1
Mt. 15:18-19
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Koma zotuluka m'kamwa mwa munthu zimachokera mu mtima, ndipo zimenezi ndizo zimamuipitsa. Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.
Compare
Explore Mt. 15:18-19
2
Mt. 15:11
Si chinthu choloŵa m'kamwa mwa munthu chimene chimamuipitsa ai, koma chotuluka m'kamwa mwake ndiye chimene chimamuipitsa.”
Explore Mt. 15:11
3
Mt. 15:8-9
“ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutali ndi Ine. Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
Explore Mt. 15:8-9
4
Mt. 15:28
Apo Yesu adati, “Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu. Zichitikedi zimene mukufuna.” Pompo mwana wake wamkazi uja adachira.
Explore Mt. 15:28
5
Mt. 15:25-27
Mai uja adadzamgwadira nati, “Ambuye, ndithu thandizeni.” Yesu adamuuza kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.” Maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amadyako nyenyeswa zimene zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la mbuye ao?”
Explore Mt. 15:25-27