YouVersion Logo
Search Icon

Mt. 11

11
Yohane Mbatizi atuma amithenga kwa Yesu
(Lk. 7.18-35)
1Yesu atatsiriza kulangiza ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, adachoka kumeneko nkumakaphunzitsa ndi kulalika m'mizinda yao.
2Pamene Yohane Mbatizi anali m'ndende, adaamva zimene Khristu uja ankachita. Choncho adatuma ophunzira ake ena kwa Iye kukamufunsa kuti, 3“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” 4Yesu adati, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mukuzimva ndi kuziwona. 5#Yes. 35.5, 6; Yes. 61.1Akhungu akupenya ndipo opunduka miyendo akuyenda; akhate akuchira ndipo agonthi akumva; akufa akuukitsidwa ndipo amphaŵi akumva Uthenga Wabwino. 6Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”
7Pamene amithenga a Yohane aja ankachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “Kodi m'mene mudaapita ku chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? 8Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofeŵa kodi? Iyai, anthu ovala zofeŵa amakhala m'nyumba za mafumu. 9Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri amene. 10#Mal. 3.1Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti,
“ ‘Nayitu nthumwi yanga,
ndikuituma m'tsogolo mwako,
kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’
11Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane Mbatizi. Komabe ngakhale amene ali wamng'onong'ono mu Ufumu wakumwamba amampambana. 12#Lk. 16.16Kuyambira pa nthaŵi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akhala akulimbana ndi Ufumu wa Kumwamba, ndipo ochita chamuna ndiwo amene akuulanda. 13Aneneri onse ndiponso Malamulo a Mose ankaneneratu za Ufumu umenewu mpaka nthaŵi ya Yohane Mbatizi. 14#Mal. 4.5; Mt. 17.10-13; Mk. 9.11-13Ndipo ngati mukufunadi kukhulupirira zimenezi, Yohaneyo ndiye Eliya uja ankati adzabwerayu. 15Amene ali ndi makutu, amve!
16“Kaya anthu amakonoŵa ndingaŵafanizire ndi chiyani? Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti,
17“ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati,
bwanji inu osavina?
Tidaabuma maliro,
bwanji inu osalira?’
18Paja Yohane Mbatizi atabwera, ankasala zakudya ndi zakumwa, anthu nkumati, ‘Adagwidwa ndi mzimu woipa.’ 19Mwana wa Munthu adabwera nkumadya ndi kumwa ndithu, anthu amvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’ Komabe chilungamo cha nzeru za Mulungu chimatsimikizika ndi zochita zake.”
Za tsoka la midzi yosatembenuka mtima
(Lk. 10.13-15)
20Pambuyo pake Yesu adayamba kudzudzula midzi imene Iye adaaichitira zamphamvu zochuluka. Adaidzudzula chifukwa anthu ake anali osatembenuka mtima. 21#Yes. 23.1-18; Ezek. 26.1—28.26; Yow. 3.4-8; Amo. 1.9, 10; Zek. 9.2-4Adati, “Uli ndi tsoka iwe Korazini! Uli ndi tsoka iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni,#11.21 Tiro ndi ku Sidoni: Ndi mizinda yachikunja kumpoto, kutali ndi Galileya. Anthu a ku mizinda imeneyo analibe mwai wakumva mau a Yesu ndi kuwona ntchito zake monga adaachitira anthu a ku Korazini ndi a ku Betsaida. bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima. 22Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu. 23#Yes. 14.13-15; Gen. 19.24-28 Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa iwe, achikhala zidaachitikira m'Sodomu, bwenzi mzindawo ukadalipo mpaka lero. 24#Mt. 10.15; Lk. 10.12Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga iwe.”
Yesu ndiye wopatsa mpumulo
(Lk. 10.21-22)
25Pa nthaŵi imeneyo Yesu adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. 26Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu.
27 # Yoh. 3.35; Yoh. 1.18; 10.15 “Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.
28 # Mphu. 6.24-30; 24.19; 51.23-26 “Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. 29#Yer. 6.16Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. 30Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Currently Selected:

Mt. 11: BLY-DC

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in