Mt. 10
10
Za atumwi khumi ndi aŵiri aja
(Mk. 3.13-19; Lk. 6.12-16)
1Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu,#10.1 Mizimu yoipitsa anthu: Inali mizimu imene inkati ikaloŵa mwa munthu, inkamusandutsa wosayenera kuchita nao zachipembedzo (woipitsidwa). kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. 2Atumwi khumi ndi aŵiriwo maina ao ndi aŵa: Woyamba ndi Simoni, wotchedwa Petro, ndipo mbale wake Andrea; Yakobe, mwana wa Zebedeo, ndi mbale wake Yohane; 3Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; 4Simoni, wa m'chipani chandale cha Azelote; ndiponso Yudasi Iskariote, amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.
Yesu atuma khumi ndi aŵiri aja
(Mk. 6.7-13; Lk. 9.1-6)
5Anthu khumi ndi aŵiri ameneŵa Yesu adaŵatuma ndi malamulo akuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kukaloŵa m'mudzi uliwonse wa Asamariya ai. 6Koma makamaka mupite kwa Aisraele amene ali ngati nkhosa zotayika. 7Pitani, muzikalalika kuti, ‘Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.’ 8Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere. 9Musatenge ndalama m'zikwama, kaya nzagolide, kaya nzasiliva, kaya nzakopala. 10#1Ako. 9.14; 1Tim. 5.18Musatenge thumba lapaulendo, kapena mikanjo iŵiri, kapena nsapato, kapena ndodo. Paja wantchito ngwoyenera kulandira zosoŵa zake.
11“Pamene mwaloŵa mu mzinda kapena m'mudzi uliwonse, mufunsitse za munthu wofunadi kukulandirani. Mukakhale kunyumba kwake mpaka nthaŵi yochoka. 12Poloŵa m'nyumba, muzikanena kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu’. 13Tsono ngati anthu am'nyumbamo akulandiranidi, mtendere wanuwo ukhale nawo ndithu. Koma ngati anthu am'nyumbamo akana kukulandirani, mtendere wanuwo ubwerere kwa inu. 14#Ntc. 13.51Munthu aliyense akakana kukulandirani kapena kumvera mau anu, musanse fumbi la kumapazi kwanu potuluka m'nyumbamo kapena m'mudzimo. 15#Mt. 11.24; Gen. 19.24-28#Lk. 10.4-12 Ndithu ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga mudzi wa Sodomu ndi wa Gomora, koma osati polanga mudzi umenewo.
Zakuti atumwi adzazunzidwa
(Mk. 13.9-13; Lk. 21.12-17)
16 #
Lk. 10.3
“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda. 17#Mk. 13.9-11; Lk. 12.11, 12; 21.12-15Anthu muchenjere nawo, pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. 18Adzapita nanu kwa nduna ndi mafumu chifukwa cha Ine, mwakuti mudzandichitira umboni pamaso pao, ndi pa anthu a mitundu ina. 19Akadzakutengerani ku milandu, musadzade nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Kodi tikakambe bwanji?’ Kapena kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Mudzapatsidwa pa nthaŵi imeneyo mau oti munene. 20Pajatu odzalankhula si ndinu ai, koma Mzimu wa Atate anu#10.20 Mzimu wa Atate anu: Ndiye kuti Mzimu Woyera. ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu.
21 #
Mk. 13.12; Lk. 21.16 “Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa. 22#Mt. 24.9; Mk. 13.13; Lk. 21.17; Mt. 24.13; Mk. 13.13Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke. 23Tsono akamadzakuzunzani ku mudzi wakutiwakuti, mukathaŵire ku mudzi wina. Ndithu ndikunenetsa kuti musanathe kuyendera midzi yonse ya Aisraele, Mwana wa Munthu adzakhala atabwera. 24#Lk. 6.40; Yoh. 13.16; 15.20Paja wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo wantchito saposa mbuye wake ai. 25#Mt. 9.34; 12.24; Mk. 3.22; Lk. 11.15Kumkwanira wophunzira kuti alingane ndi mphunzitsi wake, ndiponso wantchito kuti alingane ndi mbuye wake. Tsono ngati mwini banja anthu adamutcha Belezebulu,#10.25 Belezebulu: Ndi dzina lina la Satana, ndiye kuti Mkulu wa mizimu yoipa. nanji a m'banja mwake, kodi sadzaŵatcha maina oipa koposa apa?
Woyenera kumuwopa
(Lk. 12.2-7)
26 #
Mk. 4.22; Lk. 8.17 “Choncho inu musamaopa anthu. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika. 27Zimene ndikukuuzirani m'chibisibisi, inu mukazilankhulire poyera, ndipo zimene mukuzimvera m'manong'onong'o, inu mukazilalikire pa madenga. 28Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena. 29Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. 30Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. 31Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Za kuvomereza Khristu pamaso pa anthu
(Lk. 12.8-9)
32“Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba. 33#2Tim. 2.12Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa.
Za kugaŵikana kwa anthu chifukwa cha Yesu
(Lk. 12.51-53; 14.26-27)
34“Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo. 35#Mik. 7.6Inetu paja ndidadzalekanitsa mwana wamwamuna ndi bambo wake, mwana wamkazi ndi mai wake, mkazi ndi apongozi ake aakazi, 36mwakuti adani a munthu adzakhala a m'banja mwake omwe.
37“Munthu wokonda bambo wake kapena mai wake koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Ndipo wokonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. 38#Mt. 16.24; Mk. 8.34; Lk. 9.23Amene sasenza mtanda wake ndi kumanditsata, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. 39#Mt. 16.25; Mk. 8.35; Lk. 9.24; 17.33; Yoh. 12.25Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga.
Wodzalandira mphotho
(Mk. 9.41)
40 #
Lk. 10.16; Yoh. 13.20;
Mk. 9.37; Lk. 9.48 “Munthu wokulandirani inu, amandilandira Ine ndemwe. Ndipo wondilandira Ine, amalandiranso Iye uja amene adandituma. 41Munthu wolandira nthumwi ya Mulungu chifukwa choti ndi nthumwi, adzalandira mphotho ya nthumwi ya Mulungu. Wolandira munthu wolungama chifukwa choti ngwolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama. 42Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Currently Selected:
Mt. 10: BLY-DC
Highlight
Copy
Compare
Share
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi