YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 47

47
Babiloni adzaonongeka konse
1Tsika, ukhale m'fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka. 2Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje. 3#Aro. 12.19Maliseche ako adzakhala osafundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzachita kubwezera, osasamalira munthu. 4#Yes. 43.3, 14Mombolo wathu, Yehova wa makamu ndi dzina lake, Woyera wa Israele. 5Khala iwe chete, lowa mumdima, mwana wamkazi wa Ababiloni; pakuti sudzatchedwanso mkazi wa maufumu. 6#2Mbi. 28.9Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsera chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu. 7Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalira izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake.
8 # Zef. 2.15 Chifukwa chake tsono, imva ichi, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana; 9#1Ate. 5.3koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri. 10#Mas. 52.7; Zef. 2.15Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi chidziwitso chako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina. 11#1Ate. 5.3Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi. 12Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana. 13#Dan. 2.2Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera. 14#Mala. 4.1Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha kumphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako. 15#Chiv. 18.11Zinthu zomwe unagwira ntchito yake, zidzatero nawe; iwo amene anachita malonda ndi iwe chiyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwake; sipadzakhala wopulumutsa iwe.

Currently Selected:

YESAYA 47: BLPB2014

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in