YouVersion Logo
Search Icon

YAKOBO 1

1
1 # Yoh. 7.35; Mac. 12.17; 26.7; 1Pet. 1.1 Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.
Za mayesero
2 # 1Pet. 1.6 Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; 3#Aro. 5.3pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. 4Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.
5 # Miy. 2.3-6; Mat. 7.7 Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye. 6#Mrk. 11.24Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. 7Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; 8munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zake zonse.
9Koma mbale woluluka adzitamandire pa ukulu wake; 10#Mas. 90.5-6pakuti adzapita monga duwa la udzu. 11Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.
12 # 1Ako. 10.13; 2Tim. 4.8; 2Pet. 2.9 Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye. 13Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: 14koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. 15#Mas. 7.14; Aro. 6.23Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa. 16Musanyengedwe, abale anga okondedwa. 17#Mala. 3.6; 1Ako. 4.7Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro. 18#Yoh. 1.13; Chiv. 14.4Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zake.
Tikhale akuchita a mau
19 # Miy. 14.17; Mlal. 5.1 Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima. 20Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. 21#Aef. 1.13; Akol. 3.8Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. 22#Mat. 7.21Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. 23#Luk. 6.49Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; 24pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. 25Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake. 26#Mas. 34.13Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. 27#Mat. 25.36; 1Yoh. 5.18Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.

Currently Selected:

YAKOBO 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in