YouVersion Logo
Search Icon

Mt. 17

17
Za kusinthika kwa maonekedwe a Yesu
(Mk. 9.2-13; Lk. 9.28-36)
1Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, Yakobe ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. 2Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona. Nkhope yake idaŵala ngati dzuŵa, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. 3Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adaona Mose ndi Eliya akulankhula naye. 4Petro adauza Yesu kuti, “Ambuye, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Ngati mukufuna, ndimanga misasa itatu pano, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” 5#Gen. 22.2; Mas. 2.7; Yes. 42.1; Mt. 3.17; 12.18; Mk. 1.11; Lk. 3.22; Deut. 18.15#2Pet. 1.17, 18Akulankhula choncho, kudadza mtambo woŵala nuŵaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” 6Ophunzira aja atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri nadzigwetsa chafufumimba. 7Koma Yesu adabwera, naŵakhudza nkunena kuti, “Dzukani, musachite mantha.” 8Iwo aja poŵeramuka, adangoona kuti palibe munthu winanso, koma Yesu yekha.
9Pamene ankatsika phiri lija, Yesu adaŵalamula kuti, “Zimene mwaona m'masomphenyazi musakauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.” 10#Mal. 4.5Ophunzira aja adamufunsa kuti, “Nanga bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Eliya adzayenera kuyamba wabwera?” 11#Mphu. 48.10Yesu adati, “Inde Eliya ayambadi wabwera nkudzakonzanso zonse. 12#Mt. 11.14Koma ndikunenetsa kuti Eliya adabwera kale, ndipo anthu sadamzindikire, koma adamchita zonse zimene iwo ankafuna. Chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi anthuwo.” 13Pamenepo ophunzira aja adazindikira kuti ankaŵauza za Yohane Mbatizi.
Yesu achiritsa mnyamata wogwidwa ndi mizimu yoipa
(Mk. 9.14-29; Lk. 9.37-43)
14Pamene iwo adafikanso kumene kunali khamu la anthu kuja, munthu wina adadzagwadira Yesu. 15Adati, “Ambuye mchitireni chifundo mwana wanga. Ali ndi khunyu ndipo amavutika koopsa. Kaŵirikaŵiri amagwa pa moto mwinanso m'madzi. 16Ndinabwera naye kwa ophunzira anuŵa, koma alephera kumchiritsa.” 17Yesu adati, “Ha! Anthu a m'badwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo! Ndiyenera kukhala nanube mpaka liti? Ndiyenera kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwanayo.” 18Atatero, Yesu adazazira mzimu woipawo, ndipo udatuluka mwa mnyamatayo. Pompo iye adachira.
19Pambuyo pake ophunzira aja adadza kwa Yesu paseri namufunsa kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?” 20#Mt. 21.21; Mk. 11.23; 1Ako. 13.2Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.”
[ 21“Koma mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera ndi kusala zakudya mpamene mungautulutse.”]
Yesu aneneratunso za kufa ndi kuuka kwake
(Mk. 9.30-32; Lk. 9.43-45)
22Tsiku lina ophunzira atasonkhana onse ku Galileya, Yesu adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu. 23Iwo adzamupha, koma mkucha wake Iye adzauka.” Ophunzirawo atamva zimenezi, adagwidwa ndi chisoni chachikulu.
Yesu akhoma msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu
24 # Eks. 30.13; 38.26 Pamene Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Kapernao, okhometsa msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu#17.24 Msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu: Myuda aliyense wa zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo ankayenera kukhoma chaka ndi chaka msonkho umenewu. (Onani Eks. 30.11-16). adadzafunsa Petro kuti, “Kodi aphunzitsi anuŵa sakhoma msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu?” 25Iye adati, “Amakhoma.” Tsono Petro ataloŵa m'nyumba, asananene chilichonse, Yesu adamufunsa kuti, “Iwe Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu apansipano amalandira msonkho kwa yani? Kwa anthu a mtundu wao, kapena kwa alendo?” 26Petro adati, “Kwa alendo.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Tsono ndiye kutitu anthu a mtundu wao sayenera kukhoma. 27Koma kuwopa kuŵakhumudwitsa a ku Nyumba ya Mulunguŵa, kaŵedze nsomba ku nyanja. Nsomba imene ukayambire kuŵedza, ukaikanule kukamwa, ndipo ukapezamo ndalama. Ukatenge ndalamayo nkukakhomera msonkho wanga ndi wako womwe.”

Currently Selected:

Mt. 17: BLY-DC

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in