YouVersion Logo
Search Icon

YAKOBO 2

2
Asachite tsankho pakati pa anthu
1 # Mat. 22.16 Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe. 2Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa; 3ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga; 4kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa? 5#1Ako. 1.26-28Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye? 6#Mac. 13.50Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwowa kumabwalo a milandu? 7Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo? 8#Lev. 19.18; Mat. 22.39Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino: 9#Yak. 2.1koma ngati musamala maonekedwe, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga olakwa. 10#Agal. 3.10Pakuti amene aliyense angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse. 11#Eks. 20.13-14Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo. 12#Yak. 1.25Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu. 13#Mat. 6.15Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachita chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.
Chikhulupiriro chopanda ntchito zake chikhala chopanda pake
14 # Mat. 7.26 Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa? 15#1Yoh. 3.18Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsowa chakudya cha tsiku lake, 16#1Yoh. 3.18ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani? 17Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo. 18#Yak. 3.13Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga. 19#Mat. 8.29Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira. 20Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe? 21#Gen. 22.9, 12Abrahamu kholo lathu, sanayesedwa wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe pa guwa la nsembe? 22#Aheb. 11.17Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro; 23#Gen. 15.6; Yes. 41.8ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. 24Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha. 25#Yos. 2.1-22; Aheb. 11.31Ndipo momwemonso sanayesedwa wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina? 26Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.

Currently Selected:

YAKOBO 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in