Mt. 15
15
Za miyambo ya makolo a Ayuda
(Mk. 7.1-13; Lk. 11.37-41)
1Tsiku lina Afarisi ena ndi aphunzitsi ena a Malamulo adadza kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu. Adamufunsa kuti, 2“Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo?#15.2 Mwambo wa makolo: Onani Matanthauzo: Miyambo ya makolo. Sasamba m'manja moyenera akamadya chakudya.” 3Yesu adaŵayankha kuti, “Nanga bwanji inuyo, chifukwa choumirira miyambo yanu, mumaphwanya lamulo la Mulungu? 4#Eks. 20.12; Deut. 5.16; Eks. 21.17; Lev. 20.9 Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’ 5Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni, ndazipereka kwa Mulungu,” ameneyo sasoŵanso kulemekeza atate ake.’ 6Pakutero, chifukwa cha mwambo wanuwo, mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe. 7Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaati,
8 #
Yes. 29.13
“ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe,
koma mtima wao uli kutali ndi Ine.
9Amandipembedza inde,
koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu,
chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni
ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
Za zimene zimaipitsa munthu
(Mk. 7.14-23; Lk. 6.39)
10Pambuyo pake Yesu adaitana anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani ndipo mumvetse bwino. 11Si chinthu choloŵa m'kamwa mwa munthu chimene chimamuipitsa ai, koma chotuluka m'kamwa mwake ndiye chimene chimamuipitsa.”
12Pamenepo ophunzira ake adadzamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Afarisi aja akhumudwa atamva zija mwanenazi?”
13Yesu adati, “Chomera chilichonse chimene sichidabzalidwe ndi Atate anga akumwamba, chidzazulidwa. 14#Lk. 6.39Alekeni, ndi atsogoleri akhungu ameneŵa. Tsono ngati wakhungu atsogolera wakhungu mnzake, onse aŵiri adzagwa m'dzenje.” 15Apo Petro adampempha kuti, “Timasulirenitu fanizoli.” 16Yesu adati, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? 17Kodi inu simuzindikira kuti zonse zoloŵa m'kamwa mwa munthu zimaloŵa m'mimba mwake, pambuyo pake nkukatayidwa kuthengo? 18#Mt. 12.34Koma zotuluka m'kamwa mwa munthu zimachokera mu mtima, ndipo zimenezi ndizo zimamuipitsa. 19Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe. 20Zimenezi ndizo zimaipitsa munthu. Koma kudya chakudya osasamba m'manja, sikungaipitse munthu.”
Za chikhulupiriro cha mai wina
(Mk. 7.24-30)
21Yesu adachoka kumeneko, napita ku madera a ku Tiro ndi Sidoni. 22Mai wina wachikanani,#15.22 Wachikanani: Maiyo adaachokera ku Siro-Fenisiya, dera la Kanani lakumpoto. (Onani Mk. 7.24,26). wa ku madera amenewo, adadza kwa Yesu. Adafuula kuti, “Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi ngwogwidwa koopsa ndi mzimu woipa.” 23Koma Yesu sadamuyankhe mau ndi amodzi omwe. Ophunzira ake adadza nampempha kuti, “Muuzeni azipita, onani akubwera natisokosera.” 24Yesu adati, “Inetu Mulungu adandituma kwa amene ali ngati nkhosa zotayika pa mtundu wa Aisraele.” 25Mai uja adadzamgwadira nati, “Ambuye, ndithu thandizeni.” 26Yesu adamuuza kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.” 27Maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amadyako nyenyeswa zimene zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la mbuye ao?” 28Apo Yesu adati, “Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu. Zichitikedi zimene mukufuna.” Pompo mwana wake wamkazi uja adachira.
Yesu achiritsa anthu ambiri
29Pambuyo pake Yesu adachoka kumeneko, nayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya. Kenaka adakwera m'phiri nakakhala pansi kumeneko. 30Anthu ambirimbiri adadza kwa Iye ndi anthu opunduka miyendo, akhungu, olumala, osalankhula, ndiponso ndi odwala ena ambiri. Adaŵakhazika pafupi ndi Yesu, Iye nkuŵachiritsa. 31Tsono anthu onse adadabwa poona kuti osalankhula aja akulankhula, olumala aja achira, opunduka miyendo aja akuyenda, ndipo akhungu aja akupenya. Choncho adatamanda Mulungu wa Israele.
Yesu adyetsa anthu oposa zikwi zinai
(Mk. 8.1-10)
32Yesu adaitana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndikuŵamvera chifundo anthuŵa, chifukwa akhala nane masiku atatu tsopano, ndipo alibe chakudya. Sindifuna kuŵabweza kwao ali ndi njala chonchi, kuwopa kuti angalefuke pa njira.” 33Ophunzirawo adamufunsa kuti, “Anthu ochuluka chotereŵa tingaŵapezere kuti chakudya chokwanira, kuthengo ngati kuno?” 34Yesu adaŵafunsa kuti, “Kaya buledi muli naye mngati?” Iwo aja adati, “Msanu ndi muŵiri, ndiponso tinsomba toŵerengeka.” 35Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. 36Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, ndi nsomba zija, adathokoza Mulungu, nazinyemanyema nkuzipereka kwa ophunzira ake, iwowo nakazigaŵira anthu aja. 37Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nkudzaza madengu asanu ndi aŵiri. 38Koma tsono anthu amene adaadyawo, analipo zikwi zinai amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana.
39Pambuyo pake Yesu adatsazikana nawo anthu aja, kenaka Iye adaloŵa m'chombo napita ku dera la Magadani.
Currently Selected:
Mt. 15: BLY-DC
Highlight
Copy
Compare
Share
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi