YAKOBO Mau Oyamba
Mau Oyamba
Wolemba kalatayi alembera Akhristu achiyuda obalalika kumaiko osiyanasiyana. Apereka malangizo amitundumitundu owathandiza kuwongolera moyo wao wa masiku onse mwa njira yachikhristu. Aziwonetsa makhalidwe abwino pa zochita zao zonse, pakuti “chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo.” (2.17)
Za mkatimu
Mau oyamba 1.1
Za chikhulupiriro ndi nzeru 1.2-8
Za umphawi ndi chuma 1.9-11
Za kuyesedwa ndi zovuta kapena zinyengo 1.12-18
Za kumva ndi kuchita zimene Mulungu anena 1.19-27
Awachenjeza kuti asamachite tsankho 2.1-13
Za chikhulupiriro ndi ntchito zake 2.14-26
Za kuwongolera lilime potsata nzeru zochokera kumwamba 3.1-18
Za kuchita chibwenzi ndi pansi pano 4.1—5.6
Za kuyembekeza mopirira ndi kupempherera odwala 5.7-20
Currently Selected:
YAKOBO Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi