Mk. 8.34—9.1; Lk. 9.23-27; Yoh. 12.25)
24 # Mt. 10.38; Lk. 14.27 Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata. 25#Mt. 10.39; Lk. 17.33; Yoh. 12.25Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. 26Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake? 27#Mt. 25.31; Mas. 62.12; Aro. 2.6Ndipotu Mwana wa Munthu adzabwera ndi angelo ake ali ndi ulemerero wa Atate ake. Pamenepo adzabwezera aliyense molingana ndi zochita zake. 28Ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Mwana wa Munthu akubwera ndi ulemerero waufumu.”

Currently Selected:

Mt. 16: BLY-DC

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in